Musafulumire Kuganiza Kuti Simungakwanitse—Zimene Mungachite Ngati Muli Wotanganidwa
1. N’chifukwa chiyani anthu ena amalephera kupempha mwininyumba kuti aziphunzira naye Baibulo?
1 Anthu ena amalephera kupempha mwininyumba kuti aziphunzira naye Baibulo chifukwa chodziona kuti ndi otanganidwa. N’zoona kuti kuthandiza wophunzira Baibulo kumafuna nthawi. Pamafunika nthawi yokonzekera ndi kuchititsa phunziro komanso kuthandiza wophunzirayo kuthana ndi mavuto ake. Mtumwi Paulo ananena kuti anapereka moyo wake kuti athandize anthu a ku Tesalonika kudziwa Yehova. (1 Ates. 2:7, 8) Ndiyeno kodi ifeyo tingatani kuti tizipeza nthawi yochititsa phunziro la Baibulo ngakhale titakhala otanganidwa kwambiri?
2. Kodi kukonda Yehova kumakhudza bwanji mmene timagwiritsira ntchito nthawi yathu?
2 Kutumikira Yehova Kumafuna Nthawi: Kunena zoona, kulambira kumafuna nthawi. Mwachitsanzo, timapatula nthawi yoti tipite kumisonkhano, tikalalikire, tiwerenge Baibulo komanso yoti tipemphere. Komatu ngakhale munthu wapabanja amayesetsa kupatula nthawi yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wake kaya akhale wotanganidwa bwanji. Chotero ifenso tizikhala okonzeka ‘kugwiritsa ntchito nthawi yathu’ kulambira Yehova chifukwa chomukonda. (Aef. 5:15-17; 1 Yoh. 5:3) Yesu ananena kuti kugwira ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira ake ndi mbali yofunika pa kulambira kwathu. (Mat. 28:19, 20) Kuganizira zimenezi kungatithandize kukwaniritsa udindo wathu wochititsa phunziro la Baibulo.
3. Kodi tingatani kuti phunziro la Baibulo lisamasokonezeke ngati patakhala zifukwa zimene zingatilepheretse kulowa mu utumiki?
3 Kodi tingatani ngati timasowa nthawi yochititsa phunziro la Baibulo chifukwa chotanganidwa ndi ntchito, kudwaladwala kapena kutanganidwa ndi mautumiki ena achikhristu? Ofalitsa ena amene amayendayenda amachititsa maphunziro awo a Baibulo pogwiritsira ntchito telefoni kapena kompyuta. Ofalitsa amene amadwaladwala amakonza zoti munthu amene amaphunzira naye Baibulo azibwera kunyumba kwawo kudzachita phunziro. Ndipo ofalitsa ena amagwirizana ndi wofalitsa wina kuti azichititsa phunziro lawo la Baibulo iwowo akachoka.
4. Kodi kugwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo kumabweretsa madalitso otani?
4 Paulo anapeza chimwemwe chochuluka chifukwa chogwiritsira ntchito nthawi ndi mphamvu zake kuthandiza anthu ena kuti aphunzire choonadi. (Mac. 20:35) Iye ankathokoza Yehova akaganizira mmene khama lake linathandizira anthu a ku Tesalonika kuphunzira choonadi. (1 Ates. 1:2) Tisalole kuti kutanganidwa kutilepheretse kugwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Tikatero tidzakhala achimwemwe komanso okhutira kwambiri ndi utumiki.