Ndandanda ya Mlungu wa December 3
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 3
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 15 ndime 13-20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Nahumu 1 mpaka Habakuku 3 (Mph. 10)
Na. 1: Habakuku 2:1-14 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulalikira za Choonadi Mopanda Mantha?—2 Tim. 1:7, 8 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingakhale Bwanji Odziwa Zinthu Ndiponso Anzeru?—rs tsa. 136 ndime 1–3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu December. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph 10: Zosowa za pampingo.
Mph 10: Zimene Zinachitika Pogawira Timapepala. Nkhani yokambirana ndipo ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Pemphani omvera kuti anene zinthu zosangalatsa zimene zinachitika pamene ankagawira timapepala m’mwezi wa November. Pemphani ofalitsa awiri amene zinthu zinawayendera bwino pogawira timapepala kunyumba ndi nyumba kuti achite chitsanzo cha zimene zinachitika.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero