MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mumapindula ndi Kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku?
Kodi muli ndi pulogalamu yowerenga lemba ndi ndemanga kuchokera m’kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku? Ngati sichoncho, muyenera kuyesetsa kumachita zimenezi. Ambiri amasankha kupanga lemba la tsiku m’mawa. Zimenezi zimathandiza kuti aziganizira mfundo za lembalo tsiku lonse. (Yos. 1:8; Sal. 119:97) Kodi mungatani kuti muzipindula kwambiri ndi lemba la tsiku? Mungachite bwino kuwerenga vesilo m’Baibulo kuti mumvetse nkhani yake. Ganizirani nkhani ya m’Baibulo yomwe ikufotokoza bwino mfundo ya mulembalo. Kenako onani mmene mungaigwiritsire ntchito. Mukamalola kuti mawu a Mulungu azikutsogolerani posankha zochita, mudzapindula kwambiri.—Sal. 119:105.
Anthu otumikira pa Beteli padziko lonse amakambirana lemba la tsiku pa nthawi ya chakudya cham’mawa. Zaka zaposachedwapa, zambiri mwa mfundo zimene amakambirana pa lemba la tsiku zakhala zikuikidwa pa JW Broadcasting,® pambali yakuti MAPULOGALAMU KOMANSO ZOCHITIKA ZINA. Kodi ndi liti limene munaonera imodzi mwa mapulogalamu amenewa? Nkhani zake zingakulimbikitseni kwambiri. Mwachitsanzo, kodi nkhani ya Loti ingakuthandizeni bwanji posankha zochita?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUSAMAKONDE DZIKO (1 YOH. 2:15), KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti imene inali maziko a kukambirana pa kulambira kwa m’mawa kumeneku?
Kodi nkhani ya Loti ikutithandiza bwanji kuona kuopsa kokonda dziko kapena zinthu za m’dzikoli?—Gen. 13:12; 14:12; 19:3, 12, 13, 24-26
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova osati dziko kapena zinthu za m’dziko?
Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimaona Mawu a Mulungu kukhala ofunika pa zochita zanga za tsiku lonse?