Konzani Ndandanda ya Banja Yotheka Kuitsatira
1 Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu analimbikitsa omvera ake kuti: ‘Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ (Mat. 6:33) Njira yabwino yokonzera zochita za banja kuti muike zinthu zauzimu patsogolo ndiyo kukhala ndi ndandanda yochita kulemba. Pezani nthawi yoti mukonze ndandanda ya banja lanu ya mlungu ndi mlungu pogwiritsa ntchito ndandanda yosamaliza yomwe ili patsamba 6 m’mphatika ino. Mabanja ena angakonde kungodula zimene talembazo n’kuzimata pa ndandandayo. Ena angasankhe kuchita kulemba okha zofunika kuchitazo.
2 Chitsanzo cha ndandanda ili m’munsiyi chingakuthandizeni pamene mukukonza ndandanda yanu ya banja. Muona kuti ili ndi zochita zinayi zofunika: (1) Kupezeka pa misonkhano ya mpingo, (2) utumiki wa kumunda wa banja, (3) phunziro la banja, ndipo (4) kukambirana lemba la tsiku. Kuphatikiza zinthu zimenezi pa ndandanda yanu kungakuthandizeni kuti “mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:10, NW) Mfundo zina zokhudza mbali zinayi zimenezi zili patsamba 4 ndi 5.
3 Sikuti ndandanda ya banja lanu ingokhala ndi zochita zinayi zokhazi ayi. Ngati mumakonzekera misonkhano ina monga banja, lembani zimenezo pa ndandanda yanuyo. Ngati mumawerenga kachigawo ka Baibulo nonse pamodzi mukatha kukambirana lemba la tsiku kapena mumachita zimenezi panthawi ina, zilembeni pa ndandanda yanu. Ngati muli ndi chizolowezi chosewera monga banja, zimenezi mungaziphatikize pa ndandanda yanu.
4 Ndandanda yanu ya banja ikhale yogwirizana ndi zosowa za aliyense m’banja ndi zochita zake. Pakapita nthawi, muziona kuti ikuyenda bwanji, ndipo muziisintha ngati pali kufunikira kotero.
[Tchati patsamba 3]
Chitsanzo cha Ndandanda ya Banja
M’mawa Masana Madzulo
Laml. Lemba la Tsiku
Nkhani ya Onse ndi
Phunziro la Nsanja ya Olonda
Lole. Lemba la Tsiku Phunziro la Banja
Lachiw. Lemba la Tsiku Phunziro la Buku
la Mpingo
Lachit. Lemba la Tsiku
Lachin. Lemba la Tsiku Sukulu ya Utumiki
wa Mulungu ndi
Msonkhano wa
Utumiki
Lachis. Lemba la Tsiku
Low. Lemba la Tsiku
Utumiki wa Kumunda
wa Banja
(Tsiku la Magazini)
[Tchati patsamba 6]
Ndandanda ya Banja
M’mawa Masana Madzulo
Laml.
Lole.
Lachiw.
Lachit.
Lachin.
Lachis.
Low.
..................................................................
Lemba la Lemba la Lemba la Lemba la Lemba la Lemba la Lemba la
Tsiku Tsiku Tsiku Tsiku Tsiku Tsiku Tsiku
Nkhani Sukulu Phunziro Phunziro Utumiki Kuwerenga Kusewera
ya Onse ya la Buku la Banja wa Kumunda Baibulo Monga
ndi Utumiki wa la Monga Banja Monga Banja Banja
Phunziro Mulungu ndi Mpingo
la Nsanja Msonkhano
ya Olonda wa
Utumiki
Mwina mungakonde kupanga fotokope tsamba lino la Utumiki Wathu wa Ufumu n’kuduladula bwinobwino mmene muli mizera ya madonthomadonthomo. Mukatero mukhoza kumata timapepala mwadulato pa ndandanda yosalembapo chilichonse imene ili panoyi mogwirizana ndi zochita za banja lanu za mlungu ndi mlungu. Malo osalembawo m’mizera ya madonthomadontho, mukhoza kuwagwiritsa ntchito kulembamo zochita zina zimene mungafune kuziphatikiza pandandanda yanu ya mlungu ndi mlungu.