Pendani Mawu a Yehova Tsiku Lililonse!
1 Tsiku lililonse limabweretsa mavuto ena pa chikhulupiriro chanu. Mwinamwake mnzanu wachikunja amakukakamizani kuchita chibwenzi. Aphunzitsi anu akufuna kuti mudzapeze ntchito ya kudziko, kapena abwana anu akufuna kuti muzigwira ntchito maola ambiri kuposa ofunikira. Thanzi lanu lingakhale likufooka. Ngakhale kuti ziyeso zoterozo zingakufikireni nthaŵi ina iliyonse, simuli nokha. Yehova ali chire kukupatsani nzeru yofunika kuti mupirire. Kupenda lemba la Baibulo ndi ndemanga mu Kusanthula Malemba ndi njira imodzi imene mungaphunzirire Mawu a Yehova mokhazikika. Kodi mumagwiritsa ntchito makonzedwe ameneŵa?
2 Thandizo Lilipo: Yesaya 30:20 (NW) amafotokoza Yehova monga “Mlangizi Wamkulu” komwe anthu a Mulungu angapezeko chithandizo. Amakupatsani zomwe mungafune polimbana ndi mavuto a chikhulupiriro chanu. Motani? Vesi lotsatira likufotokoza kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.” Lerolino, Yehova watumiza “mawu” ake m’Malemba ndi m’zofalitsa za “kapolo wokhulupirika.” (Mat. 24:45) Mu nkhani za mu Nsanja ya Olonda za m’mbuyomo, muli nzeru yochuluka zedi yokhudza pafupifupi mbali iliyonse ya moyo wachikristu. Kupenda zomwe zalembedwa mu Kusanthula Malemba kumakuthandizani kumanga nkhokwe ya chidziŵitso imene ili yothandiza kwambiri polimbana ndi ziyeso za mtundu uliwonse.—Yes. 48:17.
3 Pezani Nthaŵi: Ngakhale kuti nthaŵi ya m’maŵa inali ya ntchito zambiri, mayi wina chinali chizoloŵezi chake kuŵerenga ndi kukambirana lemba komanso ndemanga yake pamodzi ndi mwana wake pachakudya cha m’maŵa. Zimenezi ndiponso pemphero, ndiwo anali mawu omaliza amene anali kuwamva m’maŵa uliwonse asanapite kusukulu. Zinam’limbikitsa kukana pamene ena amam’nyengerera kuchita naye zachiwerewere. Zinam’thandiza kupeŵa mzimu wokonda dziko lako, ndipo zinam’limbikitsa kupereka umboni molimba mtima kwa ana a sukulu ndi aphunzitsi omwe. Ngakhale kuti ndiye yekha amene anali Mboni pasukulupo, samaona kuti anali yekha.
4 Funani malangizo ndi chitsogozo kwa Yehova ndi m’Mawu ake. Mukatero, mudzam’dziŵadi, monga bwenzi lodalirika. Tembenukirani kwa iye tsiku lililonse! Inu pamodzi ndi mamiliyoni ena padziko lonse amene amapenda Mawu a Mulungu tsiku lililonse, maso anu akhaletu “maso oona Mlangizi wanu Wamkulu.”