Amaŵeta Nkhosa Mwachifundo
PA NYAMA zonse zokhala pafupi ndi anthu, palibe zilizonse zofanana ndi nkhosa yoŵeta. Nyama zochuluka zili ndi nyonga ndi nzeru zofunikira kufunira chakudya ndi kuthaŵa zinyama zolusa zimene zingazigwire, koma nkhosa njosiyana. Ikhoza kugwidwa mosavuta ndi zinyama zolusa, yosakhoza kwenikweni kudzitetezera. Popanda mbusa, nkhosa imachita mantha ndi kusoŵa chochita. Itachoka pagulu la nkhosa, imasoŵa mosavuta. Chotero nkhosa zofatsa zili ndi zifukwa zazikulu zokondera kwambiri mbusa wawo. Popanda iye zingakhale ndi mpata wochepa wa kupulumuka. Chifukwa cha mikhalidwe imeneyi, Baibulo limagwiritsira ntchito nkhosa mophiphiritsira kusonyeza anthu opanda liŵongo, ochitiridwa nkhanza, kapena opanda chitetezo.
Kunena zowona, mphotho za mbusa nzoyenerera kwambiri. Moyo wake ngwovuta. Amavutika ndi kutentha ndi kuzizira, ndipo samapeza tulo usiku. Ayenera kutetezera gulu la nkhosa ku nyama zolusa, kaŵirikaŵiri akumadziika pachiswe. Popeza kuti mbusa ayenera kusunga nkhosa pamodzi, nthaŵi yake yochuluka imathera pakufunafuna nkhosa zimene zimapatuka kapena kusokera. Ayenera kusamalira zodwala ndi zovulala. Ana a nkhosa ofooka kapena otopa ayenera kunyamulidwa. Pamakhala nkhaŵa yosatha yopeza chakudya chokwanira ndi madzi. Kuli kofala kwa mbusa kugona kunja m’thengo kuti atsimikizire kuti gulu la nkhosalo nlotetezereka. Chotero, ubusa wa nkhosa ndimoyo wovuta wofuna mautumiki a mwamuna amene ali wolimba mtima, wakhama, ndi waluso. Koposa zonse, ayenera kukhala wokhoza kusonyeza nkhaŵa yeniyeni pagulu la nkhosa limene wapatsidwa kulisamalira.
Kuŵeta Gulu la Nkhosa la Mulungu
Baibulo limasonyeza anthu a Mulungu monga nkhosa zofatsa ndipo oyawang’anira monga abusa. Yehova mwiniyo ndiye ‘mbusa ndi woyang’anira wa miyoyo yathu.’ (1 Petro 2:25) Yesu Kristu, “mbusa wabwino,” anasonyeza chikhumbo chake chakuti nkhosa zilandire chisamaliro chachifundo pamene anauza mtumwi Petro kuti: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga, ŵeta nkhosa zanga, dyetsa nkhosa zanga.’ (Yohane 10:11; 21:15-17) Oyang’anira Achikristu alamulidwa mwamphamvu ‘kuŵeta mpingo wa Mulungu.’ (Machitidwe 20:28) Ndipo ntchito yawo monga abusa auzimu imafuna mikhalidwe ya mbusa wabwino weniweni—kulimba mtima, khama, luso, ndipo wofunika koposa, chisamaliro chachikondi cha ubwino wa gulu la nkhosa.
M’masiku a Ezekieli mneneri wa Mulungu, unyinji wa abusa oikidwa kusamalira zosoŵa za anthu a Yehova m’Israyeli analephera kukwaniritsa ntchito zawo. Gulu la nkhosa la Mulungu linavutika kwambiri, zambiri zikumasiya kulambira kowona. (Ezekieli 34:1-10) Lerolino, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu amadzisonyeza kukhala abusa a wolingaliridwa kukhala mpingo Wachikristu, koma mkhalidwe wake wautenda wauzimu umasonyeza kuti atsogoleri achipembedzo ali ngati onyenga oipa amene ananyalanyaza ndi kupondereza anthu pamene Yesu anali padziko lapansi. Atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ali ngati munthu “wolipidwa” amene “sasamala nkhosa.” (Yohane 10:12, 13) Iwo sali ofunitsitsa, okhoza, kapena oyenerera konse kuŵeta gulu la nkhosa la Mulungu.
Abusa Amene Amasamaladi
Yesu anapereka chitsanzo changwiro kwa onse amene akaŵeta gulu la nkhosa la Yehova. Mwanjira iliyonse anali wachikondi, wokoma mtima, wachifundo, ndi wothandiza kwa ophunzira ake. Anadziyambira yekha kufunafuna osoŵa. Ngakhale kuti Yesu anali wotanganitsidwa ndi wotopa kaŵirikaŵiri, iye anapatula nthaŵi ya kumvetsera mavuto awo ndi kuwapatsa chilimbikitso. Kufunitsitsa kwake kupereka moyo wake m’malo mwawo kunali chisonyezero chachikulu koposa cha chikondicho.—Yohane 15:13.
Lerolino, akulu onse oikidwa mumpingo, limodzinso ndi atumiki otumikira, ali ndi thayo limeneli pagulu la nkhosa. Chotero, ngakhale mapindu akuthupi amene angakhale otheka m’dziko lina samasonkhezera unyinji wa amuna athayo ameneŵa kusamuka ndipo motero kusiya mipingo yopanda chithandizo ndi uyang’aniro wokwanira. Pokhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa,” gulu la nkhosa limafunikira chilimbikitso ndi chitsogozo. (2 Timoteo 3:1-5) Pali upandu wosatha wakuti ena angagwidwe ndi Satana, amene ali “monga mkango wobuma, [wo]yendayenda kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Lerolino kuposa ndi kalelonse, kuli kofunika kwambiri kwa abusa Achikristu ‘kuyambirira amphwayi, kulimbikitsa amantha mtima, kuchilikiza ofooka.’ (1 Atesalonika 5:14) Kugalamuka kosalekeza nkofunika ngati ati aletse opupuluma kugwa kuchoka pagulu la nkhosa.—1 Timoteo 4:1.
Kodi mbusa angadziŵe motani pamene nkhosa ifunikira chithandizo? Zina za zizindikiro zosavuta kuona ndizo kulephera kufika pamisonkhano Yachikristu, kukhala wosakhazikika muutumiki wakumunda, ndi chizoloŵezi cha kupeŵa kuyanjana kwambiri ndi ena. Zifooko zingapezedwenso mwakuona mosamalitsa mkhalidwe wa maganizo wa nkhosa ndi kumene makambitsirano awo amakhoterera. Iwo angakhale okhoterera pakusuliza ena, mwinamwake kusonyeza malingaliro akuipidwa. Makambitsirano awo angazikidwe kwakukulukulu pazolondola zakuthupi mmalo mwa zonulirapo zauzimu. Kusoŵa chikondwerero, chiyembekezo, ndi chisangalalo kungatanthauze kuti chikhulupiriro chawo chakhala chofooka. Nkhope yakugwa ingakhale chizindikiro chakuti iwo akutsenderezedwa ndi achibale otsutsa kapena mabwenzi akudziko. Poona zizindikiro zimenezi, mbusa angafunefune mwamphamvu kupeza mtundu wa chithandizo chimene chikufunika.
Paulendo wothandiza wokhulupirira mnzawo, abusa Achikristu ayenera kukumbukira cholinga chawo chachikulu. Suli chabe ulendo wocheza wokhala ndi makambitsirano a zinthu wamba. Chonulirapo cha mtumwi Paulo pochezera abale ake chinali ‘kuwagaŵira mtulo wina wauzimu kuti iwo akakhazikike ndi kuti akatonthozane.’ (Aroma 1:11, 12) Kuti zimenezi zichitidwe, pafunikira kukonzekera pasadakhale.
Choyamba, pendani munthuyo, ndipo yesani kudziŵa mkhalidwe wake wauzimu. Mutachita zimenezo, lingalirani za mtundu wa chitsogozo, chilimbikitso, kapena uphungu umene udzakhala wopindulitsa kwambiri. Mawu a Mulungu, Baibulo, ayenera kukhala magwero aakulu a chidziŵitso chifukwa “amapereka mphamvu.” (Ahebri 4:12, NW) Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! angafufuzidwe kufuna nkhani zimene zikufotokoza zosoŵa zakutizakuti za nkhosa zokhala ndi mavuto apadera. Zokumana nazo zosangalatsa ndi zotsitsimula zingapezedwe mu Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Chonulirapo ndicho kugaŵira kanthu kena kauzimu kamene kadzakhala ‘kabwino, kakumlimbikitsa.’—Aroma 15:2.
Kuŵeta Komangirira
Mbusa wa gulu la nkhosa zenizeni amadziŵa kuti zimamdalira kuti azitetezere ndi kuzisamalira. Maupandu ofala kwambiri ndiwo kusokera, utenda, kutopa, kuvulala, ndi zinyama zolusa. Mofananamo mbusa wauzimu ayenera kuzindikira ndi kuchita ndi maupandu ofanana amene amaopseza ubwino wa gulu la nkhosa. Otsatirawa ndiwo ena a mavuto odziŵika ndi malingaliro angapo amene anganenedwe pogaŵira chidziŵitso chomangirira mwauzimu.
(1) Mofanana ndi nkhosa zosakhala zatcheru, Akristu ena asokera kuchoka m’gulu la nkhosa la Mulungu chifukwa anyengeka ndi zinthu zooneka kukhala zabwino ndi zokopa zosangalatsa. Iwo angachenjeneketsedwe ndipo angatengekedi chifukwa cha kulondola zonulirapo zogwirizana ndi kukondetsa zinthu zakuthupi, maseŵera, kapena zosangulutsa. (Ahebri 2:1) Anthu otero angakumbutsidwe za kufulumira kwa nthaŵi, kufunikira kwa kukhala pafupi ndi gulu la Yehova, ndi za kufunika kwa kuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo. (Mateyu 6:25-33; Luka 21:34-36; 1 Timoteo 6:8-10) Uphungu wothandiza uli m’nkhani yakuti “Sungani Uchikatikati Wanu—Motani?” mu The Watchtower ya May 15, 1984, pamasamba 8-11.
(2) Mbusa afunikira kupereka mankhwala kwa nkhosa zimene zimadwala. Mofananamo, abusa auzimu ayenera kuthandiza Akristu amene amadwala mwauzimu chifukwa cha zinthu zovutitsa m’moyo wawo. (Yakobo 5:14, 15) Iwo angakhale osoŵa ntchito, angakhale ndi matenda aakulu akuthupi, kapena angakhale ndi mavuto m’moyo wawo wa banja. Anthu otero angakhale ndi njala yochepa ya chakudya chauzimu kapena ya kuyanjana ndi anthu a Mulungu. Ndiyeno zimenezi zimachititsa kudzipatula ndi kulefulidwa. Afunikira kulimbikitsidwa kuti Yehova amawasamalira ndi kuti adzawachilikiza m’nthaŵi zonse zovuta. (Salmo 55:22; Mateyu 18:12-14; 2 Akorinto 4:16-18; 1 Petro 1:6, 7; 5:6, 7) Kungakhalenso kothandiza kupendanso nkhani yakuti “Yang’anani Molunjika Patsogolo Monga Mkristu,” yopezeka mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1980, pamasamba 10-14.
(3) Mbusa ayenera kukhala watcheru ponena za nkhosa zimene zimatopa. Ena apirira mokhulupirika muutumiki wa Yehova kwa zaka zambiri. Iwo amenya nkhondo kupyola m’mayesero ndi ziyeso zambiri. Tsopano akusonyeza zizindikiro za kukhala otopa pakuchita zabwino ndipo angasonyezenso zikayikiro ponena za kufunikira kwa ntchito yakulalikira mwachangu. Kuli kofunika kudzutsanso mzimu wawo, kudzutsanso chiyamikiro chawo cha chimwemwe ndi madalitso amene amatuluka m’kuchita utumiki wa mtima wonse kwa Mulungu motsanzira Yesu Kristu. (Agalatiya 6:9, 10 Ahebri 12:1-3) Mwinamwake angathandizidwe kuona kuti Yehova amayamikira utumiki wawo wokhulupirika ndi kuti angawalimbitse kaamba ka ntchito za mtsogolo kuchitamando chake. (Yesaya 40:29, 30; Ahebri 6:10-12) Kungakhale kopindulitsa kukambitsirana malingaliro a m’nkhani yakuti “Musaleme Pakuchita Zabwino,” yopezeka mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1988, pamasamba 9-14.
(4) Mofanana ndi nkhosa zimene zimavulala, Akristu ena avulazidwa ndi zimene amayesa kukhala mkhalidwe wokhumudwitsa. Komabe, ngati timakhululukira ena, Atate wathu wakumwamba adzatikhululukira monga momwe kufunikira. (Akolose 3:12-14; 1 Petro 4:8) Abale kapena alongo ena angakhale atalandira uphungu kapena chilango chimene m’kuganiza kwawo chinali chosayenera. Komabe, tonsefe tingapindule ndi uphungu ndi chilango chauzimu, ndipo nkotonthoza kudziŵa kuti Yehova amalanga amene amawakonda. (Ahebri 12:4-11) Chifukwa chakuti sanapatsidwe mathayo autumiki amene aganiza kuti ali owayenerera, ena alola kuipidwa kuwachititsa kulekana ndi mpingo. Koma ngati tidzilekanitsa ndi gulu la Yehova, kulibe malo ena kumene tingapite kaamba ka chipulumutso ndi chimwemwe chowona. (Yerekezerani ndi Yohane 6:66-69.) Chidziŵitso chothandiza pankhani imeneyi chingapezeke m’nkhani yakuti “Kusungirira Umodzi Wathu Wachikristu,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1988, pamasamba 28-30.
(5) Nkhosa ziyenera kutetezeredwa kuzinyama zolusa. Mwanjira yofanana, ena angatsutsidwe ndi kuopsezedwa ndi achibale ndi antchito anzawo osakhulupirira. Umphumphu wawo ungaukiridwe pamene zitsenderezo ziikidwa pa iwo kuwachititsa kuchepetsa utumiki wawo kwa Mulungu kapena kusiya kukhala ndi phande muutumiki Wachikristu. Komabe, iwo amalimbitsidwa pamene athandizidwa kuzindikira kuti tiyenera kuyembekezera chitsutso ndi kuti chilidi chimodzi cha maumboni akuti ndife ophunzira enieni a Yesu Kristu. (Mateyu 5:11, 12; 10:32-39; 24:9; 2 Timoteo 3:12) Kungakhale kopindulitsa kutchula kuti ngati akhala okhulupirika, Yehova sadzawasiya konse ndipo adzawafupa pachipiriro chawo. (2 Akorinto 4:7-9; Yakobo 1:2-4, 12; 1 Petro 5:8-10) Nkhani ya mutu wakuti “Kupirira Mosangalala Mosasamala Kanthu za Chizunzo” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1982, pamasamba 19-27, imapereka chilimbikitso chowonjezereka.
Abusa—Kwaniritsani Mathayo Anu
Zosoŵa za gulu la nkhosa la Mulungu nzambiri, ndipo uyang’aniro woyenera ndintchito yovuta. Chotero abusa Achikristu ayenera kukhala achifundo, osamaliradi, ndi okonda kuthandiza. Kuleza mtima ndi luntha nzofunika kwambiri. Pamene kuli kwakuti anthu ena amafunikira uphungu ndi chidzudzulo, ena amapindula kwambiri ndi chilimbikitso. Maulendo okaonana ndi munthu mwiniyo angakhale okwanira pazochitika zina, pamene ena angafunikire phunziro la Baibulo lokhazikika. Pachochitika chilichonse chonulirapo chachikulu ndicho kupereka chitsogozo chomangirira mwauzimu kapena uphungu wachikondi umene udzasonkhezera munthuyo kuyambitsa zizoloŵezi zabwino za phunziro, kukhala wokhazikika kapena kupitirizabe kupezeka pamisonkhano ya mpingo, ndi kukhala ndi phande mwachangu muutumiki Wachikristu. Izi ndizo njira zazikulu zothangatira okhulupirira anzathu ndi kuwathandiza kutsegula njira ya mzimu woyera wa Yehova kuti ugwire bwino ntchito.
Abusa amene amapereka mtundu umenewo wa chichilikizo amachita ntchito yabwino mmalo mwa gulu la nkhosa la Mulungu. (Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1986, pamasamba 23-7.) Zimene abusa auzimu amachita zimayamikiridwa kwambiri ndi gulu la nkhosa. Atalandira chithandizo chotero, mutu wa banja wina anati: ‘Titakhala m’chowonadi kwa zaka 22, tinakokeredwa kudziko ndi mzimu wokondetsa zinthu zakuthupi. Kaŵirikaŵiri tinafuna kufika pamisonkhano, koma kumaoneka kukhala kosatheka kwa ife. Sitinayenererane konse ndi dongosolo la Satana, chotero tinalibiretu oyanjana nawo, tinali opatulidwa. Zimenezi zinatilefula ndi kutipsinja maganizo. Tinafunikira mawu olimbikitsa. Pamene mkulu wina anatichezera, tinavomereza mwachimwemwe makonzedwe a phunziro la Baibulo m’nyumba mwathu. Tsopano tonsefe tilinso m’gulu la Yehova lotetezereka. Sinditha kufotokoza chimwemwe chomwe ndili nacho!’
Pali chifukwa chokhalira achimwemwe pamene abale ndi alongo athu osokera kapena olefuka adzutsidwanso ndi kukhala amphamvu. (Luka 15:4-7) Chifuno cha Yehova kwa anthu ake chimakwaniritsidwa pamene ali ogwirizana “ngati zoŵeta pakati pa busa.” (Mika 2:12) M’ngaka yotetezereka imeneyi, iwo ‘amapeza mpumulo wa miyoyo yawo’ mothandizidwa ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. (Mateyu 11:28-30) Gulu la nkhosa logwirizana la padziko lonse limalandira chitsogozo, chitonthozo, ndi chitetezo limodzi ndi chakudya chauzimu chochuluka.
Lerolino, kupyolera m’ntchito yoŵeta imeneyi, Yehova akuchititsa ntchito yachikondi kuchitika mogwirizana ndi lonjezo lake lamakedzana lakuti: “Ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna. . . . Ndidzawalanditsa m’malo monse anabalalikamo . . . Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino . . . Ndidzafuna yotayika, . . . ndi kulukira tchika yothyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo.” (Ezekieli 34:11-16) Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Yehova ndiye Mbusa wathu!—Salmo 23:1-4.
Chifukwa cha zogaŵira zaumulungu zoŵetera gulu la nkhosa la Mulungu, ife monga atumiki a Yehova tinganene mawu a Davide, amene anati: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.” (Salmo 4:8) Inde, anthu a Yehova amadzimva kukhala otetezereka posamaliridwa ndi iye ndipo ali oyamikira kuti akulu Achikristu amaŵeta nkhosa mwachifundo.
[Mawu a Chithunzi pamasamba 20, 21]
Potter’s Complete Bible Encyclopedia