Misonkhano Yautumiki ya August
Mlungu Woyambira August 3
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani za lipoti la utumiki wakumunda la May, la dziko ndi la mpingo wanu.
Mph. 15: “Lakalakani Chakudya Chauzimu.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho. Pendani ndi omvetsera mmene malemba ogwidwa mawu angagwirire ntchito.
Mph. 20: “Gwiritsani Ntchito Mabrosha Kuti Mukope Maganizo ndi Mtima Womwe.” Kukambitsirana ndi omvetsera. Pendani mwachidule mabrosha amene afalitsidwa kuti mudziŵitse anthu zinthu za m’Malemba zofunikira. (Onani Watch Tower Publications Index 1986-1995, masamba 652-3.) Longosolani mabrosha aposachedwapa, ndipo kambitsiranani amene angachite chidwi ndi brosha lililonse. Chitirani chitsanzo ulaliki umodzi kapena aŵiri, mukumatchula chopereka cha broshalo.
Nyimbo Na. 191 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 10
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Tchulani za cholinga chakuti ofalitsa onse achite nawo utumiki wakumunda mu August.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: “Achinyamata—Gwiritsirani Ntchito Mwayi wa Kusukulu.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zoyenerera zochokera mu Galamukani! ya April 8, 1992, masamba 17-19, ndi Nsanja ya Olonda ya July 15, 1991, masamba 23-6.
Nyimbo Na. 37 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 17
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Funsani omvetsera kunenapo mwachidule za mmene tingafunsire dzina ndi aderesi ya munthu amene tamulalikira pamsewu, m’paki, kapena kwina kulikonse kuti tikapitirize kukambitsirana naye.
Mph. 35: “Kuona Mmene Ntchito Yamwansanga Yopanga Ophunzira Ikupitira Patsogolo.” Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 5, 10, ndi 11. Pendani mmene ntchito yochititsa maphunziro a Baibulo ikupitira patsogolo pampingo wanu. Limbikitsani onse amene akuchititsa maphunziro kuŵerenganso mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996 kuti awonjezere maluso awo akuphunzitsa. Pendani ndime 5 ndi 25 za mphatika imeneyo.
Nyimbo Na. 108 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 24
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Poti kwatsala mapeto a mlungu umodzi wokha mu August, limbikitsani aliyense kuchita nawo utumiki mweziwu usanathe. Pendani “Programu Yatsopano ya Tsiku Lamsonkhano Wapadera.”
Mph. 18: Mmene Mungalimbikirire Muutumiki Waupainiya. Nkhani yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993 masamba 28-31. Funsani mpainiya amene waphunzira kupirira mavuto akulu ndipo akupitirizabe kuchita upainiya.
Mph. 15: Gwiritsirani ntchito Utumiki Wathu Waufumu moyenerera. Kukambitsirana ndi omvetsera. Mwakugwiritsira ntchito zitsanzo za posachedwapa, sonyezani chidziŵitso chapanthaŵi yake chopezeka mu Utumiki Wathu Waufumu ndi mapindu amene timapezamo: (1) nkhani zimene zimatisonkhezera kuchita nawo utumiki nthaŵi zonse; (2) zokumana nazo zimene zimatilimbikitsa mu utumiki wathu wopatulika; (3) malingaliro amene amatithandiza kulalikira uthenga wabwino mogwira mtima; (4) kulengezedwa kwa mabuku atsopano amene amakhala othandiza m’gawo la mpingo; (5) malipoti autumiki amene amasonyeza mmene ntchito ya Ufumu ikuyendera; (6) Mbiri Yateokrase imene imatidziŵitsa mmene ntchito ya padziko lonseyi ikupitira patsogolo; (7) zilengezo ndi ndandanda zimene zimatidziŵitsa za zomwe zikuchitika; (8) Mabokosi a Mafunso amene amapereka mayankho a nkhani zofunika; ndi (9) mphatika zimene zimatiuza za misonkhano, mikupiti yapadera, ndi nkhani zina kuti tizilingalirabe zosoŵa zathu zauzimu. Limbikitsani onse kuŵerenga kope lililonse, kugwiritsa ntchito malingaliro ake, kubwera nalo ku Misonkhano Yautumiki ndi misonkhano yautumiki wakumunda, nkulisunga mu fayelo yawo kuti adzagwiritsenso ntchito mtsogolo.
Nyimbo Na. 210 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 31
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda a August. Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo aonetsetse kuti aliyense m’kagulu kawo wapereka kotero kuti malipoti onse aloŵetsedwe pofika pa September 6. Pendani chogaŵira cha September. Mwachidule chitirani chitsanzo ulaliki umene ukudzutsa funso lakuti, “Nchifukwa ninji tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu?” Yankhani ndi buku la Chidziŵitso, mutu 3, ndime 6.
Mph. 15: “Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Wotsogoza.” Nkhani ya woyang’anira wotsogoza. Atalongosola ntchito yake, akuyamikira mpingo chifukwa cha kugwirizana ndi akulu pamene akuŵeta nkhosa.
Mph. 18: Thandizani Mwana Wanu Kulimbana ndi Mavuto Kusukulu. Mkulu akukambirana ndi makolo aŵiri kapena atatu amene ali ndi ana kusukulu. Tsirani ndemanga mwachidule pa mavuto ofala amene ana amapezana nawo, monga asonyezedwera mu Galamukani! ya August 8, 1994, masamba 5-7. Ndiyeno, mogwiritsa ntchito masamba 8-10, kambitsiranani mmene makolo angatetezere ana awo ndi kukhalabe ndi unansi wabwino ndi aphunzitsi.
Nyimbo Na. 24 ndi pemphero lomaliza.