Misonkhano Yautumiki ya February
Mlungu Woyambira February 6
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Sonyezani mmene nkhani za m’magazini atsopano zingasonyezedwere m’ntchito ya kukhomo ndi khomo.
Mph. 17: “Kulalikira—Mwaŵi Wolemekezeka.” Mafunso ndi mayankho. Perekani ndemanga zowonjezereka zozikidwa mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1990, tsamba 19, ndime 13-16.
Mph. 18: “Kusonyeza Mogwira Mtima Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.” Pendani mfundo zazikulu ndi omvetsera, kuphatikizapo mawu a mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 46-7, ndime 9-12. Fotokozani mtundu wa mawu oyamba amene angakhale ogwira mtima m’gawo lanu. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri.
Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 13
Mph. 5: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti. Tchulani chiyamikiro cha Sosaite cha zopereka zimene zingakhale zitalandiridwa.
Mph. 10: Zosoŵa za pamalopo. Kapena nkhani yakuti “Achichepere Amene ‘Amadalira Yehova,’” ya mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1994, masamba 26-7. Itanani achichepere pa pulatifomu kuti adzasimbe zokumana nazo za m’magaziniwa. (Akhoza kuphatikizamo zofanana nazo za kumaloko, ngati zilipo.) Gogomezerani mbali yofunika ya makolo ya kupanga ana kukhala ophunzira enieni.
Mph. 15: “Mawu a Ufumu—Kupeza Lingaliro Lake.” Mafunso ndi mayankho. Itanani anthu aŵiri kapena atatu kudzasimba mmene ndi pamene amakonzekera kuchita phunziro lawo laumwini kapena kupenda lemba latsiku.
Mph. 15: “Lingalirani za Ena—Mbali 2.” Nkhani ndi kukambitsirana kochitidwa ndi mkulu. Tchulani za vuto lililonse limene laonedwa m’malowo, ndipo perekani chilangizo choyenera.
Nyimbo Na. 109 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 20
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Tchulani nkhani zatsopano za m’magazini zimene zili zoyenerera gawo la kumaloko. Sonyezani maulaliki ake.
Mph. 15: Nkhani yolimbikitsa yoperekedwa ndi mlembi yozikidwa mu mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa December 1993 tsamba 4. Mungawonjezere mfundo zina kuchokera m’buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa, masamba 91-2. Gogomezerani kufunika kwakuti onse adziŵe kuti kupereka lipoti kuli thayo la wofalitsa aliyense, motero palibe kufunika kwa kuyembekezera chikumbutso. Akulu amachita bwino kuika bokosi la malipoti pa Nyumba Yaufumu. Pendani Lipoti Lautumiki la October ndipo tchulani za malipoti osoŵa. Gwiritsirani ntchito mphindi zisanu zotsiriza kukambitsirana ndi woyang’anira utumiki za lipoti lautumiki wakumunda la mpingo la October. Yamikirani abale kaamba ka zimene zinachitidwa. Sonyezani mbali zofuna kuwongolera.
Mph. 18: “Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Simbani za mawu oyamikira chifukwa cha kulandira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. (Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1986, tsamba 32, ndi Nsanja ya Olonda ya December 1, 1990, tsamba 32.) Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri mwachidule zosonyeza mmene maulaliki osonyezedwawo angagwiritsiridwire ntchito. Limbikitsani onse kuyesayesa kuyamba maphunziro ndi okondwerera.
Nyimbo Na. 147 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 27
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Kambitsiranani nkhani yakuti “Kupindula ndi Nkhani Zapoyera Zokonzedwanso.”
Mph. 20: “Kuŵeta Komangirira.” Nkhani yoperekedwa ndi mkulu yozikidwa pa mfundo za pamutu waung’ono wa kope la Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, pamasamba 21-3. Fotokozani uphungu wa Malemba wothandiza kulimbana ndi mavuto.
Mph. 15: Kugaŵira buku la Achichepere Akufunsa m’March. Limbikitsani aliyense kukhala wokondwera kuligaŵira. Fotokozani mwachidule zigawo khumi za bukuli. Lingalirani za mitu ingapo yosankhidwa. Sonyezani zithunzithunzi zamphamvu, zonga chimene chili patsamba 27. Limbikitsani achichepere, makolo ndi ena kulingalira za uphungu wa panthaŵi yake wa bukuli. Kumbutsani onse kupeza makope okawagwiritsira ntchito mu utumiki kutha kwa mlungu uno.
Nyimbo Na. 207 ndi pemphero lomaliza.