Mangani Moyo Wanu pa Utumiki wa Yehova
1 Yesu anayerekezera omvetsera ake ndi anthu aŵiri omanga nyumba. Wina anamanga njira yake ya moyo pathanthwe lomvera Kristu ndipo anali wokhoza kulimbana ndi mphepo ya chitsutso ndi zosautsa zina. Winayo anamanga pamchenga wa kusamvera kodzikonda ndipo sanathe kupirira pamene mavuto anabwera. (Mat. 7:24-27) Pokhala tili ndi moyo m’masiku otsiriza ano a dongosolo la zinthuli, timakumana ndi mphepo zochuluka za mavuto. Mitambo yakuda ya chisautso chachikulu nayonso ikusonkhana mofulumira m’chizimezime. Kodi tidzapirira mpaka mapeto tili ndi chikhulupiriro chosasweka? (Mat. 24:3, 13, 21) Zimenezi zimadalira kwambiri pa mmene tikumangira miyoyo yathu tsopano lino. Choncho, kuli kofunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikumanga zolimba moyo wanga wachikristu pa utumiki wokhulupirika kwa Mulungu?’
2 Kodi kumanga moyo wathu pa utumiki wa Yehova kumatanthauzanji? Zimatanthauza kuti miyoyo yathu iyenera kumadalira pa Yehova. Zimaphatikizapo kusumika maganizo athu pa Ufumu monga chinthu chimene chili chachikulu koposa kwa ife. Zimaphatikizaponso kumvera Mulungu mu zochita zathu zonse za tsiku ndi tsiku. Zimafuna kuika mtima wathu pa kuphunzira Baibulo kwaumwini, kwa pabanja, ndi kwa pampingo ndi pa utumiki wathu wakumunda, tikumapanga zimenezi kukhala zinthu zoyamba m’moyo wathu. (Mlal. 12:13; Mat. 6:33) Moyo womvera woterowo umabweretsa chikhulupiriro cholimba ngati thanthwe chimene sichidzasweka pokumana ndi mphepo za mavuto amene angatigwere.
3 Ndi zokondweretsa kuona mamiliyoni a anthu akumanga mwachidaliro miyoyo yawo ndi ziyembekezo zawo za m’tsogolo pa kutumikira Mulungu, monga momwe Yesu anachitira. (Yoh. 4:34) Amatsatira ndandanda yosasintha ya zochita zateokalase ndipo amapeza madalitso ochuluka. Mayi wina analongosola mmene iye ndi mwamuna wake analili wokhoza kulera bwinobwino ana awo aŵiri kuti atumikire Yehova: “Tinadzaza moyo wathu ndi choonadi—kupita kumisonkhano yonse yachigawo, kukonzekera ndi kupezeka pamisonkhano yampingo, ndi kupanga utumiki wakumunda kukhala mbali ya zochita zathu za nthaŵi zonse.” Mwamuna wake anawonjezera kuti: “Choonadi sichili mbali ya moyo wathu, chili moyo wathu. Kanthu kena kalikonse kamasumikidwa pa icho.” Kodi inunso mwaika utumiki wa Yehova monga chinthu choyamba m’banja lanu?
4 Pangani Ndandanda ya Mlungu ndi Mlungu Yotsatirika: Gulu la Yehova limatithandiza kukhala ndi chizoloŵezi chabwino chauzimu mwa kulinganiza misonkhano isanu mlungu uliwonse. Akristu amene akumanga miyoyo yawo pa kulambira Yehova amalinganiza zochita zawo za kuntchito ndi za pabanja kotero kuti akhale okhoza kumafika pamisonkhano yofunika yonseyi. Salola kuti zinthu zosafunika kwambiri ziziwalepheretsa kufika pamisonkhano nthaŵi zonse.—Afil. 1:10, NW; Aheb. 10:25.
5 Akristu ofikapo amazindikira kuti monga momwe kudya chakudya mokhazikika panthaŵi inayake tsiku lililonse kulili kofunika, kulinso kofunika kupanga ndandanda yotsimikizika ya phunziro laumwini ndi labanja, kuphatikizapo kukonzekera misonkhano. (Mat. 4:4) Kodi mungamapatule nthaŵi ya mphindi 15 kapena 20 tsiku lililonse kuti muchite phunziro laumwini? Kusalola zinthu zina kuloŵerera panthaŵi yoikidwa kaamba ka phunziro ndiko chiyambi cha kuchita bwino. Chipangeni kukhala chizoloŵezi chopindulitsa. Zimenezi zingafune kuti muzidzuka m’maŵa kwambiri kusiyana ndi mmene mumadzukira tsopanoli. Anthu 17,000 a banja la padziko lonse la Beteli amadzuka m’mamaŵa kuti akambirane lemba latsiku. Zoona, kuti mudzuke m’mamaŵa pamafunika kugona nthaŵi yabwino kuti mukadzuke ndi mphamvu komanso mutapumula bwino.
6 Ngati ndinu mutu wabanja, tsogolerani kulinganiza ndi kukonza ndandanda ya zochita zateokalase ya banja lanu. Mabanja ena amaŵerengera pamodzi Baibulo, Yearbook, kapena buku lina pamene akupuma atatha kudya madzulo. Makolo ambiri amene ana awo akula ndi kukhala Akristu olimba mwauzimu amati chinthu china chimene chinawathandiza kwambiri chinali khalidwe la banjalo la kupatula nthaŵi inayake madzulo a tsiku lina mlungu uliwonse pamene amasangalala ndi zinthu zauzimu onse pamodzi. Tate wina mwa makolo oterowo anati: “Ndikuona kuti kukula mwauzimu kwa ana athu kunali kwenikweni chifukwa chakuti Lachitatu lililonse madzulo timakhala ndi phunziro labanja, limene tinaliyamba zaka 30 zapitazo.” Ana ake atatu onse anabatizidwa ali ang’onoang’ono, ndipo onse ali mu utumiki wanthaŵi zonse. Kuwonjezera pa phunziro labanja, mungayeserere maulaliki a utumiki wakumunda kapena nkhani za misonkhano ndipo mungachitire pamodzi zochitika zina zabwino.
7 Pandandanda yanu ya mlungu ndi mlungu, kodi ‘mwaombola’ nthaŵi ya kulalikira Ufumu? (Akol. 4:5, NW) Ambiri a ife ndife otanganidwa, tili ndi maudindo a banja ndi a kumpingo oti tisamalire. Ngati sitipanga makonzedwe otsimikizirika oti tizigwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa mlungu uliwonse, kudzakhala kosavuta kuti zinthu zina zitsekereze ntchito yofunika imeneyi. Mwiniwake wa famu ina yaikulu ya ng’ombe anati: “Cha mu 1944 ndinaona kuti njira yokha imene ndingamapitire mu utumiki inali kupatula tsiku loti ndizikhala mu utumikiwo. Kufikira lerolino ndimakhalabe ndi tsiku lina pamlungu limene ndimakhala ndili mu utumiki.” Mkulu wina wachikristu wapeza kuti kukhala ndi ndandanda yotsimikizika yolalikira kumamtheketsa kukhala ndi avareji ya maola 15 pa mwezi m’ntchito yolalikira. Ngati ali ndi ntchito zina pa Loŵeruka, amazigwira pambuyo pa kupita mu utumiki wakumunda m’maŵa. Kodi inuyo ndi banja lanu mungakonze kuti mwina tsiku limodzi lokha pa mlungu muzikhala mu utumiki wakumunda, ndi kuipanga kukhala mbali ya njira ya moyo wanu wauzimu?—Afil. 3:16.
8 Pendani Kachitidwe Kanu ka Zinthu: Pali zinthu zimene sizigwirizana ndi kumanga miyoyo yathu pa utumiki wa Yehova. Zochitika zosayembekezeredwa zingasokoneze ndandanda yathu yokonzedwa bwino ya kuphunzira, kufika pamisonkhano, ndi utumiki. Ndipo Mdani wathu Satana, adzachita zilizonse zimene angathe kuti ‘atseke njira yathu’ ndi kulepheretsa zolinga zathu. (1 Ates. 2:18, NW; Aef. 6:12, 13) Musafooketsedwe ndi zopinga zimenezi ndi kungosiya. Pangani masinthidwe alionse amene ali ofunika kuti muchitebe ntchito yateokalase imene munalinganiza kuchita. Kutsimikiza mtima ndi kulimbikira ndi zofunika kuti mukwaniritse chinthu chimene chilidi chaphindu.
9 Sitiyenera kulola zisonkhezero zadziko ndi chitsenderezo cha thupi lathu lopanda ungwiro kutipangitsa kuyamba kuchita zinthu zimene sizili zauzimu ndi zimene zingayambe kutidyera nthaŵi ndi kutipangitsa kusumika malingaliro athu pa izo. Kudzipenda nkofunika, tikumagwiritsa ntchito mafunso ngati awa: ‘Kodi zochita zanga zikukhala zopanda uchikatikati kapena titi ndikucheukitsidwa? Kodi ndayamba kumanga moyo wanga pa zinthu za m’dzikoli zimene zikupita? (1 Yoh. 2:15-17) Kodi ndimathera nthaŵi yochuluka motani pa kufunafuna zinthu zaumwini, maulendo okasangalala, maseŵero, kapena zosangulutsa zina poiyerekezera ndi nthaŵi imene ndimathera pazinthu zauzimu?’
10 Ngati mukuona kuti moyo wanu wadzazidwa ndi zinthu zosafunika zochuluka, kodi muyenera kuchitanji? Monga mmene Paulo anapempherera kuti abale ake ‘akakonzedwe’ kapena ‘kubweretsedwa mumzere woyenera,’ bwanji osampempha Yehova kuti akuthandizeni kusumikanso maganizo anu pa utumiki wake? (2 Akor. 13:9, 11, NW, mawu a mtsinde.) Ndiyeno khalani ofunitsitsa kukwaniritsa chosankha chanu ndipo pangani masinthidwe ofunikawo. (1 Akor. 9:26, 27) Yehova adzakuthandizani kupewa kutembenukira kumanja kapena kumanzere kwa utumiki wokhulupirika kwa iye.—Yerekezerani ndi Yesaya 30:20, 21.
11 Khalani Otanganidwa mu Utumiki Wachimwemwe wa Mulungu: Anthu ambiri omwe amachita khama kufunafuna chimwemwe amangopeza kuti pamene moyo ukupita kumapeto, zinthu zakuthupi zimene anali kulondola mozifunitsitsa sizinawabweretsere chimwemwe chokhalitsa. Kunali “kungosautsa mtima.” (Mlal. 2:11) Mosiyana ndi zimenezo, pamene tisumika miyoyo yathu pa Yehova, ‘kumuika patsogolo pathu nthaŵi zonse,’ timakhala okhutira kwambiri. (Sal. 16:8, 11) Zili choncho chifukwa tili ndi moyo chifukwa cha Yehova. (Chiv. 4:11) Popanda iye, Wachifuno Wamkuluyo, moyo ulibe tanthauzo. Kutumikira Yehova kumadzaza miyoyo yathu ndi ntchito yamtengo wake, ntchito yachifuno imene imatipindulitsa ifeyo ndiponso anthu ena kwanthaŵi yaitali, inde, kwamuyaya.
12 Ndi kofunika kusakhala wotayirira ndi kusaona kufulumira kwanthaŵi ya kutha kwa dziko la Satanali. Moyo wathu wa tsiku ndi tsiku umasonkhezeredwa ndi kaonedwe kathu ka m’tsogolo. Anthu a m’tsiku la Nowa, amene sanakhulupirire kuti kudzakhala chigumula cha dziko lonse, “sanadziŵa kanthu,” anali kusumika miyoyo yawo ya tsiku ndi tsiku pa zokhumba zawo—kudya, kumwa, ndi kukwatira—mpaka chigumula “chinapululutsa iwo onse.” (Mat. 24:37-39) Lerolino, awo amene amasumika miyoyo yawo padzikoli adzaona ziyembekezo zawo zam’tsogolo zikunyotsoka pamaso pawo pachiwonongeko chachikulu kwambiri chimene anthu sanachionepo, “tsiku la Mulungu.”—2 Pet. 3:10-12.
13 Motero pitirizani kumanga moyo wanu pa Mulungu wamoyo, Yehova, ndi pa kuchita chifuno chake. Palibe chinthu chaphindu chilichonse chimene mungapange m’moyo uno chimene chili ndi Wochirikiza wodalirika monga Yehova. Iye sanganame—adzakwaniritsa malonjezo ake. (Tito 1:2) Iye sangafe—chilichonse chosungitsidwa kwa Yehova sichisoŵa. (Hab. 1:12; 2 Tim. 1:12) Moyo womvera ndi chikhulupiriro chimene tikuumba tsopano ndi chiyambi chabe cha moyo umene udzakhala kwamuyaya mu utumiki wosangalatsa wa Mulungu wathu wachimwemwe!—1 Tim. 1:11, NW; 6:19.
[Mawu Otsindika patsamba 3]
“Choonadi sichili mbali ya moyo wathu, chili moyo wathu. Kanthu kena kalikonse kamasumikidwa pa icho.”