Ndandanda ya Mlungu wa August 24
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 24
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 24, ndime 11-21, ndi bokosi, tsa. 249
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Numeri 14-16
Na. 1: Numeri 14:26-43
Na. 2: Kodi Kukonda Chilamulo cha Mulungu Kumatanthauza Chiyani? (Sal. 119:97)
Na. 3: Amene Angatitonthoze (lr-CN mutu 31)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya September. Fotokozani mwachidule zimene zili m’magaziniwo. Pemphani omvera kuti atchule funso limene angafunse kuti ayambitse makambirano komanso lemba limene angawerenge asanagawire magaziniwo. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire magaziniwa.
Mph.20: “Zimene Tingachite Kuti Tizilalikira kwa Amuna Ambiri.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukakambirana ndime 9, funsani mkulu mmodzi kuti afotokoze chimene chinamuthandiza kuyesetsa kuti apeze mwayi wa utumiki mumpingo. Kodi waphunzitsidwa zotani ndipo anaphunzitsidwa ndi ndani?