Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kuwagawira buku la Lambirani Mulungu. Cholinga chathu chikhale choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba, makamaka ndi anthu amene anaphunzira kale buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. June: Gawirani buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, ndipo ngati anthuwo anena kuti alibe ana, gawirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Gawirani lililonse la mabulosha awa: Buku la Anthu Onse, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo pa June 1, kapena patangodutsa masiku ochepa kuchoka pa detili. Akatha kuwerengerako, mukalengeze kumpingo mukamawerenga lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ DVD Yatsopano Yomwe Ilipo:
They Bore Thorough Witness to the Good News (dvbo-ASL)—Ili M’chinenero Chamanja cha ku America chokha basi