Musalephere Kulalikira
1. Kodi pamafunika kulimba mtima kuti tichite chiyani ndipo n’chifukwa chiyani?
1 Kodi nthawi ina munalepherapo kulalikira kusukulu chifukwa chochita mantha kuti mwina anzanu akusekani? Kunena zoona, pamafunika kulimba mtima kuti mulalikire, makamaka ngati ndinu wamanyazi. Kodi chingakuthandizeni n’chiyani?
2. Pa nkhani yolalikira kusukulu, kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu wosamala?
2 Muzikhala Osamala Kwambiri: Ngakhale kuti kusukulu angakhale malo abwino kwambiri kulalikirako, muzikumbukira kuti n’zosatheka kukambirana zinthu zauzimu ndi munthu aliyense ngati mmene mungachitire mukamalalikira nyumba ndi nyumba. Choncho, muzikhala osamala kwambiri mukamafuna kulankhula. (Mlal. 3:1, 7) Nkhani imene mukuphunzira m’kalasi kapena zimene akuuzani kuti muchite kusukulu zikhoza kukupatsani mwayi wofotokoza zimene mumakhulupirira. Kapena mnzanu wa m’kalasi angakufunseni chifukwa chimene simuchitira nawo zinthu zina. Akhristu ena amadziwitsa aphunzitsi awo akangotsegulira sukulu kuti iwowo ndi a Mboni za Yehova ndipo amapatsanso aphunzitsiwo mabuku ofotokoza zimene timakhulupirira. Ena amaika dala mabuku poonekera kuti anzawo akusukuluko akaona afunse mafunso.
3. Kodi mungakonzekere bwanji kulalikira kusukulu?
3 Muzikhala Okonzeka: Mukakonzekera, simuchita mantha kuyamba kulalikira. (1 Pet. 3:15) Choncho, muziganizira za mafunso amene mungafunsidwe ndiponso mmene mungayankhire. (Miy. 15:28) Ngati zingatheke, muzitenga m’chikwama chanu mabuku ochepa monga la Kukambitsirana, Zimene Achinyamata Amadzifunsa ndi mabuku ena amene amafotokoza za kulengedwa kwa zinthu kuti muwagwiritse ntchito akafunika. Muzipemphanso makolo anu kuti pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, muziyeserera mmene mungalalikire anzanu kusukulu.
4. N’chifukwa chiyani muyenera kupitirizabe kulalikira kusukulu?
4 Muzikhala ndi Maganizo Abwino: Musamaganize kuti nthawi zonse anzanu a kusukulu adzakusekani mukamawauza choonadi. Mosakayikira, ena adzakusirirani chifukwa cha kulimba mtima ndipo adzamvetsera. Koma musagwe mphwayi ngati palibe amene akuchita chidwi. Yehova adzasangalala kuona kuti mwachita zimene mukanatha. (Aheb. 13:15, 16) Pitirizani kumupempha kuti akuthandizeni ‘kupitiriza kulankhula molimba mtima.’ (Mac. 4:29; 2 Tim. 1:7, 8) Taganizirani mmene mungasangalalire ngati wina atasonyeza chidwi ndi uthenga wanu. Munthu ameneyo akhozatu kudzakhala mtumiki mnzathu wa Yehova.