Kodi Mwakonzekera Kukalalikira Kusukulu?
1. Kodi mumakhala ndi mwayi wotani kusukulu?
1 Achinyamata achikhristu amakumana ndi mavuto ambiri kusukulu. Komanso ali ndi mwayi ‘wochitira umboni choonadi.’ (Yoh. 18:37) Kodi mwakonzekera bwino kukachitira umboni choonadi?
2. Kodi mwaphunzitsidwa motani kuti muzilalikira kusukulu?
2 Pofuna kukuthandizani kuti zonse zikuyendereni bwino, mwakhala mukuphunzitsidwa zambiri ndi Yehova, makolo anu ndiponso kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Miy. 1:8; 6:20; 23:23-25; Aef. 6:1-4; 2 Tim. 3:16, 17) Pofika pano muyenera kuti mukudziwa bwino mavuto amene mungakakumane nawo kusukulu. Popeza mwaphunzitsidwa zimene Mulungu amafuna ndiponso za malo amene mukupita, konzekerani kukachitira umboni choonadi. (Miy. 22:3) Ganizirani mofatsa malangizo ndiponso mfundo za m’Malemba zimene zili m’mabuku awiri a “Zimene Achinyamata Amafunsa” ndiponso nkhani za achinyamata zimene zimapezeka nthawi zonse mu Galamukani!
3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zidzakupatsani mwayi wolalikira kusukulu?
3 Sukulu, monga gawo lanu lapadera, idzakupatsani mwayi wolalikira m’njira zambiri. Ena akamaona kavalidwe kanu ndi kudzikongoletsa koyenera, makhalidwe ndi zolankhula zanu, ulemu umene mukupereka kwa ana a sukulu anzanu komanso aphunzitsi, mmene mukukhozera m’kalasi, ndiponso kuona kuti muli ndi moyo wabwino, angakufunseni kuti, “N’chifukwa chiyani uli wosiyana kwambiri ndi ena?” (Mal. 3:18; Yoh. 15:19) Zimenezi zingakupatseni mwayi wolalikira ndi kufotokoza zimene mumakhulupirira. (1 Tim. 2:9, 10) M’chaka chonse, mungakumane ndi zinthu monga miyambo yosonyeza kukonda dziko lanu ndiponso maholide ena a dziko. Mukadzafunsidwa chifukwa chake simuchita nawo zimenezi, kodi mudzangoyankha kuti, “Ndine wa Mboni za Yehova, ndipo chipembedzo changa sichiloleza zimenezo,” kapena kodi mudzapezerapo mwayi wochitira umboni za Atate wanu wachikondi, Yehova? Kukonzekera bwino potsatira malangizo a Yehova kudzakuthandizani kuchitira umboni bwino kwambiri kwa aphunzitsi anu, ophunzira anzanu ndiponso anthu ena.—1 Pet. 3:15.
4. N’chifukwa chiyani mukuona kuti mungathe kulalikira kusukulu?
4 Mwina muli ndi mantha pang’ono mukaganiza za mavuto a kusukulu, koma dziwani kuti pali ambiri amene ndi okonzeka kukuthandizani kuti zinthu zikakuyendereni bwino. Ndiponso tikusangalala nanu chifukwa tikuyembekezera kuti mukachitira umboni kwa ena m’gawo lanu la kusukulu. Choncho, khalani wolimba mtima ndiponso wokonzeka kukalalikira kusukulu.