Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 7 kufikira December 21, 1998. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. “Mphatso” yotchulidwa pa 2 Timoteo 1:6, ndi luso lolankhula m’zinenero zosiyanasiyana limene Timoteo anapatsidwa mwa kugwira ntchito kwa mzimu woyera wa Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85-CN 9/15 tsa. 16 ndime 15.]
2. Mkristu wofikapo ‘amazoloŵeretsa nzeru zake kuti asiyanitse pakati pa zabwino ndi zoipa’ mwa kukhala ndi chizoloŵezi chogwiritsira ntchito chidziŵitso chilichonse cha Mawu a Mulungu chimene ali nacho. (Aheb. 5:14, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w85-CN 12/1 tsa. 9 ndime 7.]
3. Popeza kuti Yehova “amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama” zimasonyeza kuti m’zochita zake zonse ndi banja la anthu, Yehova wakhala akuonetsa kuti alibe tsankho. (Mat. 5:45) [w96-CN 11/15 tsa. 25, ndime 7]
4. Lamulo la pa 2 Yohane 10 la kusalandira anthu ena kunyumba kapena kuwapatsa moni limanena kokha za anthu amene amachirikiza chiphunzitso chonyenga. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w86-CN 1/1 tsa. 30, ndime 1-3.]
5. Popeza kuti Baibulo limalola kumwa moŵa, kuli chabe koyenera kuti miyambo ndi chikhalidwe chakumaloko nzimene zizilamulira kuti munthu angamwe kufika pati. (Sal. 104:15) [w96-CN 12/15 tsa. 27, ndime 5].
6. Mawu akuti “wokana Kristu akudza” pa 1 Yohane 2:18 amanena za munthu mmodzi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani rs-CN tsa. 414, ndime 2.]
7. Mawu akuti “maubatizo osiyanasiyana” amatanthauza maubatizo a mwambo a zikho ndi miphika ochitidwa ndi Ayuda. (Aheb. 9:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 2/15 tsa. 24.]
8. Pamene mphepo zinayi za chisautso zidzamasulidwa, mwachionekere Israyeli yense wauzimu adzakhala atatha kusindikizidwa chizindikiro. Ngakhale kuti ena angadzakhalebe adakali ndi moyo m’thupi, mamembala onse adzakhala atakwanira. (Chiv. 7:3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani re tsa. 116, ndime 9.]
9. Chivumbulutso 13:11-15 amasonyeza molondola mmene Ulamuliro wa Dziko Lonse wa Anglo-American unakhalira chochirikiza chachikulu ndiponso choyambitsa cha bungwe la League of Nations ndi bungwe lomwe linaloŵa m’malo mwake la United Nations. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 12/15 tsa. 19, ndime 3.]
10. Chitsanzo cha Balamu ndi chenjezo kwa onse amene ali ouma khosi ndi amene amapitiriza kukana chifuniro cha Mulungu pamene akufunafuna kupeza phindu mwadyera. (Yuda 11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani it-1 tsa. 244, ndime 4.]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi zimatanthauzanji kuti woyang’anira sayenera kukhala ‘wandewu’? (Tito 1:7) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 9/1 tsa. 27, ndime 21.]
12. Perekani zifukwa ziŵiri zimene Yehova amachititsira kupatsa kukhala mbali ya kulambira koona. [w96-CN 11/1 tsa. 29, ndime 3-6; tsa. 30, ndime 3]
13. Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati, “Nsembe ndi chopereka simunazifuna”? (Aheb. 10:5) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 7/1 tsa. 14, ndime 3.]
14. Pa Chivumbulutso 13:1, 2, nchifukwa ninji kuli koyenerera kuti maboma adziko akutchedwa “chirombo”? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 4/1 tsa. 20, ndime 17.]
15. Kodi mawu a Petro akuti ‘kumakumbukira tsiku la Yehova’ amatanthauzanji? (2 Pet. 3:12 NW) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 9/1 tsa. 19, ndime 2.]
16. Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa pa chiyero cha mzimu, ndipo kodi zimenezi zimathandiza motani kutetezera banja la munthu? (2 Akor. 7:1) [fy-CN tsa. 46, ndime 14]
17. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 1:7, kodi awo amene anapyoza Yesu adzamuona motani ‘akudza ndi mitambo’? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 5/1 tsa. 22, ndime 7.]
18. Ndi mawu ati pa 1 Yohane 2:2 amene amatithandiza kuzindikira magulu aŵiri amene akupindula ndi imfa yansembe ya Yesu? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 1/15 tsa. 12, ndime 11.]
19. Ngakhale kuti Yesu Kristu anatha zaka zitatu ndi theka akulalikira pakati pa Aisrayeli, nchifukwa chiyani ochuluka anamkana kuti sanali Mesiya? [w96-CN 11/15 tsa. 29, ndime 1, 6; tsa. 30, ndime 3]
20. Kodi ndani amene akuimiridwa ndi “akulu makumi aŵiri mphambu anayi” pa Chivumbulutso 4:4, ndipo kodi “mipando yachifumu” ndi “akolona” awo amatikumbutsa chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 7/1 tsa. 13, ndime 17.]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Mwamuna ndi mkazi ayenera kukhala ․․․․․․․․ kwa wina ndi mnzake, akumakumbukira kuti ․․․․․․․․ ali wofunika kwambiri kuposa maonekedwe akunja. [fy tsa. 26 bokosi lobwereza]
22. Kuti tithamange makani adatiikira, tifunika kutaya cholemetsa chilichonse ndi ․․․․․․․․ limene limangotizinga, limene lili ․․․․․․․․. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 1/1 tsa. 10, ndime 15.]
23. Kuti akhaledi wokongola, mkazi wachikristu sayenera kungovala bwino komanso ayenera kukhala ndi ․․․․․․․․. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 3/15 tsa. 30.]
24. Pamene mwamuna ndi mkazi alankhulana, ․․․․․․․․ ndi ․․․․․․․․ ndi zofunika kwambiri. [fy-CN tsa. 36, ndime 21]
25. Pa Chivumbulutso 6:1-8, wokwera pakavalo wofiira amaimira ․․․․․․․․; wokwera kavalo wakuda amaimira ․․․․․․․․; imfa ili pa kavalo wotumbuluka, kuimira ․․․․․․․․; chifukwa cha miliri ndi zochititsa zina. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani bokosi patsamba 3 mu w86-CN 7/1.]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Pa Ahebri 11:10, “mudzi wokhala nawo maziko” ndiwo (Yerusalemu womangidwanso; mudzi wotchulidwa pa Ezekieli 48:35; Ufumu wa Umesiya). [si tsa. 247, ndime 26]
27. Mawu akuti (chikondi; ulemu; kuchereza alendo) amasuliridwa kukhala “kuŵerengera ena, kuwalemekeza.” [fy-CN tsa. 30, ndime 7]
28. Pa Luka 14:28, Yesu anali kunena za ( kukonzekeratu; kusawononga ndalama; kusabwereka ndalama). [fy-CN tsa. 40, ndime 4]
29. ‘Mngelo wolimba’ mwachionekere ndi (Gabrieli; Satana; Yesu Kristu wolemekezedwa). (Chiv. 10:1) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani re tsa. 155, ndime 3.]
30. Pa Chivumbulutso 11:11, “masiku atatu ndi nusu lake,” pamene otsalira odzozedwa anali ngati mitembo m’maso mwa adani awo, ndi (zaka zitatu ndi theka; nthaŵi yaifupi; miyezi itatu ndi theka). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani re tsa. 167, ndime 21.]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Miy. 8:30; Mat. 19:13-15; Aheb. 2:1; Yak. 4:15; 1 Pet. 3:4
31. Kuti tilimbane ndi mabodza anthaŵi ndi nthaŵi amene ali m’dzikoli, tiyenera “kusamaliradi” Mawu a Mulungu mwa kukhala ndi zizoloŵezi zabwino za kuphunzira ndiponso kukhala ndi ndandanda yabwino yoŵerenga Baibulo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 1/1 tsa. 7, ndime 9.]
32. Nthaŵi zonse tikamakonza za mtsogolo, tiyenera kulingalira mwapemphero mmene zimagwirizanirana ndi chifuno cha Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 11/15 tsa. 21, ndime 10-11.]
33. “Mzimu wofatsa ndi wachete” wa mkazi ndi mayi wachikristu sumangosangalatsa mwamuna wake komanso chofunika kwambiri umasangalatsa Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 5/15 tsa. 19, ndime 12.]
34. Potsanzira chitsanzo cha Yehova, atate wabwino ayenera kukulitsa unansi wabwino ndi wachikondi kwa mwana wake kuyambira pachiyambi penipeni pa moyo wa mwanayo. [fy-CN tsa. 53, ndime 7]
35. Popeza kuti Yesu sanasankhe podalitsa ana ang’onoang’ono, munthu sayenera kuona ngati kuti ana aamuna amapambana ana aakazi. [fy-CN tsa. 52, ndime 4]
S-97-CN Mal, Moz & Zam #296b 12/98