Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/98 tsamba 1
  • Achinyamata—Gwiritsirani Ntchito Mwayi Wokhala Pasukulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata—Gwiritsirani Ntchito Mwayi Wokhala Pasukulu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera Kukalalikira Kusukulu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
  • Musalephere Kulalikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 8/98 tsamba 1

Achinyamata—Gwiritsirani Ntchito Mwayi Wokhala Pasukulu

1 Kodi mumamva bwanji ngati mukupitanso kusukulu maholide atatha? Kodi mumafunitsitsa kukapindula kusukulu m’chaka china? Kodi mudzagwiritsira ntchito mwayi umene mumakhala nawo pasukulu kuuzako anzanu a pasukulupo ndi aphunzitsi anu choonadi? Tili ndi chidaliro kuti mumafuna kuchita bwino kwambiri pasukulu.

2 Khalani Wophunzira Wabwino: Ngati mukonzekera bwino pamene mukukaloŵa m’kalasi ndi kumamvetsera mwatcheru, mudzapeza mapindu osatha. Khalani wakhama kuchita homuweki yomwe mwapatsidwa, koma musamalole kuti zochita zanu za kusukulu zizisokoneza zochita zateokrase.—Afil. 1:10.

3 Yambani temu yasukulu yatsopano mwa kuŵerenga brosha la Mboni za Yehova ndi Maphunziro. Ndiyeno inuyo kapena makolo anu akapatse aphunzitsi anu onse kope limodzilimodzi la broshali. Adziŵitseni kuti mafunso alionse amene angakhale nawo adzayankhidwa. Zidzawathandiza kumvetsetsa zochita zanu ndi zikhulupiriro zanu ndipo adzagwirizana nanu pamene mukutsatira zimene munaphunzira. Aphunzitsi anu adzakhalanso otsimikizira kuti inu pamodzi ndi makolo anu muli ofunitsitsa kugwirizana nawo pamene akukuthandizani kupeza maphunziro ofunika kwambiri.

4 Khalani Mboni Yabwino: Bwanji osaona pasukulu ngati gawo lanu lochitirapo umboni wamwamwayi? M’chaka chikudzachi, mudzakhala ndi mwayi wapadera wochitira umboni. Muli ndi chidziŵitso chauzimu chodabwitsa chimene ngati mutauzako ena, ‘mungadzipulumutse inu nokha ndi iwo akumva inu.’ (1 Tim. 4:16) Mwa kukhalabe ndi khalidwe lachikristu lachitsanzo ndi mwa kuchitira umboni nthaŵi iliyonse pamene kuli koyenera, mudzapindula inu ndi anthu enanso.

5 Mbale wina wachinyamata anachitira umboni mwamwayi kwa anzake a pasukulu yawo. Ena mwa amene anamvetsera anali Mkatolika, wosakhulupirira Mulungu amene ankakonda kuseka anthu amene amakhulupirira Mulungu, ndi mnyamata wina amene anali wosuta fodya kwambiri ndiponso chidakwa. Mbale wachinyamatayu anathandiza mabwenzi ake 15 onse pamodzi kuti adzipatulire ndi kubatizidwa!

6 Achinyamata, dziperekenitu kuti muphunzire ndi kuti muchitire umboni m’gawo lanu lapaderalo. Mwakutero mudzapeza mapindu ochuluka pakupita kusukulu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena