Ndandanda ya Mlungu wa August 17
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 17
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 24, ndime 1-10
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 10-13
Na. 1: Numeri 13:17-33
Na. 2: Zimene Zingatithandize Kuthetsa Mantha (lr-CN mutu 30)
Na. 3: Kodi Lemba la 1 Petulo 3:19, 20 Limatanthauza Chiyani? (rs-CN tsa. 205, ndime 2)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.15: Kulalikira Nyumba ndi Nyumba. Nkhani yokambirana ndi omvetsera kuchokera m’buku la Gulu, tsamba 92, ndime 3 mpaka tsamba 95, ndime 2. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene amalalikira ku nyumba ndi nyumba ngakhale kuti ali ndi mavuto amene angawalepheretse kutero, monga kudwaladwala kapena manyazi. Kodi apeza madalitso otani chifukwa cha khama lawo?
Mph.15: “Kodi Mwakonzekera Kukalalikira Kusukulu?” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani wachinyamata mmodzi kapena awiri amene analalikirapo kusukulu. Kodi chinawathandiza n’chiyani? Apempheni kuti afotokoze mmene zinachitikira.