Nyimbo 134
‘Chitani Monga Amuna’
1. ‘Ona mwamuna!’ ati Pilato.
Ndithu Yesu ndi chitsanzo chabwino!
Ndi kulimba mtima analaka
Dziko la Satana la udanili.
2. Yesu anakhazika chitsanzo.
Tikhale monga mmene analiri.
Poyang’anana ndi Armagedo,
Tilimbe mtimatu; monga amuna.
3. Kulimba kuli kofunikadi
Kwa okhulupirika onse a Ya.
Pomwe mapeto ayandikira,
Tilimbebe mu ntchito ya Ufumu.
4. Atumiki onse a Yehova,
Amayang’ana kwa Yesu Mfumuyo.
Mosawopa khalani amphamvu.
Nyimbo yolakika adzaiimba.