Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w24 November tsamba 31
  • Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muziphunzira Mlungu Uliwonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muziphunzira Mlungu Uliwonse
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizisangalala Ndikamawerenga Baibulo?
    Galamukani!—2012
  • Ndandanda ya Banja Yochitira Phunziro la Banja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Phunziro Limapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Musafulumire Kuganiza Kuti Simungakwanitse—Zimene Mungachite Ngati Muli Wotanganidwa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24 November tsamba 31
Mlongo akugwiritsa ntchito kompyuta, Baibulo ndi kope pophunzira Baibulo payekha. Iye akugwiritsanso ntchito tchati cha “Maulamuliro Amphamvu Padziko Lonse Amene Danieli Analosera” pa Zakumapeto B9 mu Baibulo la Dziko Latsopano.”

Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muziphunzira Mlungu Uliwonse

KODI zimakuvutani kuti muziphunzira Baibulo panokha mlungu uliwonse komanso kuti muzisangalala pophunzirapo? Tonsefe zimenezi nthawi zina zimatichitikira. Koma taganizirani zinthu zina zomwe timachita nthawi zonse, monga kusamba. Kuti munthu asambe pamafunika nthawi komanso khama koma akasamba amamva bwino. Kuphunzira Baibulo tingakuyerekezere ndi ‘kusamba m’madzi a Mawu a Mulungu.’ (Aef. 5:26) Tiyeni tione mfundo zina zomwe zingatithandize pa nkhaniyi.

  • Muzipanga ndandanda. Kuphunzira Baibulo ndi chimodzi mwa ‘zinthu zofunika kwambiri’ zimene Mkhristu sayenera kunyalanyaza. (Afil. 1:10) Kuti muzitsatira ndandanda yanu, muziika pamalo amene mungamaone mosavuta monga pakhoma kapena pafiriji. Kapenanso mungatchere alamu pachipangizo chanu chamakono kuti izilira nthawi yophunzira ikatsala pang’ono.

  • Muzisankha nthawi komanso njira yophunzirira yomwe ingakhale yabwino kwa inuyo. Kodi mungakonde kuphunzira kamodzi pa mlungu kwa nthawi yaitali kapena maulendo angapo moduladula? Mukhoza kukonza zoti muziphunzira mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Ngati mumaona kuti mumagwa ulesi nthawi yophunzira ikafika, mungayese kumangophunzira kwa 10 minitsi yokha. Kuphunzira kwa nthawi yochepa chonchi kungakuthandizeni kwambiri kusiyana ndi kungokhala osaphunzira. Ndipo mwina mukayamba kuphunzira mudzalimbikitsidwa kuti mupitirize.​—Afil. 2:13.

  • Muzisankhiratu nkhani zoti muphunzire. Mukakhala pansi n’kumaganizira zoti muphunzire nthawi yomweyo, simungagwiritse ntchito bwino nthawi yanu. (Aef. 5:16) Mungachite bwino kusankhiratu nkhani zimene mukufuna kuphunzira n’kuzilemba penapake. Funso linalake likabwera m’maganizo mwanu muzililemba. Mukamaliza kuphunzira ulendo uliwonse muziwonjezera zinthu zimene mukufuna kudzaphunzira.

  • Muzikhala okonzeka kusintha. Muziyesa kusintha zinthu zina pandandanda yanu monga kuchuluka kwa nthawi kapena nkhani zimene mungaphunzire. Chofunika si tsiku, kuchuluka kwa nthawi kapena nkhani zimene mungaphunzire koma kuti muziphunzira mlungu uliwonse.

Timapindula kwambiri tikamaphunzira mlungu uliwonse. Ubwenzi wathu ndi Yehova umalimba, timachita zinthu mwanzeru komanso timalimbikitsidwa.​—Yos. 1:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena