Misonkhano Yautumiki ya January
Mlungu Woyambira January 2
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.
Mph. 17: “Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho yokambidwa ndi mkulu amene ana ake ali ofalitsa, kapena amene amalalikira ndi ana ake aang’ono. Ndime zonse ziyenera kuŵerengedwa. Yamikirani ofalitsa kaamba ka mbali yawo m’ntchito yowonjezereka mkati mwa chaka chautumiki.
Mph. 18: “Kugwiritsira Ntchito Bwino Mabuku Athu Akale.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Dziŵitsani mpingo za mabuku akale amene alipo; alimbikitseni kuti aombole makope kaamba ka kuwagwiritsira ntchito mu utumiki. Linganizani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zachidule za maulaliki osonyezedwa.
Nyimbo Na. 188 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 9
Mph. 15: Zilengezo za pamalopo. Lipoti la maakaunti. Pendani mbali zokondweretsa za brosha la Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira (Onani Utumiki Wathu Waufumu wa October 1994, patsamba 7.) Limbikitsani onse kutenga makope awo ndi kuwagaŵira pamene kuli koyenera.
Mph. 15: “Ubusa Umene Uli Womangirira.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu yotengedwa pa mawu a mutu waung’ono pamasamba 21-3 a kope la Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993. Fotokozani uphungu wa m’Malemba wotithandiza kulimbana ndi mavuto.
Mph. 15: Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro? Nkhani yokambidwa mwamphamvu komanso yosonkhezera maganizo yoperekedwa ndi mkulu wokhoza bwino yoti ithandize abale kuyamikira chitetezero chofunika cha khadi lathu la Advance Medical Directive/Release ndi Identity Card. Tsatiraninso njira ya m’January wapitayo kuti mutsimikizire kuti onse amene ali oyenerera ndi amene akufuna chitetezero chimenechi, achipeze mwa kulemba makadiwo. Onani Utumiki Wathu Waufumu wa January 1994, patsamba 2, pa “Mlungu Woyambira January 10” kaamba ka tsatanetsatane wake.
Nyimbo Na. 198 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 16
Mph. 10: Zilengezo za pamalopo. Kambitsiranani mfundo zokambitsirana za m’magazini atsopano. Limbikitsani onse kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda kutha kwa mlungu uno.
Mph. 18: “Lingalirani za Ena—Mbali 1.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanimo zikumbutso zonena za kufunika kwa akulu kugwirira ntchito pamodzi poona ngati denga, mipope, mafani, magetsi, ndi zotetezera Nyumba Yaufumu zikusamaliridwa bwino.—Onani Utumiki Wathu Waufumu wa January 1985, tsamba 4.
Mph. 17: “Sonyezani Kuti Mumasamala mwa Kupanga Maulendo Obwereza.” Ofalitsa atatu kapena anayi akambitsirana za chifuno ndi kufunika kwa kupanga maulendo obwereza. Agogomezera za chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro. Apenda maulaliki osonyezedwawo. Achita chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri, kaguluko kakumayamikira ndi kupereka malingaliro ena a kuwongolera.
Nyimbo Na. 196 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 23
Mph. 5: Zilengezo za pamalopo.
Mph. 10: “Mmene Mungalinganizire Laibulale Yateokratiki.” Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1994, masamba 28-31.
Mph. 20: “Kutetezera Ana Anu ku Mwazi.” Mkulu akamba nkhaniyo pandime 1-11. Sonyezani bwino lomwe chifukwa chimene makolo amene amavomereza dokotala kusamalira mwana wawo m’mikhalidwe yofotokozedwa m’ndime 5-7 sayenera kuonedwa monga ogonjera.
Mph. 10: “Phunziro Laumwini—Nkhani Yofuna Chisamaliro.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanimo ndemanga zosankhidwa mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1985, masamba 8-13.
Nyimbo Na. 116 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 30
Mph. 12: Zilengezo za pamalopo. Mkulu afotokoza za Lipoti la Utumiki Wakumunda la September. Yamikirani abale kaamba ka kugwira ntchito zolimba m’chiwonjezeko chimene chakhalapo.
Mph. 15: “Kutetezera Ana Anu ku Mwazi.” Kukambitsirana mwamafunso ndi mayankho kwa ndime 12-28. Sumikani chisamaliro pa mayankho a mafunso osonyezedwa m’ndime 12 ndi 20. Gogomezerani kuti kukonzekera pasadakhale kochitidwa ndi makolo m’kupeza chisamaliro cha mankhwala cha mwana wawo kaŵirikaŵiri ndiko mfungulo ya chipambano m’kupeŵa kuthiridwa mwazi.
Mph. 18: Gaŵirani Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha m’February. Fotokozani chifukwa chake pali kufunika kwakuti anthu akhale ndi chidziŵitso chimene bukuli lili nacho. (Onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 1988, masamba 25-6, ndime 17, 18.) Simbani mwachidule zokumana nazo zosonyeza chiyamikiro chosonyezedwa ndi anthu oona mtima amene aliŵerenga. (Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1989, patsamba 32, ndi Nsanja ya Olonda ya December 1, 1991, patsamba 32.) Perekani malingaliro ena osonyeza mmene tingayambitsire maphunziro a Baibulo ndi anthu okondwerera amene tinawagaŵira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Chitani kuti wofalitsa wokhoza bwino achitire chitsanzo ulaliki wachiŵiri mwachidule pa mutu wakuti “Moyo/Chimwemwe” m’buku la Kukambitsirana, patsamba 11. Kapena gwiritsirani ntchito ulaliki wina woyenerana ndi kumaloko. Kumbutsani omvetsera kuti adziombolere mabuku ogwiritsira ntchito mu utumiki mlungu uno.
Nyimbo Na. 199 ndi pemphero lomaliza.