Nyimbo 184
Abusa Achikondi Ayang’anira “Nkhosa”
1. Ambuye tikuthokoza,
Muli Mbusa wamkulu.
Mutisunga mwachikondi.
Mutetezera “nkhosa.”
2. Yesu anapatsa ’busa
Amatidera nkhaŵa.
Adzipereka muntchito,
Kuphunzitsa cho’nadi.
3. Abusa a gulu la Ya,
Mufunire ubwino.
Mulithandize kukula,
Kuti liwonjezeke.
4. Polalikira pamodzi,
Timalimbikitsidwa!
Tidzatumikira M’lungu,
Ndi kusonyeza changu.