Phunziro Laumwini—nkhani Yofuna Chisamaliro
1 Kodi ndi nkhani ziti zimene zimafuna chisamaliro chathu chachikulu? Tiyenera kukhala ofunitsitsa kukulitsa ndi kusunga unansi wapafupi ndi Yehova. Phunziro laumwini limachita mbali yaikulu ya kukulitsa unansi wotero. Lerolino, ndi oŵerengeka mwa ife amene ali ndi mikhalidwe imene imawalola kuthera nyengo zazitali za nthaŵi pakusinkhasinkha ndi pa phunziro laumwini. Komabe, ngati sitiŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, tingakhale ofooka kufikira pa kusoŵa mphamvu ya kulimbana ndi mzimu wa dziko ndi zokhumba zake zathupi.
2 Kulitsani Chikhumbo cha Mawu: Poyamba pamene tinadziŵa za zifuno za Mulungu, mwachionekere tinali ofunitsitsa kupeza chidziŵitso chowonjezereka. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, njala yathu ya chakudya chauzimu ingakhale itazirala. Pangafunikire “kukulitsa chikhumbo” cha chakudya chauzimu. (1 Pet. 2:2, NW ) Kodi tingakulitse motani chikhumbo chimenecho?
3 Kununkhira kwa chakudya chokondedwa kumayambitsa kuŵaŵa kwa njala chifukwa cha kukumbukira kukoma kwa chakudyacho. Nyengo zazifupi za phunziro laumwini zingatiyambukire m’njira yofananayo mwauzimu. Kudya zibenthu zingapo zokoma za chakudya chauzimu kungasonkhezere njala yathu ya kufuna kudziŵa choonadi chakuya. Chikhutiro chimene chimadza chifukwa cha kuphunzira chingatilimbikitse kufufuza mwakuya m’Mawu a Yehova.
4 Kulitsani Njira Yochitira Zinthu Imene Ili Yabwino Kwambiri kwa Inu: Ena amapatula nthaŵi yonse ya madzulo kaamba ka phunziro laumwini, pamene kuli kwakuti ena amakonda nyengo zazifupi zapafupipafupi za phunziro. Ngati muona kuti mumamvetsetsa bwino kwambiri mmamaŵa, mungasankhe kuchita phunzirolo musanafisule. Ngati mumamvetsetsa kwambiri usiku, mungasankhe kuchita phunziro lanu musanakagone. Mulimonse mmene zingakhalire, chinthu chofunika ndicho kukhala wanthaŵi zonse ndi kumamatira pa njira yochitira zinthu yoyenerera bwino koposa zosoŵa zanu.
5 Pamene tilimbikitsidwa kuchita phunziro laumwini mowonjezereka, mwina tingafulumire kunena kuti tili kale ndi zochita zambiri. Komabe, tonsefe tifunikira kukhala oona mtima m’kupenda mmene timathera nthaŵi yathu. Kodi tsiku lililonse maola ambiri amatheredwa pakuonerera maprogramu a wailesi yakanema? Kodi tili ofunitsitsa kudzimana zokonda zathu zina? Kupenda moona mtima za mmene timagwiritsirira ntchito nthaŵi yathu mwachionekere kudzasonyeza nyengo zatsiku ndi tsiku zimene zingagwiritsiridwe ntchito mopindulitsa pa phunziro laumwini.—Aef. 5:15, 16.
6 Phunziro la Mawu a Mulungu limafuna chisamaliro chathu chonse. Kuyesa kuchita kanthu kena panthaŵi yofananayo kumachepetsa mapindu ake. Ngati timayesa kuphunzira pamene tikudya, kumvetsera wailesi, kapena kuonerera wailesi yakanema, mwachionekere sitidzamwerekera m’zimene tikufuna kudziŵa. (1 Tim. 4:15) Chotero pafunika kuchotsa zocheukitsa.—Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 33-4.
7 Phunziro latsiku ndi tsiku ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo nzofunika chifukwa chakuti imeneyo ndiyo njira imene timalandiriramo chitsogozo kuchokera kwa Yehova. Pangani kukhala chonulirapo chanu kutenga choonadi chosindikizidwa ndi kuchiloŵetsa mu mtima mwanu. Gwiritsirani ntchito mwaŵi uliwonse, mosasamala kanthu kuti ndi waufupi motani, kuti muŵerenge, kupenda, kapena kusinkhasinkha pa zinthu zauzimu.—Deut. 6:6-8; Akol. 1:9, 10.