Kodi Ana Anu Akonzekera?
1. N’chifukwa chiyani ana asukulu ayenera kukonzekera zimene akakumane nazo kusukulu?
1 Pangotsala masiku ochepa kuti ana anu atsegulire sukulu ndipo mosakayikira akakumana ndi mavuto ena atsopano. Komanso, anawa akakhala ndi mwayi watsopano ‘wochitira umboni choonadi.’ (Yoh. 18:37) Kodi iwo akonzekera?
2. Kodi ana anu ayenera kudziwa zinthu ziti kuti akhale okonzekera?
2 Kodi ana anu akudziwa bwino zikondwerero ndi maholide achikunja amene amachitika m’dziko lathuli ndiponso chifukwa chake sayenera kuchita nawo zikondwererozi? Kodi akudziwa zimene anganene ngati wina atawanyengerera kuti achite maphunziro apamwamba, apeze chibwenzi, ayambe kumwa mowa kapena mankhwala osokoneza bongo? Kodi akhoza kungoyankha kuti chipembedzo chawo sichilola kuchita zinthu zimenezi, kapena angafotokoze zimene iwowo amakhulupirira?—1 Pet. 3:15.
3. Kodi makolo angachite chiyani pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kuti akonzekeretse ana awo?
3 Konzekerani pa Kulambira kwa Pabanja: N’zoona kuti pa nthawi yonse imene mwana wanu azipita kusukulu, muzikambirana naye mfundo zina ndi zina mogwirizana ndi mavuto amene akukumana nawo. Komabe, kukambirana nawo mwapadera asanatsegulire sukulu, za mavuto ena amene angakakumane nawo kungawathandize kukhala olimba mtima. Mungachite zimenezi kamodzi kapena kangapo pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Kuti mudziwe nkhani zoyenera kukambirana nawo, mungafunse ana anuwo kuti afotokoze zimene zikuwadetsa nkhawa akaganizira zokayambanso sukulu. Mungabwereze kukambirana nawo nkhani zina zimene munakambirana nawo zaka za m’mbuyomu chifukwa mwina panopo anawo akula ndipo ayamba kumvetsa zinthu. (Sal. 119:95) Mungayeserere zimenezi ndipo inuyo mungayerekezere kuti ndinu mphunzitsi, mlangizi amene amawathandiza pa zamaphunziro apamwamba komanso za ntchito, kapena mungakhale mwana wasukulu. Phunzitsani ana anu mmene angayankhire pogwiritsa ntchito Baibulo ndiponso mabuku ngati la Kukambitsirana ndi la Zimene Achinyamata Amadzifunsa. Mayi wina ankakonda kuyeserera ndi ana ake powakonzekeretsa mmene angakauzire aphunzitsi awo atsopano zoti ndi a Mboni za Yehova akakatsegulira sukulu.
4. Kodi makolo anzeru amachita chiyani pofuna kuthandiza ana awo?
4 Mavuto amene achinyamata achikhristu akukumana nawo akuwonjezeka kwambiri m’masiku otsiriza ano. (2 Tim. 3:1) Makolo anzeru amaganizira za mavuto amene ana awo angakumane nawo ndipo amawakonzekeretsa kupeza njira zothetsera mavutowo. (Miy. 22:3) Choncho, ana anu asanatsegulire sukulu, yesetsani kuwathandiza kuti akhale okonzekera.