Nyimbo 147
Chuma Chosalephera
1. Tate wakumwamba, tikuthokoza
Kuti tadziŵa cho’nadi!
Ndimwaŵi kulengeza za
Ufumu Ndi kuti uli pafupi!
2. Nzeru, chilungamo, mphamvu, chikondi
Zimasonkhezera mtima.
Kukhala ndi Yesu Mpulumutsiyo,
Kumatipatsa chimwemwe.
3. Ubwenzi wathu nanu ndidalitso.
Tingakhumbenso chiyani?
Chifundo chanu chipatsa mtendere
Umenedi timafuna.
4. Tiri ndi chifukwa choyamikira;
Mawuwo adzapambana.
Mupatsa chiyanjo kwa okondedwa.
Ndi chuma chosalephera.