Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/95 tsamba 1-7
  • Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 1/95 tsamba 1-7

Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994

1 Lipoti la chaka chautumiki cha 1994 likusonyeza kuti aliyense wayesetsa kugwira ntchito zolimba pomvera lamulo la mbuye la ‘kulalikira mbiri yabwino’ ndi kupanga ophunzira. (Mat. 24:14, NW; 28:19, 20) Ofalitsa anatsimikizira za kupereka lipoti panthaŵi yake ndipo alembi anakonza ndi kutumiza lipoti la mpingo ku Sosaite panthaŵi yake. Onse ayenera kuyamikiridwa chifukwa cha phande lawo m’lipoti labwino kwambiri limeneli.

2 Tiyeni tione zina za mbali zake zazikulu. Chiŵerengero cha ofalitsa onse chinawonjezeka kuchokera pa 30,408 chaka chatha kufika pa 33,142. Chiŵerengero cha obatizidwa chinawonjezeka kuchokera pa 1,498 chaka chatha kufika pa 4,247 ndipo ofika Pachikumbutso anawonjezeka kuchokera pa 68,525 kufika pa 88,903. Abale akuyamikiridwa chifukwa cha kugwira ntchito zolimba m’kuchititsa maphunziro a Baibulo ndipo chiŵerengero cha ochititsidwawo chinawonjezeka kuchokera pa 19,191 kufika pa 25,219. Kodi tonse sitili okondwa kwambiri kuona chiwonjezeko chimenechi? Kodi pali chilichonse chimene tifunikira kuwongolera mkati mwa chaka chotsatirachi?

3 Kodi tingachitenji mkati mwa chaka chautumiki chatsopano? Tsopano popeza kuti palibenso ziletso pantchito yathu yolalikira tonsefe tifunikira kuthera mwina mwake theka la nthaŵi yathu yolalikira mu ntchito yautumiki wa kunyumba ndi nyumba. Funafunani oyenerera m’malo mwa kupanga maulendo obwereza ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo kwa awo amene sakupita patsogolo konse. Maiko okhala ndi ofalitsa ochepa kuposa Malaŵi akufola gawo lawo kamodzi pa mlungu. Ifenso tiyeneradi kuchita chimodzimodzi.

4 Makamaka, kodi tingachitenji kuti tithandize ana athu kukhala alaliki? Pafupifupi theka la awo amene amafika pamisonkhano yathu ya mpingo ndi yadera ali ana a pasukulu. Kodi anawo ngayani? Ambiri a iwo ali ana athu. Komabe, makolo ambiridi amanena kuti ana awo ngaang’ono kwambiri kwakuti sangakhale ofalitsa. Kodi pali usinkhu wa ana amene angatsagane ndi makolo mu utumiki wakumunda? Kodi ayenera kukhala ofalitsa osabatizidwa choyamba asanayambe kutsagana ndi makolo awo mu utumiki? Ayi, zimenezo zili zosafunika ndipo palibe usinkhu wa ana oti atsagane ndi makolo awo. Mwachitsanzo, mmodzi wa oyang’anira athu achigawo ku Zambia ankatenga mwana wake wamkazi wa zaka zitatu wotchedwa Dorcas mu utumiki ndipo potsirizira pake iye anaphunzira mmene angagaŵire Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Mkulu wina m’dziko limodzimodzilo amatengera mwana wake wausinkhu wosapita kusukulu wotchedwa Chibasha mu utumiki ndipo kamnyamatako kamagaŵira magazini ndi matrakiti atate wake atamdziŵikitsa kwa mwininyumba. Achikulire ambiri amadabwa kumva ana aang’ono akuchitira umboni ndipo amawamvetsera mosamalitsa kwambiri kuposa mmene akanachitira kwa munthu wachikulire. Chotero, musalingalire konse kuti ana anu ngaang’ono kwambiri kwakuti sangatsagane nanu mu utumiki wakumunda ndi kumaphunziro anu a Baibulo. Aphunzitseni kuŵerengera malemba eninyumba ndipo ngakhale kuwafotokozera. Kuphunzitsa kumeneku kuyenera kupitirizabe kufikira pamene wachichepereyo ayenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Zoonadi, maphunzirowo adzapiritirizabe pambuyo pa zimenezo monga momwe timachitira ndi aliyense amene amakhala wofalitsa.

5 Mbali ya Mafunso mu Utumiki Wathu Waufumu wa October 1992 inafunsa kuti: “Kodi ndi kuukulu wotani umene ana aang’ono a makolo Achikristu angakhale ndi phande muuminisitala wakumunda asanazindikiridwe monga ofalitsa osabatizidwa?” Inayankha kuti: “Makolo Achikristu amafuna kuti ana awo akule kukhala atumiki a Yehova achikulire, odzipereka. (1 Sam. 2:18, 26; Luka 2:40) Ngakhale pamsinkhu wachichepere, ana a m’mabanja Achikristu ayenera kukhala okhoza kufotokoza momvekera bwino chodzikanira cha chikhulupiriro chawo cha Baibulo. Kukula kwauzimu kwa ana kumawonjezeredwa pamene atsagana ndi makolo awo muuminisitala wakumunda kuyambira paukhanda. Koma nkofunika kuti achichepere asonkhezeredwe kuchokera mumtima ngati ati asangalale ndi utumiki wakumunda, kukhumba kukhala ofalitsa osabatizidwa, ndi kupitiriza kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira Ufumu. Kuphunzitsa kosamalitsa kochitidwa ndi makolo kumafunikira. (1 Tim. 4:6; 2 Tim. 2:15) Ofalitsa ena okhoza bwino angathandize panthaŵi zina ngati makolo avomereza.—Onani Uminisitala Wathu, masamba 99-100.

6 “Pamene ana akhalidwe labwino atsagana ndi makolo awo Achikristu ku ntchito yakunyumba ndi nyumba, amaphunzira mmene angagwirire ntchito muuminisitala. Koma sadzazindikiridwa monga ofalitsa osabatizidwa kufikira atakulitsa luso ndi luntha lawolawo. Makolo Achikristu angagamulepo kuti ndi kuukulu wotani umene mwana angakhale ndi phande m’kupereka umboni pamene akugwira ntchito pamodzi. Ana amene sanazindikiridwebe monga ofalitsa osabatizidwa sayenera kupanga maulendo ali okha kapena kutsagana ndi ana ena muutumiki wakumunda. Makolo angakonzekeretse ana awo kaamba ka utumiki wakumunda ndi kuwalola kutenga mbali m’njira zosiyanasiyana, monga ngati kuŵerenga lemba, kugaŵira trakiti kapena magazini, kapena kusonyeza mwininyumba chithunzi cha m’buku. Pamene mwanayo akukula, iye angakhale wokhoza kutenga mbali kumlingo wokulira m’kukambitsirana.

7 “Ndi kuphunzitsa koyenerera, achichepere amaphunzira kuzindikira kuwopsa kwa uminisitala pamene avomereza kuchitsogozo cha makolo awo ndi kuchita zinthu moyenera. Makolo sayenera kusiya ana awo amene sanazindikiridwebe monga ofalitsa osabatizidwa pa misonkhano ya utumiki wakumunda, akumayembekezera kuti ena adzawasamalira. Makolo odera nkhaŵa amazindikira thayo lawo laumwini lakuyang’anira ntchito za ana awo. Ndithudi, ofalitsa ena athayo angakhale ofunitsitsa kuthandiza kuphunzitsa ana aang’ono mumpingo amene amasonyeza chikondwerero chenicheni m’kutumikira Yehova muuminisitala.”

8 Tangolingalirani chiŵerengero chowonjezereka cha ofalitsa chimene chingakhaleko m’munda ngati banja lililonse limaona mwamphamvu thayo la kuphunzitsa ana onse kulalikira ndipo ndi umboni wamphamvu chotani umene achichepere ameneŵa angapereke m’munda ndi kusukulu komwe. Musayembekezere mpaka pamene ana anu amaliza sukulu kuti muyambe kuwaphunzitsa koma yambani paukhanda, yambani tsopano lino. Chikhaletu chonulirapo chathu mkati mwa 1995 kuona chiwonjezeko chikumachokera m’mabanja a ife eni choyamba m’malo mwa kuthera nthaŵi pa anthu achilendo chabe. Monga momwe lemba lathu la chaka likulimbikitsira, tiyeni tikhale otsimikizira kuti mabanja athu ‘akhale ogwirizana pamodzi m’chikondi,’ tikumagwira ntchito pamodzi m’kututa kwakukulu.—Akolose 2:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena