Ndandanda ya Mlungu wa November 26
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 26
Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 15, bokosi patsamba 121 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mika 1-7 (Mph. 10)
Na. 1: Mika 3:1-12 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi N’chiyani Chikusonyeza Kuti Paradaiso Wotchulidwa pa Luka 23:43 Adzakhala Padziko Lapansi Pompano?—rs tsa 338 ndime 2–tsa. 339 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Timadziwa Bwanji Kuti Yehova Ndi Wakumva Pemphero?—1 Yoh. 5:14 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo, Loweruka loyambirira m’mwezi wa December. Limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph 10: Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa. Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2012, tsamba 8 ndi 9.
Mph 15: “Musafulumire Kuganiza Kuti Simungakwanitse—Zimene Mungachite Ngati Muli Wotanganidwa.” Mafunso ndi mayankho. Mwachidule funsani wofalitsa amene amagwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo ngakhale kuti iyeyo ndi wotanganidwa.
Nyimbo Na. 73 ndi Pemphero