Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. January: Lililonse la mabuku a masamba 192 limene mpingo ungakhale nalo lofalitsidwa isanafike 1985. Mipingo imene ilibe mabuku amenewa ingagaŵire buku lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? kapena Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Mipingo iyambe kuoda mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 1998 paoda yawo ya mabuku ya December. Mabaundi voliyumu adzakhalako achingelezi okha. Mpaka pamene mabaundi voliyumu adzakhalako ndi kutumizidwa, adzaonekera monga “Zoyembekezera” pa mpambo wolongedzera mabuku wa mipingo. Mabaundi voliyumu ndi zinthu za oda yapadera.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamsankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Mutatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo pambuyo popereka lipoti la maakaunti lotsatira.
◼ Chikumbutso cha m’chaka cha 2000 chidzakhalako Lachitatu, pa April 19, dzuŵa litaloŵa. Takudziŵitsani zimenezi pasadakhale kuchitira kuti abale apezeretu maholo amene angafunikire, ngati kuli koti pali mipingo ingapo yomwe imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndiponso kuti mwina mungafune kupezeratu malo ena. Akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo nkutsimikizira kuti sipadzakhala zochitika zina zododometsa pamalopo, kuti pologalamu ya Chikumbutsoyo idzachitike mwamtendere ndi mwadongosolo. Popeza kuti chochitikacho nchapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu yemwe alidi wokhoza bwino kwenikweni, osati kumangosinthana kapena osati chaka chilichonse azingokamba munthu mmodzimodziyo. Zidzakhala zosiyana ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu wokhoza bwino kukamba nkhani.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Imbirani Yehova Zitamando (Lalikulu ndi laling’ono)—Chingelezi
1997 Watchtower Publications Index—Chingelezi