Ndandanda ya Banja Yochitira Lemba la Tsiku
1 Makolo achikondi amayesetsa kukonzera ana awo chakudya chabwino tsiku lililonse. Kuwapatsa chakudya chabwino chauzimu chochokera m’Mawu a Mulungu n’kofunika koposa. (Mat. 4:4) Njira imodzi imene mungathandizire ana anu kukhala ndi chilakolako cha chakudya chauzimu ndiponso ‘kukula kufikira chipulumutso’ ndiyo mwa kupeza nthawi yowerenga lemba la tsiku ndi ndemanga monga banja tsiku lililonse. (1 Pet. 2:2) Kodi mungaike nthawi iti pa ndandanda yanu ya banja yochitira zimenezi?
2 Nthawi za Chakudya: Kuyamba ndi lemba la tsiku m’mawa kungathandize banja lanu kulingalira za Yehova tsiku lonse. (Sal. 16:8) Mayi wina anakonza zomawerenga ndi kukambirana lemba la tsiku ndi mwana wake wamwamuna pa nthawi imene mwanayo akudya chakudya cha m’mawa ndi kupemphera ali limodzi asanapite ku sukulu. Zimenezi zinathandiza mwana wakeyo kuti azikhala wolimba akamakumana ndi chiyeso choti aonetse kuti amakonda dziko lake. Chinamuthandizanso kukana zachiwerewere, ndi kulalikira molimba mtima kwa ana a sukulu anzake ndi aphunzitsi. Ngakhale kuti Wamboni anali yekhayo pasukulupo, iye sanaone ngati anali yekha.
3 Ngati kukambirana lemba la tsiku m’mawa n’kosatheka, mukhoza kumakambirana pa nthawi ina monga banja, mwina panthawi ya chakudya cha madzulo. Nthawi imeneyi ndi imenenso ena amakambirana zokumana nazo za mu utumiki wa kumunda ndiponso mfundo zimene zawasangalatsa pamene anali kuwerenga Baibulo paokha. Ambiri akamakumbukira kale lawo, amaona kuti nthawi imene anali kukhalira limodzi pa chakudya madzulo monga banja ndi imodzi mwa nthawi zosangalatsa kwambiri zimene anali nazo.
4 Nthawi ya Usiku: Mabanja ena, amaona nthawi ya usiku asanapite kokagona kukhala yabwino kuchita lemba la tsiku. Imeneyi ingakhalenso nthawi yabwino yopemphera limodzi. Ana anu akamakumvani mukulankhula za Yehova ndi kupemphera kwa iye tsiku ndi tsiku, amayamba kuona kuti Yehova ndi weniweni.
5 Yehova akudalitseni pa khama lanu lokhomereza choonadi mwa ana anu pogwiritsa ntchito bwino kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku.