Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/95 tsamba 1
  • Mawu A Ufumu—Kupeza Lingaliro Lake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu A Ufumu—Kupeza Lingaliro Lake
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu wa Mulungu—Kodi Mukumvetsa Lingaliro Lake?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Ndandanda ya Banja Yochitira Lemba la Tsiku
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • ‘Pitirizanibe Kufunafuna Choyamba Ufumuwo’
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Lalikirani Uthenga wa Ufumu
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 2/95 tsamba 1

Mawu A Ufumu—Kupeza Lingaliro Lake

1 M’fanizo lake la wofesa, Yesu anati mbewu yogwera pa “nthaka yabwino” inaimira “wakumva mawu [ndi kupeza lingaliro lake, NW].” (Mat. 13:23) Titamva za Ufumu, kodi tapeza “lingaliro lake”? Kodi umayambukira miyoyo yathu kufikira pati? Kodi taika zinthu za Ufumu pamalo oyamba, motero tikumasonyeza kuti tinapeza lingaliro la uthengawo?

2 Kumvetsetsa uthenga wa Ufumu kolondola kumafuna phunziro laumwini. Tifunikira kupatula nthaŵi ya kusinkhasinkha pa chakudya chauzimu choperekedwa. Kuŵerenga Nsanja ya Olonda kothamanga kuli ngati kumeza mofulumira chakudya chokoma ndi chopatsa thanzi. Kodi mumapatula nthaŵi ya kulingalira chakudya chauzimu mosamalitsa? Kuti mupeze phindu lalikulu, payenera kukhala chisonkhezero ndi njala yabwino yauzimu. Ngati palibe zimenezi, zochita zina zingachepetse mapindu a phunziro laumwini kapena kudya nthaŵi imene tikufuna kaamba ka phunzirolo. Kumamatira ku ndandanda ya phunziro yabwino sikokhweka. Ngakhale kuti kumafuna kulinganiza kosamalitsa kwa zinthu zoyamba, chuma chauzimu chimene chingapezedwe nchamtengo wosayerekezereka.—Miy. 3:13-18; Akol. 1:27.

3 Kabuku ka Kusanthula Malemba kamatithandiza tsiku lililonse kusunga malingaliro abwino ndi omangirira onena za Ufumu. Awo amene ali “osauka mumzimu” amalinganiza za kupatula mphindi zingapo tsiku lililonse kuti aŵerenge lemba latsiku ndi ndemanga. (Mat. 5:3) Malemba ambiri amafotokoza mbali zosiyanasiyana za Ufumu. Mwachitsanzo, pa November 22, 1994, lemba limene linasonyezedwa linali la Mateyu 13:4. Ndemanga yake inafotokoza za chiyembekezo cha Ufumu ndi kutikumbutsa za ngozi za mayanjano oipa ndi achibale ndi anansi. Chenicheni chakuti panyumba za Beteli kuzungulira dziko lonse, pamakhala kukambitsirana kwa lemba latsiku kwa mphindi 15 mmaŵa wa tsiku lililonse lantchito chimagogomezera za mapindu ndi kufunika kwakukulu kwa kulingalira lemba latsiku pamodzi. Kodi banja lanu limaphatikizapo kukambitsirana kofananako m’njira yanu yochitira zinthu yatsiku ndi tsiku?

4 Pamene mukulitsa chiyamikiro cha Ufumu, padzakhala chisonkhezero chokulirapo cha kuuza ena uthenga wa Ufumu. Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amapereka chimene chingayerekezeredwe monga mafuta osonkhezera maganizo amene amadyetsa malingaliro athu chidziŵitso chapanthaŵi yake. Amatithandiza kukhalabe amaso ponena za mmene dzikoli limafunira Ufumu wa Mulungu. Amatithandiza kukhala anthu amkhalidwe wauzimu, a “mtima wa Kristu.” (1 Akor. 2:15, 16) Zonsezi zingalimbitse chiyembekezo chathu ndi kuwonjezera changu chathu cha kuuza ena za chiyembekezo cha Ufumu.—1 Pet. 3:15.

5 Nkofunika kwambiri kuti ife enife tipeze lingaliro la uthenga wa Ufumu. Ufumuwo ndiwo njira imene Mulungu adzagwiritsira ntchito kuchirikizira uchifumu wake, kuthetsa kuipa, ndi kubweretsera dziko latsopano—paradaiso. Yesu anatilamulira kuuika poyamba m’miyoyo yathu. Tiyenera kukhala nzika zonga nkhosa kuti tidzakhale ndi moyo pansi pa ulamuliro wake. (Mat. 6:10, 33) Gwiritsirani ntchito mpata wanu mokwanira kuti mulandire madalitso ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena