Lingalirani za Ena—mbali 2
1 Malinga ndi kuthekera kwake, tikufuna kusunga unansi wabwino ndi anthu okhala m’chitaganya chathu. Zimenezi zimafuna kuti tisonyeze mkhalidwe wa kulingalira ena ndi kulemekeza zoyenera zawo ndi malingaliro awo.
2 Mboni za Yehova zimadziŵidwa kaamba ka makhalidwe abwino. Makhalidwe athu abwino m’chitaganya, pasukulu, ndi kumalo antchito, limodzinso ndi pamisonkhano yathu, athokozedwa ndi ambiri.—Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1989, tsamba 20.
3 Ndithudi, kudzisungira kwabwino kumaphatikizapo zinthu zambiri, zonga kuona mtima, khama, ndi makhalidwe abwino. Kumaphatikizaponso kukhala waulemu kwa anthu okhala m’malo apafupi ndi Nyumba Yathu Yaufumu. Kudzisungira kwathu kwaumulungu m’mbali zina kunganyalanyazidwe ngati tilephera kulingalira za anansi athu. Paulo anatilangiza ‘kuyenda moyenera mbiri yabwino.’—Afil. 1:27.
4 Nthaŵi ndi nthaŵi, okhala pafupi ndi Nyumba Zaufumu adandaula chifukwa cha zimene amaona kukhala kusalingalira ena kwa awo ofika pamisonkhano. Abale ndi alongo ayenera kupeŵa kusokhana m’njira yodutsa pa Nyumba Yaufumu akumakambitsirana mokweza mawu amene angamvedwe ndi a m’nyumba zapafupi. Ana sayenera kuloledwa kuthamangathamanga akumaloŵa ndi kutuluka mu Nyumba Yaufumu. Kutseka zitseko za galimoto mwamphamvu kwambiri kapena kuliza huta kosasamala kungasokoneze okhala pafupiwo. Khalidwe la mtundu umenewu limapereka chithunzi choipa cha mpingo.
5 Galimoto siziyenera kuikidwa pamalo a eni kapena pamene zingatsekereze galimoto zina kapena kuzichingira njira. Malo osungirapo galimoto osamaliridwa ndi magulu abizinesi apafupi olinganizidwira makasitomala awo sayenera kugwiritsiridwa ntchito pokhapo ngati chilolezo chaperekedwa. Kumene mipingo itatu kapena inayi imagwiritsira ntchito Nyumba Yaufumu imodzi, misonkhano imandandalikidwa pafupifupi tsiku lililonse la mlungu, ndipo zimenezi zimafuna kugwirizana kwambiri kwa mabungwe a akulu.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 1988, tsamba 17, ndime 13.
6 Baibulo limatisonkhezera ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu,’ ndipo zimenezo zimaphatikizapo kusonyeza mkhalidwe wolingalira za akunja. (1 Akor. 10:31-33) Ngati ‘tipenyerera za ena,’ sitidzangoloŵa mopanda ulemu pamalo a eni. (Afil. 2:4) Tidzapeŵanso kuloŵerera m’zochitika za eni malonda a kumalo kwathu.
7 Kulingalira za ena—mkati ndi kunja komwe kwa mpingo—ndiko chisonyezero chakunja cha mmene timamvera m’mitima mwathu. Zimene timachita ndi kunena ziyenera kusonyeza kuti ‘timakonda anansi athu monga ife eni.’—Mat. 7:12; 22:39.