Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 3/15 tsamba 30
  • Khalani Okhazikika M’chikhulupiriro!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Okhazikika M’chikhulupiriro!
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mayendedwe Ozikidwa pa Malamulo Amakhalidwe Abwino Aumulungu
  • Chipiriro Chimadzetsa Madalitso
  • Chotandizira Kupirira Pobvutika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Kodi Akazi Azibisa Kukongola Kwawo?
    Galamukani!—2005
  • Kumvera Ulamuliro Kumene Kuli Kopindulitsa
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Tigwiritse Chikhulupiriro Chathu Chamtengo Wapatali!
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 3/15 tsamba 30

Khalani Okhazikika M’chikhulupiriro!

Mfundo Zazikulu Zochokera m’Petro Woyamba

MBONI ZA YEHOVA zimayang’anizana ndi ziyeso, kapena zopsinja zosiyanasiyana za chikhulupiriro chawo. M’maiko ena, ntchito yawo yolalikira Ufumu imachitidwa moyang’anizana ndi chizunzo chachikulu. Wokhala kumbuyo kwa izi ndi zoyesayesa zina zofuna kuwononga unansi wawo ndi Mulungu ndiye Satana Mdyerekezi. Koma iye sadzapambana, popeza kuti Yehova amalimbitsa atumiki ake​—inde, kukhazikika m’chikhulupiriro.

Mtumwi Petro anapatsidwa mwaŵi wa ‘kukhazikitsa abale ake’ omwe anali ‘kuchitidwa chisoni ndi mayesero amitundumitundu.’ (Luka 22:32; 1 Petro 1:6, 7) Iye anatero m’kalata yake yoyamba, yolembedwa pafupifupi 62-64 C.E. ali ku Babulo. M’kalatayo Petro analangiza, kutonthoza, ndi kulimbikitsa Akristu Achiyuda ndi Akunja, kuwathandiza kuchirimika ziukiro za Satana ndi kukhalabe ‘okhazikika m’chikhulupiriro.’ (1 Petro 1:1, 2; 5:8, 9) Tsopano popeza kuti nthaŵi ya Mdyerekezi njaifupi ndipo kuukira kwake nkwankhanza, ndithudi anthu a Yehova angapindule kuchokera m’mawu ouziridwa a Petro.

Mayendedwe Ozikidwa pa Malamulo Amakhalidwe Abwino Aumulungu

Kaya chiyembekezo chathu nchakumwamba kapena chapadziko lapansi, chiyenera kutithandiza kupirira ziyeso ndi kuchita zinthu m’njira yaumulungu. (1:1–2:12) Chiyembekezo cha choloŵa chakumwamba chimachititsa odzozedwa kusangalala poyang’anizana ndi ziyeso, zimene kwenikweni zimayenga chikhulupiriro chawo. Pokhala nyumba yauzimu yomangidwa pa maziko a Kristu, iwo amapereka nsembe zauzimu zolandirika kwa Mulungu ndipo ngamayendedwe okoma omwe amadzetsera Iye ulemerero.

Zochita zathu ndi anthu anzathu onse ziyenera kulamulidwa ndi malamulo amakhalidwe abwino aumulungu. (2:13–3:12) Petro anasonyeza kuti tiyenera kugonjera olamulira aumunthu. Akapolo anafunikira kugonjera ambuye awo, ndipo akazi amuna awo. Mayendedwe aumulungu a mkazi Wachikristu angakope mwamuna wake wosakhulupirira ku chikhulupiriro chowona. Ndipo mwamuna wokhulupirira ayenera ‘kuchitira mkazi wake ulemu monga chotengera chochepa mphamvu.’ Akristu onse ayenera kusonyeza chifundo, kukhala ndi chikondi cha pa abale, kuchita chokoma, ndi kulondola mtendere.

Chipiriro Chimadzetsa Madalitso

Chipiriro chokhulupirika cha kuvutika kwa Akristu owona chidzatulukapo madalitso. (3:13–4:19) Ngati tivutika kaamba ka chilungamo, tiyenera kukhala okondwa. Kuwonjezerapo, popeza kuti Kristu anamva zoŵaŵa m’thupi kutitsogolera kwa Mulungu, sitiyeneranso kukhalira moyo zikhumbo zathupi. Ngati tipirira ziyeso mokhulupirika, tidzakhala ndi phande m’kusangalala kwakukulu pavumbulutso la Yesu. Kusenza chitonzo kaamba ka dzina la Kristu, kapena monga ophunzira ake, kuyenera kutikondweretsa chifukwa chakuti kumatsimikizira kuti tiri ndi mzimu wa Yehova. Chotero pamene tivutika mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, tiyeni tidzipereke kwa iye ndi kupitirizabe kuchita chokoma.

Monga Akristu, tifunikira kuchita ntchito zathu mokhulupirika ndi kudzichepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu. (5:1-14) Akulu ayenera kuŵeta gulu la Mulungu mwaufulu, ndipo tonsefe tiyenera kusenzetsa Yehova nkhaŵa zathu, pozindikira kuti iye amatisamaliradi. Tifunikiranso kutenga kaimidwe kathu motsutsana ndi Mdyerekezi ndipo tisalefulidwe konse, popeza kuti abale athu amakumana ndi kuvutika kumodzimodziko konga kwathu. Nthaŵi zonse kumbukirani kuti Yehova Mulungu adzatilimbitsa ndipo adzatikhozetsa kukhala okhazikika m’chikhulupiriro.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 30]

Kudzikometsera Kwachikazi: Polangiza akazi Achikristu, Petro anati: “Ndipo musalole kudzikometsera kwanu kukhale kuja kwakunja kwa kuluka tsitsi ndi kwa kuvala zokometsera zagolidi kapena kuvala zovala zakunja, koma kuloleni kukhale munthu wobisika wa mtima wovala chovala chosavunda cha mzimu wachete ndi wodekha, chimene chiri chamtengo waukulu m’maso mwa Mulungu.” (1 Petro 3:3, 4, NW) Mkati mwa zaka za zana loyamba C.E., akazi achikunja kaŵirikaŵiri anali ndi mapesedwe atsitsi onkitsa, kuluka tsitsi lawo lalitali m’masitayelo okometsetsa ndi kuika zokometsera zagolidi m’dzikondo. Mwachiwonekere, ambiri anachita tero monga kudziwonetsera​—chinthu chosayenera kwa Akristu. (1 Timoteo 2:9, 10) Komabe, sikukometsera konse kumene kuli kolakwika, popeza kuti Petro akuphatikizapo “kuvala zovala zakunja”​—chinthu chofunikadi. Zokometsera zinkagwiritsiridwanso ntchito ndi atumiki akale a Mulungu. (Genesis 24:53; Eksodo 3:22; 2 Samueli 1:24; Yeremiya 2:32; Luka 15:22) Komabe, mkazi Wachikristu mwanzeru amapeŵa zokometsera zopambanitsa ndi kavalidwe kodzutsa chilakolako ndipo ayenera kusamala kuti kugwiritsira ntchito kulikonse kwa zopakapaka nkoyenerera. Mfundo ya kulangiza kwautumwi njakuti mkazi ayenera kuika chisamaliro, osati pakukometsera kwakunja, koma kwamkati. Kuti akhaledi wokongola, iye ayenera kuvala mwachikatikati ndi kukhala nkaimidwe ka munthu wowopa Mulungu.​—Miyambo 31:30; Mika 6:8.

[Mawu a Chithunzi]

Israel Department of Antiquities and Museums; Israel Museum/​David Harris

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena