Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/09 tsamba 3-4
  • Zimene Tingachite Kuti Tizilalikira kwa Amuna Ambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Tingachite Kuti Tizilalikira kwa Amuna Ambiri
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • N’zotheka Kukhala Osangalala M’banja Limene Wina Si Mboni
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Yesetsani Kucheza ndi Anthu Osakhulupirira Amene Akazi Kapena Amuna Awo ndi Mboni
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Choonadi Sichibweretsa “Mtendere Koma Lupanga”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Malangizo Anzeru kwa Okwatirana
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 8/09 tsamba 3-4

Zimene Tingachite Kuti Tizilalikira kwa Amuna Ambiri

1. Kodi pali vuto lotani pankhani yosamalira zinthu za Ufumu?

1 Pamene ntchito ya Ufumu ikupitiriza kuwonjezeka m’masiku otsiriza ano, amuna oyenerera mwauzimu oti azitsogolera mu mpingo ndi ochepa kwambiri. (Maliko 4:30-32; Mac. 20:28; 1 Tim. 3:1-13) Ndipo m’madera ena amuna amene amamvetsera uthenga wa Ufumu ndi ochepa poyerekezera ndi akazi. M’madera enanso amuna amasiyira akazi awo udindo wotsogolera ana pa zinthu zauzimu. Kodi tingatani kuti tithandize amuna ambiri kudziwa zosowa zawo zauzimu ndi kuyamba kulambira nafe Mulungu woona?

2. Kodi khama la Paulo ndi Petulo lolalikira kwa amuna linali ndi zotsatirapo zotani?

2 Khalani ndi Cholinga Cholalikira Amuna Ambiri: Nthawi zambiri mwamuna, yemwe ndi mutu wabanja, akaphunzira choonadi amatha kulimbikitsa ena m’banjamo kuti nawonso ayambe kulambira Mulungu woona. Mwachitsanzo, Paulo ndi Sila atamangidwa chifukwa cholalikira, analalikira mwamuna woyang’anira ndende. Kenako mwamunayo pamodzi ndi onse a m’banja lake anabatizidwa. (Mac. 16:25-34) Nthawi inanso Paulo atalalikira ku Korinto, “Kirisipo, mtsogoleri wa sunagoge, anakhala wokhulupirira mwa Ambuye, pamodzi ndi onse a m’banja lake.” (Mac. 18:8) Yehova anagwiritsira ntchito Petulo kulalikira kwa Koneliyo, yemwe anali kapitawo wa gulu la asilikali ndiponso anali “wopembedza ndi woopa Mulungu.” Koneliyo anabatizidwa limodzi ndi achibale ake komanso mabwenzi ake.—Mac. 10:1-48.

3. Potengera chitsanzo cha Filipo, kodi ndi amuna “apamwamba” ati amene mungawalalikire?

3 Kulalikira amuna “apamwamba,” kapena kuti audindo, kungapindulitse anthu ambiri. (1 Tim. 2:1, 2) Mwachitsanzo, mngelo wa Yehova anauza Filipo kuti alankhule ndi “munthu waulamuliro” amene ankayang’anira chuma chonse cha mfumukazi ya ku Itopiya. Filipo anamva mwamunayu ‘akuwerenga mokweza m’buku la mneneri Yesaya’ ndipo anam’fotokozera uthenga wabwino wonena za Yesu. Mwamuna wa ku Itopiya ameneyu anakhala wophunzira ndipo n’kutheka kuti ankalalikira uthenga wabwino pamene ankabwerera kwawo. N’kuthekanso kuti analalikira mfumukaziyo ndi anthu ena amene ankakhala m’nyumba yake, omwe zikanakhala zovuta kuti akhale ndi mwayi womva uthenga wabwino.—Mac. 8:26-39.

4. Kodi tingatani kuti tithandize amuna ambiri kumva uthenga wabwino?

4 Zimene Mungachite Kuti Mulalikire Amuna Ambiri: Popeza nthawi zambiri amuna amakhala kuntchito, kodi mungakonze ndandanda yanu kuti muzitha nthawi yambiri mu utumiki chigawo chakumadzulo, Loweruka, Lamlungu, kapenanso masiku a holide? Ngati nthawi zambiri tilalikira m’gawo lamalonda, tidzakhala ndi mwayi wolalikira amuna amene kawirikawiri sapezeka pakhomo. Abale nawonso angayesetse kulalikira kwa amuna amene amagwira nawo ntchito. Mu utumiki wa khomo ndi khomo, makamaka m’gawo limene mumalalikira kawirikawiri, abale angathe kupempha kuti alankhule ndi bambo wa pakhomopo.

5. Kodi mlongo ayenera kuchita chiyani akapeza mwamuna amene wachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu?

5 Mlongo akapeza mwamuna wachidwi sayenera kupitakonso ali yekha. Akhoza kupitako ndi mwamuna wake kapena ndi wofalitsa wina. Munthu wachidwiyo akamapita patsogolo, ndi bwino kupereka phunzirolo kwa m’bale woyenerera.

6. Kodi tingatsanzire bwanji mtumwi Paulo kuti ‘tipindule anthu ochuluka koposa’?

6 Sankhani Nkhani Zimene Amuna Amachita Nazo Chidwi: Mtumwi Paulo ankaganizira omvera ake ndipo ankasintha ulaliki wake n’cholinga choti ‘apindule anthu ochuluka koposa.’ (1 Akor. 9:19-23) Ifenso tiyenera kuganizira nkhani zimene zingachititse chidwi amuna amene tingakumane nawo mu utumiki ndiponso tizikonzekera mmene tingalankhulire nawo. Mwachitsanzo, nthawi zambiri amuna amadera nkhawa za mavuto a zachuma, boma labwino, ndiponso mmene angasamalirire ndi kutetezera banja lawo. Angachitenso chidwi kuti adziwe cholinga cha moyo, tsogolo la dzikoli komanso chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Amuna ambiri angalandire uthenga wabwino wa Ufumu ngati tikambirana nawo nkhani zimene iwowo amachita nazo chidwi.—Miy. 16:23.

7. Kodi onse mu mpingo angathandize bwanji amuna osakhulupirira amene amabwera kumisonkhano?

7 Yesetsani Kuthandiza Amuna Osakhulupirira: Ndi zoona kuti khalidwe labwino la alongo athu achikhristu lingakope amuna awo osakhulupirira, komabe anthu onse mu mpingo angathe kuthandiza amuna osakhulupirira amenewa. (1 Pet. 3:1-4) Mwamuna wosakhulupirira akabwera ndi mkazi wake kumisonkhano, kumulandira ndi manja awiri kungakhale kuchitira umboni wogwira mtima. Kubwera kwake kumisonkhano kungakhale chizindikiro choti amachita chidwi ndi choonadi ndipo angalole kuphunzira Baibulo.

8. Kodi abale angathandize bwanji amuna osakhulupirira amene ali ndi chidwi chochepa?

8 Nthawi zina amuna ena amasonyeza chidwi chochepa poyambirira koma m’kupita kwa nthawi angathe kulola kuphunzira Baibulo ndi m’bale amene amamasuka naye. Abale mu mpingo wina anakonza zoti akamachezera banja lina limene mwamuna anali wosakhulupirira, azikambirana ndi mwamunayo nkhani zimene abalewo ankadziwa kuti zimamuchititsa chidwi. Zimenezi zinachititsa kuti m’kupita kwanthawi ayambe kukambirana naye zinthu zauzimu ndipo tsopano mwamunayu ndi m’bale wobatizidwa. M’bale winanso anathandiza mwamuna wosakhulupirira amene anali wochezeka. M’baleyu anathandiza mwamunayu kumanga mpanda wa nyumba yake. Chifukwa chomusonyeza mwamuna ameneyu chidwi mwa njira imeneyi, phunziro la Baibulo linayambika. (Agal. 6:10; Afil. 2:4) Ngati ndinu m’bale wachikhristu, bwanji osayesetsa kuthandiza mwamuna wosakhulupirira mmodzi kapena angapo?

9. Kodi kuthandiza amuna achikhristu kungakhale ndi zotsatirapo zotani?

9 Aphunzitseni Kuti Adzathe Kusamalira Maudindo: Amuna amene amamvetsera uthenga wa Ufumu ndi kuyesetsa kuti apeze maudindo potumikira Yehova, amadzakhala “mphatso za amuna,” kapena kuti akulu achikhristu, amene amagwiritsira ntchito mphamvu zawo ndiponso luso lawo pothandiza mpingo wa anthu a Yehova. (Aef. 4:8; Sal. 68:18) Amuna amenewa amaweta mpingo mofunitsitsa ndiponso modzipereka. (1 Pet. 5:2, 3) Kunena zoona, gulu lonse la abale limapindula chifukwa cha amuna amenewa.

10. Kodi khama la Ananiya pothandiza Paulo lapindulitsa bwanji anthu ambiri?

10 Mwachitsanzo, Saulo anadzakhala “mtumwi weniweni wotumidwa kwa mitundu ina,” ngakhale kuti poyamba ankazunza Akhristu. (Aroma 11:13) Chifukwa cha zimenezi, wophunzira Ananiya poyamba anakayikira zomulalikira Saulo. Komabe, Ananiya anatsatira malangizo a Ambuye ndipo analankhula ndi mwamunayu amene kenako anadzakhala mtumwi Paulo. Kwa zaka zambiri Paulo anathandiza anthu ambiri amene anamumva akulalikira ndipo makalata ake ouziridwa opezeka m’Mawu a Mulungu akupitirizabe kuthandiza anthu ambirimbiri masiku ano.—Mac. 9:3-19; 2 Tim. 3:16, 17.

11. N’chifukwa chiyani tifunika kuchita zilizonse zomwe tingathe kuti tilalikire amuna ambiri?

11 Choncho, tiyeni tiyesetse kuchita chilichonse chotheka kuti tilalikire kwa amuna ambiri. Pamene tikuyesetsa kukwaniritsa cholinga chimenechi, tikukhulupirira kuti Yehova adalitsa khama lathu kuti zinthu ziyende bwino ndipo apititsa patsogolo ntchito ya Ufumu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena