Nyimbo 207
Kodi Ndife a Yani?
1. Ndinutu wa yani?
Mumamvera yani?
Amene mutumikira
Yemweyo ndi mbuye wanu.
Sungatumikire
Milungu iŵiri
Singagaŵane chikondi chako.
Sukhulupirika.
2. Ndinutu wa yani?
Mudzamvera yani?
Pakuti wina ngwonama,
Wina ngwowona; Sankhani.
Kodi Kaisara
Udzagonjera ’ye?
Kaya udzamveratu Mulungu
Ndi chifuno chake?
3. Ndinetu wa yani?
Ndidzamveratu Ya.
Ndidzatumikira Mlungu;
Wa chowonadi kosatha.
Anandigulatu;
Sindiri wa anthu.
Imfa ya Kristu ndi dipo langa;
Sindidzabwevuka.
4. Ndife a Mulungu!
Musakayikire.
Tikondwera ndi umodzi
Wonenedweratu kale.
Mongatu mafuta
Odzoza wansembe,
Timapeza ukoma kukhala
M’chowonadi chake.