Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fy mutu 4 tsamba 39-50
  • Kodi Mungasamalire Motani Banja?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungasamalire Motani Banja?
  • Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KHALIRANI MOYO ZIMENE MULI NAZO
  • KUTHANDIZANA NTCHITO
  • UKHONDO—NCHIFUKWA NINJI ULI WOFUNIKA KWAMBIRI?
  • CHILIMBIKITSO CHIMATITHANDIZA
  • N’chifukwa Chiyani Ukhondo Uli Wofunika?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mulungu Amakonda Anthu Oyera
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kumaumanga Moyo Wabanja Wacimwemwe
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Makonzedwe a Yehova Achikondi a Banja
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
fy mutu 4 tsamba 39-50

Mutu 4

Kodi Mungasamalire Motani Banja?

1. Kodi nchifukwa ninji kusamalira banja kungakhale kovuta kwambiri lerolino?

“MKHALIDWE wa dzikoli ukusintha.” (1 Akorinto 7:31, NW) Mawuwo analembedwa zaka zoposa 1,900 kalelo, ndipo ali oona kwenikweni lerolino! Zinthu zikusintha, makamaka moyo wa m’banja. Zimene zinaoneka kukhala zabwino ndi zamwambo zaka 40 kapena 50 zapitazo, kaŵirikaŵiri zimakhala zosafunika lerolino. Chifukwa cha zimenezi, kusamalira bwino banja kungakhale ndi zothetsa nzeru zazikulu. Komabe, ngati mulabadira mapulinsipulo a Malemba, mungathe kulaka zothetsa nzeru zimenezo.

KHALIRANI MOYO ZIMENE MULI NAZO

2. Kodi ndi mikhalidwe yazachuma yotani imene imachititsa vuto m’banja?

2 Lerolino anthu ambiri salinso okhutira ndi moyo wapafupi, malinga ndi mkhalidwe wa banja lawo. Pamene dziko la malonda likupanga zinthu zochulukirachulukira ndi kugwiritsira ntchito maluso ake akusatsa malonda kukopa nawo anthu, mamiliyoni a atate ndi amayi akutayira maola ambiri kuntchito kuti akhoze kugula zinthu zimenezo. Mamiliyoni ena akuyang’anizana ndi vuto la tsiku ndi tsiku la kupeza chakudya chokha. Amatayira nthaŵi yaikulu kuntchito kuposa mmene zinalili kumbuyoku, mwinamwake akumagwira ntchito ziŵiri, kuti akhoze kulipirira zofunika zazikulu chabe. Komabe, ena angakonde kupeza ntchito, pakuti ulova wakhala vuto lofala. Inde, si nthaŵi zonse pamene moyo umakhala wosavuta kwa banja lamakono, koma mapulinsipulo a Baibulo angathandize mabanja kudziŵa mochitira ndi mkhalidwewo.

3. Kodi ndi pulinsipulo liti limene mtumwi Paulo analongosola, ndipo kuligwiritsira ntchito kungathandize motani munthu kukhala wachipambano pakusamalira banja?

3 Mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto azachuma. Mwa kulimbana nawo, anatengapo phunziro labwino, limene akulongosola m’kalata yake kwa bwenzi lake Timoteo. Paulo akulemba kuti: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:7, 8) Zoona, banja limafuna zoposa chabe chakudya ndi zovala. Limafunanso malo okhala. Ana amafunikira kuphunzira. Ndipo pali kulipirira mankhwala ndi zinthu zina. Chikhalirechobe, pulinsipulo la mawu a Paulo limagwirabe ntchito. Ngati timakhutira ndi zofunika zazikulu m’malo mwa kuyesayesa kukhutira ndi zofunika zazing’ono, moyo udzakhala wosavuta kwambiri.

4, 5. Kodi kulingalira pasadakhale ndi kukonzekeratu kungathandize motani pakusamalira banja?

4 Pulinsipulo lina lothandiza limapezeka m’fanizo lina la Yesu. Iye anati: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?” (Luka 14:28) Yesu pano akulankhula za kulingalira pasadakhale, kukonzekeratu. Taona m’mutu wapitawo mmene zimenezi zilili zothandiza kwa achinyamata ofuna kukwatirana. Ndipo pambuyo pa tsiku la ukwati, zimathandizanso pakusamalira banja. Kulingalira pasadakhale pankhani imeneyi kumafuna kukhala ndi bajeti, kukonzekera pasadakhale kuti mugwiritsire ntchito mwanzeru ndalama zimene muli nazo. Mwa njira imeneyi banja lingasamalire bwino ndalama zowonongedwa, likumapatula zogulira zinthu zofunika kwambiri tsiku ndi tsiku kapena mlungu ndi mlungu, ndi kusakhalira moyo zimene alibe.

5 M’maiko ena, kupanga bajeti kotero kungaphatikizepo kuletsa chikhumbo cha kutenga ngongole za chiwongola dzanja chachikulu zogulira zinthu zosafunika kwenikweni. M’maiko enanso, kungaphatikizepo kudziletsa kwambiri pakugwiritsira ntchito makadi angongole. (Miyambo 22:7) Kungafunenso kukaniza chilakolako cha kugula mwasontho—kungogula chinthu mofulumira osalingalira kufunika kwake ndi zotsatirapo zake. Ndiponso, kupanga bajeti kudzasonyeza kuti kuwononga ndalama kwadyera pa juga, kusuta fodya, ndi kumwetsa moŵa kumawononga chuma cha banja, ndiponso kumawombana ndi mapulinsipulo a Baibulo.—Miyambo 23:20, 21, 29-35; Aroma 6:19; Aefeso 5:3-5.

6. Kodi ndi mfundo zoona ziti za m’Malemba zimene zimathandiza aja okakamizidwa kukhala paumphaŵi?

6 Koma bwanji za aja amene mikhalidwe imawakakamiza kukhala paumphaŵi? Choyamba, iwo angatonthozedwe mwa kudziŵa kuti mavuto a dzikoli ali akanthaŵi chabe. M’dziko latsopano lomwe likufika mofulumira, Yehova adzachotsamo umphaŵi limodzi ndi zoipa zina zonse zimene zimasautsa anthu. (Salmo 72:1, 12-16) Pakali pano, Akristu oona, ngakhale ngati ali osauka kwambiri, sali opsinjika mtima kotheratu, pakuti ali ndi chikhulupiriro m’lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” Chotero, wokhulupirira anganene mwachidaliro kuti: “Mthandizi wanga ndiye Ambuye [“Yehova,” NW]; sindidzawopa.” (Ahebri 13:5, 6) M’masiku ano ovuta, Yehova wachirikiza alambiri ake m’njira zambiri pamene iwo atsatira mapulinsipulo ake ndi kuika Ufumu wake patsogolo m’moyo wawo. (Mateyu 6:33) Ambiri a iwo angachitire umboni, mwa kunena m’mawu a mtumwi Paulo kuti: “M’zinthu zonse ndi m’mikhalidwe yonse ndaphunzira chinsinsi cha kukhuta ndi cha kumva njala komwe, kukhala nazo zochuluka ndi kusoŵa komwe. M’zinthu zonse ndili nayo nyonga mwa iye amene apatsa mphamvu kwa ine.”—Afilipi 4:12, 13, NW.

KUTHANDIZANA NTCHITO

Zithunzi patsamba 42

Kusamalira banja ndi ntchito ya banja lonse

7. Kodi ndi mawu ati a Yesu, amene ngati agwiritsiridwa ntchito, adzathandiza kusamalira banja mwachipambano?

7 Chakumapeto kwa utumiki wake padziko lapansi, Yesu anati: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:39) Kugwiritsira ntchito uphungu umenewu m’banja kumathandiza kwambiri pakusamalira banja. Ndi iko komwe, kodi anzathu apafupi kwambiri ndi okondedwa ndani, oposa amene tikhala nawo m’nyumba imodzi—amuna, akazi, makolo ndi ana? Kodi a m’banja angasonyeze motani chikondi kwa wina ndi mnzake?

8. Kodi chikondi chingasonyezedwe motani m’banja?

8 Njira imodzi ndiyo yakuti aliyense wa m’banja achite mbali yake ya ntchito zapanyumba. Chotero, ana afunikira kuphunzitsidwa kuchotsa zinthu zawo atamaliza kuzigwiritsira ntchito, kaya ndi zovala kapena zoseŵeretsa. Kuyala bwino pogona mmaŵa uliwonse kungafune kutayirapo nthaŵi ndi kuyesayesa, koma kumathandiza kwambiri kusamalira banja. Ndithudi, kusokoneza zinthu kwakung’ono kudzakhalapobe nthaŵi zina, koma onse angathandizane kusunga nyumba ili yaukhondo, ndi kuyeretsa pambuyo pa chakudya. Mzimu wa ulesi, wakusamala zaumwini zokha, ndi wakusunga chakukhosi ndi kuchita zinthu monyinyirika umayambukira ena moipa. (Miyambo 26:14-16) Koma mzimu wosangalala ndi wofuna kutumikira umamangirira moyo wa banja kukhala wachimwemwe. “Mulungu akonda wopereka mokondwerera.”—2 Akorinto 9:7.

9, 10. (a) Kodi ndi mtolo uti umene kaŵirikaŵiri umakhala pa mkazi wapanyumba, ndipo kodi umenewu ungapeputsidwe motani? (b) Kodi ndi lingaliro loyenera liti limene laperekedwa ponena za ntchito yapanyumba?

9 Kulingalirana ndi chikondi zidzathandiza kuletsa mkhalidwe umene uli vuto lalikulu m’nyumba zina. Amayi mwamwambo ndiwo amachirikiza kwambiri moyo wapanyumba. Amasamalira ana, kuyeretsa panyumba, kuchapa zovala za banja, ndi kugula ndi kuphika chakudya. M’maiko ena, akazi mwachizoloŵezi amagwira ntchito m’minda, kukagulitsa za m’munda kumsika, ndi kuthandizira m’njira zambiri kupeza ndalama za banja. Ngakhale kumene kunalibe chizoloŵezi chimenechi, mikhalidwe yakakamiza akazi okwatiwa mamiliyoni ambiri kukaloŵa ntchito kunja. Mkazi wokwatiwa amene alinso mayi ndipo amagwira ntchito mwamphamvu m’mbali zosiyana zimenezi afunikira kuthokozedwa. Mofanana ndi “mkazi wangwiro” wolongosoledwa m’Baibulo, masiku ake ali odzala bwino. “Sadya zakudya za ulesi.” (Miyambo 31:10, 27) Komabe, zimenezi sizitanthauza kuti mkazi ayenera kugwira yekha ntchito zapanyumba. Pambuyo pakuti onse aŵiri mwamuna ndi mkazi afika panyumba atagwira ntchito tsiku lonse, kodi mkazi ayenera kugwira yekha ntchito zapanyumba pamene mwamunayo ndi ena a m’banja akupumula? Ndithudi ayi. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:13, 14.) Motero, mwachitsanzo, ngati mayi adzakonza chakudya, angayamikire kwambiri ngati ena athandiza kusamalira zofunikira ndi kukonza pathebulo, kukagula zinthu zina, kapena kuyeretsa izi ndi izi panyumba. Inde, onse angagaŵane thayoli.—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:2.

10 Ena anganene kuti: “Kwathu si ntchito ya mwamuna kuchita zimenezo.” Zimenezo zingakhale zoona, koma kodi sikungakhale bwino kulingaliraponso pankhani imeneyi? Pamene Yehova Mulungu anapanga banja, sanalamule kuti ntchito zina zidzachitidwa ndi akazi okha. Panthaŵi ina, pamene mwamuna wokhulupirika Abrahamu anachezeredwa ndi amithenga apadera aŵiri ochokera kwa Yehova, iye mwini anatenga mbali m’kukonza chakudya ndi kuchigaŵira kwa alendowo. (Genesis 18:1-8) Baibulo limalangiza kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha.” (Aefeso 5:28) Ngati pamapeto pa tsiku, mwamuna watopa ndipo akufuna kupumula, kodi sikwachionekere kuti mkazinso akumva chimodzimodzi, ndipo mwina kuposerapo? (1 Petro 3:7) Pamenepo, kodi sikungakhale koyenera ndi kwachikondi kwa mwamuna kuthandiza ntchito zapanyumba?—Afilipi 2:3, 4.

11. Kodi Yesu anapereka motani chitsanzo chabwino kwa aliyense m’banja?

11 Yesu ali chitsanzo chabwino koposa cha munthu amene anakondweretsa Mulungu ndi kudzetsa chimwemwe pa anzake. Ngakhale kuti sanakwatirepo, Yesu ali chitsanzo chabwino kwa amuna, limodzinso kwa akazi ndi ana omwe. Iye anati za iye mwini: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira,” ndiko kuti, kugwirira ntchito ena. (Mateyu 20:28) Ali achisangalalo chotani nanga mabanja mmene onse amakulitsa mzimu umenewu!

UKHONDO—NCHIFUKWA NINJI ULI WOFUNIKA KWAMBIRI?

12. Kodi Yehova amafunanji kwa awo amene amamtumikira?

12 Pulinsipulo lina la Baibulo limene lingathandize kusamalira banja limapezeka pa 2 Akorinto 7:1. Pamenepo timaŵerenga kuti: ‘Tileke chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.’ Amene amalabadira mawu ouziridwa ameneŵa ali oyanjidwa ndi Yehova, amene amafuna “mapembedzedwe oyera ndi osadetsa.” (Yakobo 1:27) Ndipo mabanja awo amapeza mapindu ake.

13. Kodi nchifukwa ninji ukhondo uli wofunika pakusamalira banja?

13 Mwachitsanzo, Baibulo limatilonjeza motsimikiza kuti tsiku lidzafika pamene sikudzakhala matenda ndi kudwala. Panthaŵiyo, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4, 5) Komabe, pakali pano banja lililonse lidzadwazikabe winawake nthaŵi ndi nthaŵi. Ngakhale Paulo ndi Timoteo anadwala. (Agalatiya 4:13; 1 Timoteo 5:23) Komabe, akatswiri a zamankhwala amanena kuti matenda ambiri ali opeŵeka. Mabanja anzeru amapeŵa matenda ena opeŵeka pamene apeŵa litsiro lakuthupi ndi lauzimu. Tiyeni tione kuti zili motani.—Yerekezerani ndi Miyambo 22:3.

14. Kodi chiyero cha makhalidwe chingatetezere motani banja ku matenda?

14 Chiyero cha mzimu chimaphatikizapo chiyero cha makhalidwe. Monga tidziŵa, Baibulo limalimbikitsa miyezo yapamwamba ya makhalidwe ndi kutsutsa chisembwere cha mtundu uliwonse kunja kwa ukwati. “Adama, . . . kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Kusunga miyezo yokhwima imeneyi ndi kofunika kwambiri kwa Akristu okhala m’dzikoli lovunda. Kuchita zimenezo kumakondweretsa Mulungu, ndipo kumathandizanso kutetezera banja ku matenda opatsirana mwa kugonana monga AIDS, chindoko, chinzonono, ndi chlamydia.—Miyambo 7:10-23.

15. Perekani chitsanzo cha kusoŵa chiyero chakuthupi kumene kungachititse matenda opeŵeka.

15 ‘Kuleka ife eni chodetsa chonse cha thupi’ kumathandiza kutetezera banja ku matenda enanso. Matenda ambiri amadza ndi kupanda chiyero chakuthupi. Chitsanzo chodziŵika bwino ndi chizoloŵezi cha kusuta. Kusuta sikumangonunkhitsa m’mapapu, zovala, ndi mpweya komanso kumadwalitsa anthu. Anthu mamiliyoni ambiri amafa chaka chilichonse chifukwa cha kusuta fodya. Tangolingalirani; chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri sakanadwala ndi kufa mwamsanga ngati akanapeŵa ‘chodetsa thupi’ chimenecho!

16, 17. (a) Kodi ndi lamulo lotani loperekedwa ndi Yehova limene linatetezera Aisrayeli ku matenda ena? (b) Kodi ndi motani mmene pulinsipulo la Deuteronomo 23:12, 13 lingagwirire ntchito m’mabanja onse?

16 Talingalirani chitsanzo china. Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Mulungu anapatsa mtundu wa Israyeli Chilamulo chake kuti alinganize kalambiridwe kawo, ndi moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Chilamulo chimenecho chinathandiza kutetezera mtunduwo ku matenda mwa kuika malamulo aang’ono a zaukhondo. Limodzi la malamulo amenewo linali la katayidwe ka zonyansa za munthu, zimene zinayenera kufotseredwa bwino kutali ndi msasa kotero kuti malo okhalako anthu asaipitsidwe. (Deuteronomo 23:12, 13) Lamulo lakale limenelo lidakali uphungu wabwino. Ngakhale lerolino anthu amadwala ndi kufa chifukwa chosalitsatira.a

17 Mogwirizana ndi pulinsipulo la lamulolo la Aisrayeli, chipinda chosambira cha banja ndi chimbudzi—kaya zikhale mkati kapena kunja kwa nyumba—ziyenera kusungidwa zaudongo ndi zothiridwa mankhwala akupha tizilombo. Ngati chimbudzi sichisungidwa chaukhondo ndi chovundikira, ntchentche zidzasonkhana kumeneko ndi kufalitsa tizilombo tamatenda kumalo ena m’nyumbamo—ndi kuchakudya chimene timadya! Ndiponso, ana ndi achikulire omwe ayenera kusamba m’manja atachokera kumalowo. Ngati satero, pochoka kumeneko amabweretsa tizilombo tamatenda pakhungu lawo. Malinga ndi kunena kwa dokotala wina wa ku France, kusamba m’manja “kudakali imodzi ya njira zotsimikizirika zoletsera matenda ena a m’mimba, zifuŵa, kapena oyambukira khungu.”

Chithunzi patsamba 47

Kusunga zinthu zili zaukhondo nkochipa kuposa kugula mankhwala

18, 19. Kodi ndi njira zotani zimene zaperekedwa zosungira nyumba kukhala yaukhondo ngakhale m’malo a anthu osauka?

18 Zoona, ukhondo ngwovuta m’malo okhala anthu osauka. Munthu wina amene amadziŵa bwino malo oterowo anafotokoza kuti: “Mkhalidwe wa kutentha kwambiri umachititsa ntchito yoyeretsa kukhala yovuta kwenikweni. Fumbi lofiira la chimphepo limadzaza mng’alu uliwonse wa nyumba. . . . Kuchuluka kwa anthu m’mizinda, ndiponso m’malo ena akumidzi, kumachititsanso mikhalidwe yangozi. Malo otayira za m’chimbudzi okhala poyera, miyulu ya zinyalala zosatoledwa, zimbudzi za anthu ambiri zauve, makoswe onyamula matenda, mphemvu, ndi ntchentche zimapezeka paliponse.”

19 Kusunga ukhondo m’mikhalidwe imeneyi nkovuta. Komabe, kuyesayesa kumeneko mpake. Sopo ndi madzi ndi ntchito pang’ono nzochipa kuposa mankhwala ndi ndalama zolipira chipatala. Ngati mukukhala m’malo oterowo, yesayesani mmene mungakhozere kusunga nyumba yanu ili yaukhondo ndi yosakhala ndi ndowe za ziŵeto pabwalo. Ngati kamsewu kopita panyumba panu kamakhala ndi matope m’nyengo za mvula, kodi mungaikemo dothi la nsangalawe kapena miyala kuti matope asamafike panyumba? Ngati munthu wavala nsapato kapena patapata, kodi angazivule asanaloŵe m’nyumba? Ndiponso, muyenera kusunga malo anu otungako madzi kukhala ali aukhondo. Ziŵerengero zimasonyeza kuti pafupifupi anthu mamiliyoni aŵiri amafa chaka chilichonse ndi matenda ochititsidwa ndi madzi odetsedwa ndi zimbudzi zosasamalidwa bwino.

20. Kuti nyumba ikhale yaukhondo, kodi ndani ali ndi thayo?

20 Nyumba yabwino imadalira pa aliyense—mayi, tate, ana, ndi alendo omwe. Mayi wina wa ana asanu ndi atatu wa ku Kenya anati: “Onse aphunzira kuchita mbali zawo.” Nyumba yoyeretsedwa bwino ndi yaukhondo imapereka chithunzi chabwino cha banja lonse. Mwambi wachispanya umati: “Palibe chidani pakati pa umphaŵi ndi ukhondo.” Kaya munthu akukhala m’chinyumba chachikulu chokongola, m’nyumba yosanja, m’nyumba wamba, kapena m’chithando, ukhondo ndiwo kiyi ya banja lathanzi labwino.

CHILIMBIKITSO CHIMATITHANDIZA

21. Mogwirizana ndi Miyambo 31:28, kodi nchiyani chimene chingathandize kudzetsa chimwemwe m’banja?

21 Polongosola za mkazi wangwiro, buku la Baibulo la Miyambo limati: ‘Ana ake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama.’ (Miyambo 31:28) Kodi ndi liti pamene munathokoza wina wa m’banja lanu? Ndithudi, tili ngati zomera m’nthaŵi ya ngululu, zokonzekera kuphuka pamene zilandira kufunda ndi chinyontho. Ifenso timafunikira kuthokozedwa mwachikondi. Kumathandiza mkazi kudziŵa kuti mwamuna wake amayamikira ntchito zake zamphamvu ndi chisamaliro chake chachikondi ndi kuti samamuona mopepuka. (Miyambo 15:23; 25:11) Ndipo kumamvetsa bwino pamene mkazi athokoza mwamuna wake pantchito zake za kunja ndi zapanyumba. Ananso amakula bwino pamene makolo awo awatamanda pantchito zawo zapanyumba, kusukulu, kapena mumpingo wachikristu. Inde, mawu othokoza angakhale ochepa, koma amachita zazikulu! Kodi kumakutayitsani chiyani kunena kuti: “Zikomo”? Zochepa kwenikweni, koma phindu lake limakhala lalikulu kwabasi pakulimbikitsa banja.

22. Kodi chofunika nchiyani kuti banja ‘likhazikike’ zolimba, ndipo kodi zingapezeke motani?

22 Kusamalira banja kumakhala kovuta pa zifukwa zambiri. Komabe, kukhoza kuchitika ndi chipambano. Mwambi wa Baibulo umati: “Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa.” (Miyambo 24:3) Nzeru ndi luntha zingapezeke ngati onse m’banja ayesayesa kuphunzira chifuniro cha Mulungu ndi kuchigwiritsira ntchito m’moyo wawo. Kuyesayesa konseko kuti mupeze banja lachimwemwe mpake ndithu!

a M’buku la malangizo opeŵera kutseguka m’mimba—nthenda yofala imene imapha makanda ambiri—World Health Organization ikuti: “Ngati mulibe chimbudzi: pitani kuthengo kutali ndi nyumba, ndi kutali ndi malo oseŵererako ana, ndi pamtunda wa mamita osachepera 10 kuchokera pamadzi; fotserani zonyansazo ndi dothi.”

KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . BANJA KUSAMALIRA NYUMBA YAWO?

Kuli kwanzeru kukhutira ndi zofunika zazikulu zokha za moyo.—1 Timoteo 6:7, 8.

Yehova sadzasiya awo amene amamtumikira.—Ahebri 13:5, 6.

Kukonda ena kuli mkhalidwe waukulu wa Akristu.—Mateyu 22:39.

Akristu amakhala oyera mwa kuthupi ndi kuuzimu.—2 Akorinto 7:1.

MADZI OYERA, THANZI LABWINO

Bungwe la World Health Organization likupereka njira zina zogwira ntchito kwa anthu okhala m’maiko kumene madzi oyera angakhale ovuta kupeza kumenenso kungakhale kulibe zimbudzi zamakono.

“Tungani madzi akumwa ndi kuwasunga m’mitsuko yotsukidwa bwino. Vundikirani mtsuko wa madzi ndipo musalole ana kapena zifuyo kumwamo. . . . Potungamo madzi gwiritsirani ntchito kokha chotungira chokhala ndi chogwirira chachitali chogwiritsira ntchito pachifuno chokhacho. Khutulani madzi ndi kutsuka mtsukowo tsiku lililonse.

“Ŵiritsani madzi okonzera chakudya kapena zakumwa za ana. . . . Madzi amangofunika kuŵiritsa timphindi toŵerengeka.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena