Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/95 tsamba 3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 2/95 tsamba 3

Zilengezo

◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu February: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Bukuli litagaŵiridwa payenera kukhala maulendo obwereza, ndipo muyenera kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo. March: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. April ndi May: Mkupiti wa sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda.

◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki ayenera kupenda ntchito za apainiya okhazikika onse. Ngati pali aliyense amene akukhala ndi vuto la kufitsa chofunika cha maola, akulu ayenera kulinganiza kuti chithandizo chiperekedwe. Kuti mupeze malingaliro, pendani makalata a Sosaite a (S-201) October 1, 1993, ndi November 1, 1992. Ndiponso, onani ndime 12-20 za mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa October 1986.

◼ Phwando la Chikumbutso lidzachitidwa pa Lachisanu, April 14, 1995. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumirapo, chonde kumbukirani kuti kuperekedwa kwa mkate ndi vinyo wa Chikumbutso sikuyenera kuyamba kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsani odziŵa zanyengo akumaloko za nthaŵi yeniyeni pamene dzuŵa limaloŵa kwanuko. Palibe misonkhano iliyonse imene iyenera kuchitidwa tsiku limenelo kusiyapo kukumana kwa utumiki wakumunda. Ngati mpingo wanu umakhala ndi misonkhano pa Lachisanu, mungaisinthire patsiku lina la mlunguwo ngati Nyumba Yaufumu ingakhale yomasuka. Akulu akukumbutsidwa kuyambirira kufunafuna vinyo woyenera.—Onani tsamba 2 la Utumiki Wathu Waufumu wa March 1994.

◼ Ofalitsa amene akufuna kutumikira monga apainiya othandiza m’March, April, ndi May ayenera kupanga makonzedwe awo tsopano lino ndi kupereka mwamsanga chofunsirapo chawo. Izi zidzathandiza akulu kupanga makonzedwe a utumiki wakumunda oyenera ndi kukhala ndi mabuku okwanira.

◼ Tikufuna kulimbikitsa onse kupanga kuyesayesa kwapadera kwa kuitanira awo amene adzapezeka pa Chikumbutso ku nkhani yapoyera yapadera imene idzakambidwa pambuyo pa mlungu umodzi. Chidziŵitso chimene chidzaperekedwa pambuyo pake pamsonkhanowo patsiku limenelo chidzasonkhezera iwo ndi abale athu onse kuyembekezera kukhala ndi phande m’kugaŵira trakiti lapadera. Panthaŵi imodzimodziyo, chidzatchula za mavuto amene anthu akukumana nawo ndi kufunika kwa kuchitapo kanthu motsimikiza mogwirizana ndi Mawu a Mulungu.

◼ Zofalitsidwa Zomwe Zilipo:

Chicheŵa: Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Chingelezi: Imbirani Yehova Zitamando (Lalikulu). Chipwitikizi: Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. French: Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira; Mabaundi voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 1993.

◼ Makaseti Amene Alipo:

Chingelezi: Alubamu ya Malemba Achigiriki onse; Alubamu ya Malemba Achihebri—Voliyumu 2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena