Tapatsidwa Chuma Choti Tisamalire
1 Mtumwi Paulo ankaona kuti ntchito yolalikira imene Mulungu anam’patsa n’njofunika kwambiri ndipo anaitcha kuti “chuma.” (2 Akor. 4:7) Pogwira ntchito imeneyo, iye anapirira zovuta ndiponso chizunzo. Mosatopa, anali kulalikira kwa aliyense amene anam’peza. Anayenda maulendo ambiri ovuta ndiponso oopsa, pamtunda ndi panyanja. Kodi tingatsanzire bwanji Paulo ndi kusonyeza kuti timalemekeza utumiki wathu? (Aroma 11:13) N’chiyani chimachititsa utumiki wathu kukhala chuma choposa chuma china chilichonse?
2 Chuma Chamtengo Wapatali Zedi: Chuma chapadziko lapansi, nthawi zambiri chimabweretsa mavuto ochuluka ndipo sichithandiza kwenikweni kapena chimangopindulitsa kwa nthawi yochepa chabe. Koma utumiki wathu, umatipindulitsa kosatha ndiponso umapindulitsa ena. (1 Tim. 4:16) Umathandiza anthu oona mtima kudziwa Yehova, kusintha moyo wawo, ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chenicheni cha moyo wosatha. (Aroma 10:13-15) Tikamaona kuti utumiki wathu n’ngofunika, moyo wathu umakhala ndi cholinga, timakhutira ndi zimene timachita, ndiponso timakhala ndi chiyembekezo chosangalatsa.—1 Akor. 15:58.
3 Sonyezani Kuti Mumayamikira Kwambiri Chuma Chimenechi: Timasonyeza kuti chinthu chinachake n’chofunika mwa zimene talolera kutaya kuti tipeze chinthucho. Ndi mwayi waukulu kwambiri kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu kutamanda Yehova! (Aef. 5:16, 17) Tizigwiritsira ntchito nthawi yathu mosonyeza kuti timaona zinthu zauzimu kukhala zofunika kuposa zinthu zakuthupi. Popeza tili ndi uthenga wofunika kwambiri woti tiuze ena, tidzalalikira mwakhama ndi kukhala atcheru kulalikira uthenga wabwino panthawi iliyonse yomwe tapeza mpata.
4 Nthawi zambiri zinthu za mtengo wapatali zimaikidwa poonekera kuti anthu ena azione ndi kusangalala nazo. Ngati timaona kuti utumiki wathu ndi chuma, udzakhala mbali yofunika kwambiri ya moyo wathu. (Mat. 5:14-16) Moyamikira kwambiri, tiyeni nthawi zonse titsanzire Paulo ndiponso tigwiritsire ntchito mpata uliwonse, kusonyeza kuti timaonadi utumiki wathu kuti ndi wofunika, ndiponso kuti timauona ngati chuma.