Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/95 tsamba 3-6
  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Muli ndi Kuyenera kwa Kusankha
    Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 1/95 tsamba 3-6

Kutetezera Ana Anu ku Mwazi

1 “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.” (Sal. 127:3) Ngati muli nacho choloŵa chamtengo wapatali chimenecho cholandira kwa Yehova, inu monga makolo, muli ndi thayo lodzetsa chimwemwe, ngakhale kuti nlalikuludi, la kuphunzitsa, kusamalira, ndi kutetezera ana anu. Mwachitsanzo, kodi mwachitapo kanthu mwa njira iliyonse yofunikira kutetezera ana anu aang’ono kuti asathiridwe mwazi? Kodi ana anu angachite motani ngati ayang’anizana ndi mkhalidwe wofuna kuti athiridwe mwazi? Kodi munakambitsirana monga banja zimene mungachite kuti mulake mkhalidwe wopereka chiwopsezo cha kuthiridwa mwazi?

2 Kukonzekeretsa banja lanu kaamba ka mikhalidwe yoteroyo sikuyenera kuchititsa nkhaŵa yosafunikira ndi kupsinjika maganizo. Simungathe kuyembekezera ndi kukonzekerera chotigwera chilichonse m’moyo, koma zilipo zinthu zambiri zimene inu monga makolo mungachite pasadakhale, kuti mutetezere ana anu kuti asathiridwe mwazi. Kunyalanyaza mathayo ameneŵa kungachititse mwana wanu kuthiridwa mwazi popatsidwa chithandizo cha mankhwala. Kodi muyenera kuchitanji?

3 Kutsimikiza Mtima Kolimba Nkofunika: Muyenera kulingalira mwamphamvu ponena za kutsimikiza mtima kwanu kwamphamvu pa lamulo la Mulungu la mwazi. Kodi mumaphunzitsa ana anu kumvera Yehova pankhani imeneyi, monga momwe mumawaphunzitsira malamulo ake a kuona mtima, makhalidwe, uchete, ndi nkhani zina za moyo? Kodi timaonadi mmene lamulo la Mulungu linalamulirira pa Deuteronomo 12:23 kuti: “Mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo”? Vesi 25 limawonjezera kuti: “Musamadya uwu; kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m’mbuyo mwanu, pakuchita inu zoyenera pamaso pa Yehova.” Dokotala anganene kuti mwazi ‘ungakomere’ mwana wanu wodwalayo, koma muyenera kulimbika mtima pasanabuke vuto lililonse la kukana mwazi kwa inu eni ndi kukanira ana anu, mukumaona unansi wanu ndi Yehova kukhala wofunika kuposa kutalikitsidwa kwa moyo kulikonse kumene kungafune kuswa lamulo lake laumulungu. Zimaphatikizapo chiyanjo cha Mulungu tsopano ndi moyo wosatha mtsogolo!

4 Inde, Mboni za Yehova zimakonda moyo. Sizimakhumba kufa. Izo zimafuna kukhala ndi moyo kuti zitamande Yehova ndi kuchita chifuniro chake. Ndicho chimodzi cha zifukwa zimene izo zimapitira kuzipatala ndi kupereka ana awo kuti akachiritsidwe. Zimapempha madokotala kuzichiritsa, ndipo pamene ziuzidwa kuti mwazi ndiwo njira yotsatiridwa yochiritsira kapena ndiwo chithandizo cha mankhwala chimene chasonyezedwa, zimapempha njira ina yochiritsira popanda mwazi. Zilipo njira zina zambiri m’malo mwa mwazi. Madokotala achidziŵitso amazigwiritsira ntchito. Njira zina zochiritsira zimenezo sindizo mankhwala ongopeka chabe, koma zimaphatikizapo machiritso oyenera ndi malangizo olembedwa m’mabuku otchuka a zamankhwala. Madokotala zikwi zambiri kuzungulira dziko lonse amatithandiza pakupereka chisamaliro chabwino cha mankhwala popanda kugwiritsira ntchito mwazi, ngakhale kuti lidakali vuto nthaŵi zina kupeza madokotala omwe angachiritse ana a Mboni popanda kugwiritsira ntchito mwazi.

5 Kupeza Dokotala Wothandiza: Madokotala amakhala ndi nkhaŵa zambiri pochiritsa odwala, ndipo pamene muwapempha kuchiritsa mwana wanu popanda mwazi, zimenezi zimakulitsa vuto lawolo. Madokotala ena amavomera kuchiritsa achikulire ndi kulemekeza zofuna zawo pankhani ya mwazi malinga ngati fomu yowamasula ku mlandu yadzazidwa. Ena angavomerezenso kuchiritsa achichepere omwe asonyeza kuti ali achichepere okhwima, pakuti makhoti ena avomereza kuti achichepere okhwima ali nako kuyenera kwa kupanga zosankha zawozawo pa zamankhwala. (Onani Nsanja ya Olonda, June 15, 1991, masamba 16-17, kuti mupeze mfundo zosonyeza amene ali wachichepere wokhwima.) Komabe, madokotala angakane kuchiritsa ana aang’ono, makamaka makanda, pokhapo ngati ali ndi chilolezo cha kuthira mwazi. Kwenikweni, ndi madokotala oŵerengeka chabe amene angalonjeze motsimikiza kuti sadzagwiritsira ntchito mwazi pamikhalidwe iliyonse pochiritsa mwana. Pazifukwa zamankhwala ndi zalamulo, madokotala ambiri amaganiza kuti sangapereke chitsimikizo choterocho. Komabe, owonjezereka akufuna kupereka chithandizo kwa ana a Mboni za Yehova malinga ndi mmene angakhozere m’kulemekeza zofuna zathu pa mwazi.

6 Malinga ndi zimenezi, bwanji ngati, pofunira mwana wanu dokotala, mupeza amene ali ndi mbiri yabwino ya kuthandiza Mboni za Yehova ndi amene kumbuyoku anachitapo kuchiritsa kofananako pa Mboni zina popanda mwazi, komabe akuti lamulo silimulola kukupatsani chitsimikizo chonse chakuti mwazi sudzagwiritsiridwa ntchito? Komabe, iye akukutsimikizirani kuti sakuona kuti padzakhala vuto ngakhale panthaŵiyo. Inu mungaone limenelo kukhala lingaliro labwino koposa. M’mikhalidwe yotero mungaganize za kumlola kuti apitirize. Komabe, mveketsani bwino kuti pakulola kwanu kuchiritsa mwana wanu simukulola kumthira mwazi. Kutsatira kachitidwe kameneka kukakhala thayo limene muyenera kutenga popanda kuchititsa chosankha chanu kuonedwa kukhala kugonja.

7 Ndithudi, ngati mungapeze njira ina yabwino yochiritsira imene ingachepetseko vuto la mwazi kapena kulichotsapo, pamenepo mungasankhe kutenga njira imeneyo yosakhala yaupandu kwambiri. Muyenera kuyesayesa mwakhama kuti mupeze dokotala kapena dokotala wa opaleshoni amene angavomereze kuposa wina aliyense kusagwiritsira ntchito mwazi. Chitetezo chabwino ndicho kukhala woyembekezera zovuta. Pangani kuyesayesa kulikonse kwa kupeza dokotala wothandiza pasadakhale. Ngati kuli kotheka, yesani kupeŵa madokotala ndi zipatala zosafuna kuthandiza.

8 M’maiko ena mfundo ina imene ingathandize kusapatsidwa mwazi ndiyo mmene kulipirira chithandizo cha chipatala kumachitidwira. Kumene odwala ali ndi inshuwalansi ya umoyo kapena chinjirizo linalake limene limawalola kudzifunira okha dokotala amene iwo angafune, ana angatetezereke kwa madokotala kapena antchito achipatala osafuna kuthandiza. Kaŵirikaŵiri, ndalama zokwanira zolipiridwa zimatheketsa mtundu wa kuchiritsa ndi chithandizo zimene banja lingafune kulandira kwa madokotala ndi zipatala. Ndiponso, kaya chipatala kapena dokotala ali wofunitsitsa kulola mwana kusamutsidwa, kaŵirikaŵiri zimadalira pa kukhoza kwa makolo kulipirira chithandizocho. Ndipo inu anakubala amene muli ndi pakati, kuli kofunika kuti musamalire thanzi lanu m’nthaŵi yokhala ndi pathupi! Zimenezi zidzathandiza kwambiri kuletsa kubadwa kwa mwana miyezi isanakwane ndi zovuta zotsatirapo, popeza kuti njira yotsatiridwa yochiritsira makanda obadwa osakhwima ndi mavuto awo kaŵirikaŵiri imaphatikizapo mwazi.

9 Nthaŵi zina madokotala amadandaula kuti Mboni za Yehova sizimafotokoza kukana kwawo mwazi kufikira pamphindi yomalizira. Zimene siziyenera konse kukhala choncho. Chimodzi cha zinthu zoyambirira zimene makolo a Mboni ayenera kuchita popita kuchipatala kapena poitanitsa chithandizo cha dokotala ndicho kukambitsirana naye kaimidwe kawo pa mwazi. Ngati padzakhala opaleshoni, pemphani kuonana choyamba ndi dokotala wochititsa dzanzi. Dokotala wa opaleshoni angakuthandizeni pambali imeneyi. Mafomu oloŵera m’chipatala ayenera kupendedwa mosamalitsa. Muli nayo mphamvu ya kufafanizapo chilichonse chimene simufuna. Kuti muchotsepo chikayikiro chilichonse, lembani pa fomu yoloŵera m’chipatala moonekera bwino kuti, mulimonse mmene zingakhalire, simufuna kapena kulola mwazi pazifukwa zachipembedzo ndi za umoyo.

10 Thandizo Loperekedwa ndi Gulu la Yehova: Kodi ndi makonzedwe otani amene gulu la Yehova lapanga kuti likuthandizeni kutetezera ana anu ku mwazi? Alipo ambiri. Sosaite yafalitsa zochuluka kutiphunzitsa ponena za machiritsidwe a mwazi ndi opanda mwazi. Mwaphunzira brosha lakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? ndi zofalitsidwa zina pankhani imeneyi. Ndipo muli nawo abale ndi alongo m’mipingo yanu amene angakupatseni chithandizo ndi chichirikizo chachikulu. Ngati pali vuto, akulu angakuone kukhala kofunika kulinganiza kulonda kwa maola 24 kuchipatala, makamaka ndi mkulu ndi kholo la wodwalayo kapena wachibale wa m’banjalo. Kaŵirikaŵiri kuthira mwazi kumachitika usiku pamene achibale onse apita kunyumba kukagona.

11 M’kupita kwanthaŵi Makomiti Olankhulana ndi Chipatala adzapangidwa m’mizinda yaikulu. Mipingo yonse idzagaŵiridwa komiti yopangidwa ndi abale ophunzitsidwa omwe adzakhala okonzekera kuthandiza. Mudzafunikira kuwafikira pamene akhala ofunikira, kupyolera mwa akulu anu. Iwo sadzayenera kuitanidwira mavuto aang’ono, koma musayembekeze kwa nthaŵi yaitali kwambiri kuwaitana ngati mwaona kuti pangakhale vuto lalikulu. Iwo kaŵirikaŵiri akhoza kupereka maina a madokotala ofuna kuthandiza ndi malingaliro a njira zina. Pamene kuli kofunika ndi kotheka, abale ameneŵa amalinganiza kuti akhalepo pachochitikacho kuti athandize kusamalira vutolo.

12 Kukhala Odikira ndi Kuchita ndi Kuloŵamo kwa Khoti: Bwanji ngati dokotala kapena chipatala chikufuna kupeza chilolezo cha khoti cha kuthira mwana wanu mwazi? Kodi apa ndipo polekera, mukumaganiza kuti palibenso zimene mungachite? Kutalitali! Kungakhalebe kotheka kupeŵa kuthira mwazi. Mkhalidwe wothekera woterowo uyenera kukonzekeredwa pasadakhale. Kodi mungachitenji?

13 Kudziŵa malamulo amene amatsogoza kapena kusonkhezera zipatala ndi oweruza m’nkhani zimenezi kudzakuthandizani kwambiri kupereka zifukwa zodzichinjiriza. Limodzi la malamulo ofunika kwambiri amenewo ndilo lakuti lamulo silimapatsa makolo ulamuliro wonse wa kuvomereza kapena kukana chithandizo cha mankhwala pa ana awo. Ngakhale kuti achikulire kwakukulukulu ali ndi kuyenera kwa kuvomereza kapena kukana chithandizo cha mankhwala malinga ndi chikhumbo chawo, makolo alibe ufulu wa kukana chithandizo cholingaliridwa kukhala chofunikira kaamba ka ubwino wa mwana wawo ngakhale pamene kukana kwawo kuli kozikidwa pa zikhulupiriro zoona mtima zachipembedzo.

14 Lamulo lalikulu limeneli linaperekedwa m’chigamulo cha mu 1944 cha Supreme Court ya ku United States chimene chinati: “Makolo angakhale aufulu kufera chikhulupiriro chawo. Koma iwo alibe ufulu, m’mikhalidwe yofananayo, wa kuchititsa ana awo kufera chikhulupiriro asanafike pausinkhu wa kuzindikira kokwanira kwalamulo, pamene iwo akhoza kudzipangira okha chosankha chimenecho.” Nkhaŵa yaikulu imeneyi pa thanzi ndi umoyo wa mwana ikuphatikizidwanso m’malamulo a lerolino osamalira umoyo wa ana. Malamulo ameneŵa, oikidwira kuletsa nkhanza pa ana, aikidwiranso kutetezera ana kuti asanyalanyazidwe pa chisamaliro cha mankhwala.

15 Ndithudi, makolo Achikristu samatsutsa kutetezera ana ku nkhanza ndi kunyalanyazidwa ndi makolo. Koma malamulo oletsa kunyalanyaza ana ndi mawu a Supreme Court ogwidwawo kaŵirikaŵiri amagwiritsiridwa ntchito molakwa m’nkhani zoloŵetsamo ana a Mboni za Yehova. Chifukwa ninji? Choyamba, cholinga cha makolo Achikristu sindicho chakuti ana awo “afere chikhulupiriro.” Chikanakhala chimenecho, nanga amaperekeranji ana awo kuchipatala? Mosiyana ndi zimenezo, makolo a Mboni amafuna kupeza chithandizo cha mankhwala kaamba ka ana awo. Iwo amakonda ana awo ndipo amafuna kuti iwo akhale ndi thanzi labwino. Koma iwo amakhulupirira kuti ali ndi thayo lopatsidwa ndi Mulungu la kusankha mosamala mtundu wa chithandizo cha mankhwala umene uli wabwino koposa kwa ana awo. Iwo amafuna kuti matenda a ana awo achiritsidwe popanda mwazi. Njira zina zochiritsira popanda mwazi sizili chabe zabwinopo ndi zotetezereka kuposa za mwazi zimenezo, komanso, chofunika koposa, zimalolabe ana awo kukhala m’chiyanjo cha Wopatsa Moyo wamkulu, Yehova Mulungu.

16 Ngakhale kuti njira zochiritsira zopanda mwazi zili ndi mapindu ake, madokotala ambiri ndi oyang’anira za umoyo wa ana amaona kuthira mwazi kukhala njira yochiritsira yoyenera kutsatiridwa imene ingakhale yofunikira kapena ngakhale yopulumutsa moyo m’zochitika zina. Chifukwa chake, pamene makolo a Mboni akana kuthira mwazi kovomerezedwa, pangabuke mavuto. Kunena mwachisawawa, madokotala sangapereke mwalamulo chithandizo cha mankhwala kwa ana popanda chivomerezo cha makolo. Kuti apeŵe chitsutso cha makolo pa kugwiritsira ntchito mwazi, madokotala kapena antchito ena a m’chipatala angakafune chivomerezo cha woweruza mwa njira ya chilolezo cha khoti. Chivomerezo cha khoti choterocho chingapezedwe kupyolera mwa oyang’anira za umoyo wa ana kapena madokotala kapenanso akuluakulu achipatala akumachita zimenezo kuti atetezere mwana ku chimene amati ndi kunyalanyaza kupereka mankhwala.a

17 Nthaŵi zambiri zilolezo za khoti za kugwiritsira ntchito mwazi zimatengedwa mofulumira makolo asakudziŵa kwenikweni kapena asakudziŵa kalikonse. Madokotala, akuluakulu achipatala, kapena oyang’anira za umoyo wa ana amayesayesa kulungamitsa zilolezo zofulumizitsidwa zimenezo mwa kunena kuti pali vuto lofuna chisamaliro mwamsanga limene silimalola nthaŵi yodziŵitsa makolo bwino lomwe za zimene zikuchitika. Komabe, kaŵirikaŵiri pofunsitsidwa, madokotalawo avomereza kuti sipamakhala vuto lofuna chisamaliro mwamsanga kwenikweni ndi kuti amangofuna chilolezo cha khoti “kuti mwinamwake,” malinga ndi kuona kwawo, kuthira mwazi kungakhale kofunikira pambuyo pake. Monga makolo ake a mwana wanuyo, inu muli ndi kuyenera kwakukulu kwa kudziŵa zimene madokotala, akuluakulu achipatala, kapena oyang’anira za umoyo wa ana akuchita kwa mwana wanu panthaŵi iliyonse. Lamulo limafuna kuti, ngati kuli kotheka, muyenera kuuzidwa za kufuna kwawo kupeza chilolezo cha khoti ndipo muyenera kuloledwa kupereka malingaliro anu pamaso pa khoti.

18 Mfundo zimenezi za lamulo zimasonyeza kufunika kwa kupeza dokotala wothandiza. Thandizanani naye, ndipo limodzi ndi chithandizo cha ziŵalo za Komiti yanu Yolankhulana ndi Chipatala, mthandizeni kuyesayesa njira yochiritsira vuto la mwana wanu yosagwiritsira ntchito mwazi kapena samutsirani mwana wanu kwa dokotala kapena chipatala chimene chidzapereka njira yochiritsira imeneyo. Koma ngati pali zizindikiro zakuti dokotalayo, mkulu wa chipatala, kapena wantchito yoyang’anira za umoyo wa ana akufuna kupeza chilolezo cha khoti, muyenera kukhala maso ndi kufunsa ngati zimenezo ndi zimene akulinganizadi kuchita. Nthaŵi zina zimenezi zimachitidwa mobisa pafoni. Ngati pali makonzedwe a kupita kukhoti, gogomezerani kuti mukufuna kudziŵa zimenezo kotero kuti nanunso mukapereke malingaliro anu kwa woweruza. (Miy. 18:17) Ngati pali nthaŵi, kaŵirikaŵiri kumakhala bwino kufuna chithandizo cha loya.

19 Ngati kukana kwanu mwazi kutengeredwa kukhoti, lingaliro la dokotala lakuti mwazi ngwofunikira kupulumutsa moyo kapena thanzi la mwana wanu lingakhale lokopa kwambiri. Woweruza, pokhala munthu wamba m’zamankhwala, kaŵirikaŵiri amagonja pa ukatswiri wa dokotala m’zamankhwala. Zimenezi zimachitika makamaka pamene makolo sakupatsidwa mpata wabwino kapena sapatsidwa uliwonse kuti alongosole malingaliro awo pankhaniyo, pamene kuli kwakuti dokotalayo, mosatsutsidwa, amaloledwa kufotokoza maganizo ake ponena za kufunika “kwamwamsanga” kwa mwazi. Kachitidwe ka zinthu ka mbali imodzi koteroko sikali koyenera kudziŵira zenizeni. Choonadi nchakuti, nthaŵi imene madokotala amalingalirira kuti mwazi uli wofunikira ndi chifukwa chake, zimadalira kwambiri pa kapenyedwe ka munthu ndipo nzosatsimikizirika. Kaŵirikaŵiri, pamene dokotala wina anena kuti mwazi uli wofunikira kwenikweni kuti upulumutse moyo wa mwana, dokotala wina, wokhala ndi chidziŵitso cha kuchiritsa nthenda yofananayo popanda mwazi, amanena kuti mwazi suli wofunika kuchiritsira wodwalayo.

20 Kodi munganenenji ngati loya kapena woweruza akufunsani chifukwa chimene mwakanira kuthira mwazi “kopulumutsa moyo” wa mwana wanu? Ngakhale kuti chikhoterero chanu choyamba chingakhale cha kufuna kufotokoza chikhulupiriro chanu cha chiukiriro ndi kusonyeza chikhulupiriro chanu cholimba chakuti Mulungu adzaukitsa mwana wanu akafa, yankho loterolo mwa ilo lokha lingangokhutiritsa maganizo a woweruzayo, kuti inu muli wachipembedzo wotengeka maganizo, motero nkhaŵa yake yaikulu ya umoyo wakuthupi wa mwanayo idzamchititsa kuona kuti ayenera kuloŵererapo kuti atetezere mwana wanu.

21 Chimene khoti liyenera kudziŵa nchakuti, ngakhale kuti mukukana mwazi pa zifukwa zamphamvu zachipembedzo, inu simukukana chithandizo cha mankhwala. Woweruza afunikira kuona kuti simuli makolo osasamala kapena ankhanza, koma, m’malo mwake, kuti ndinu makolo achikondi omwe mukufuna kuti mwana wanu achiritsidwe. Kokha kuti simukuvomereza kuti mapindu onenedwawo a mwazi ngaakulu kuposa maupandu ake ndi zovuta zake zakupha, makamaka pamene njira zina zochiritsira zimene zilibe maupandu ameneŵa zilipo.

22 Zikumadalira pamkhaliwewo, mungadziŵitse woweruzayo kuti lili lingaliro la dokotala mmodzi lakuti mwazi uli wofunikira, koma madokotala amasiyana m’kapenyedwe kawo, ndipo pemphani kuti mupatsidwe mwaŵi wokafuna dokotala yemwe adzasamalira mwana wanu ndi njira zina zochiritsira zopanda mwazi. Mothandizidwa ndi Komiti Yolankhulana ndi Chipatala, mungakhale mutapeza kale dokotala woteroyo amene adzasamalira mwana wanu popanda mwazi ndi amene adzapereka umboni wothandiza m’khoti, mwinamwake pafoni. Mwachionekere komiti yolankhulanayo idzakhala yokhoza kusonyeza woweruza—ngakhale madokotala omwe akuyesayesa kupeza chilolezo cha khoti—nkhani zonena za mankhwala zosonyeza mmene vuto la mwana wanu lingachiritsidwire popanda kugwiritsira ntchito mwazi.

23 Pamene oweruza apemphedwa kupereka zilolezo za khoti mofulumira, kaŵirikaŵiri samalingalira kapena kukumbutsidwa za maupandu ambiri okhala m’mwazi, kuphatikizapo AIDS, kutupa chiŵindi, ndi maupandu ena ambiri owopsa. Mukhoza kutchula zimenezi kwa woweruza, ndipo mungamudziŵitsenso kuti, monga kholo Lachikristu, mumaona kugwiritsira ntchito mwazi wa munthu wina kuti upulumutse moyo kukhala kuswa lamulo la Mulungu kwakukulu ndi kuti kukakamiza mwazi pa mwana wanu mudzakuona kukhala mlandu wofanana ndi wa kugwirira chigololo. Inu ndi mwana wanu (ngati ali wamkulu wokhoza kupereka zifukwa za iye mwini) mungalongosole kunyansidwa kwanu ndi kuloŵerera pathupi la munthu kumeneko kopanda lamulo ndipo mungapemphe woweruzayo kuti asapereke chilolezocho koma kuti akuloleni kufunafuna njira zina zochiritsira mwana wanu.

24 Pamene zifukwa zoyenera zodzichinjiriza zaperekedwa, oweruza amakhala okhoza kuona bwino lomwe mbali inayo—mbali yanu—monga makolo. Pamenepo samakhala ofulumira kwambiri kulamula kuthira mwazi. M’zochitika zina, oweruza achepetsa kwambiri ufulu wa madokotala wa kugwiritsira ntchito mwazi, nthaŵi zina amafunadi kuti njira zina zigwiritsiridwe ntchito choyamba, kapena apereka mwaŵi kwa makolo wakuti adzipezere okha madokotala omwe angachiritse popanda mwazi.

25 Pochita ndi awo ofuna kukakamiza kuthira mwazi, nkofunika kwambiri kuti musapereke chizindikiro chilichonse cha kugwedezeka pa maganizo anu otsimikizirika. Oweruza (ndi madokotala) nthaŵi zina amafunsa kaya makolo agakhale ndi vuto lililonse ngati thayo la kugamula kuthira mwazi “lisamutsidwira” pa iwo, akumalingalira kuti zimenezi zingachititse kukhala kosavuta kwa makolowo kukhala ndi chikumbumtima chawo chili choyera. Koma muyenera kudziŵitsa onse okhudzidwa kuti, inu monga makolo, mukuona kukhala ndi thayo la kupitiriza kuchita zonse zimene mungathe kuti mupeŵe kuthira mwazi. Ili ndi thayo lopatsidwa kwa inu ndi Mulungu. Silingasamutsidwe.

26 Chifukwa chake, polankhula ndi madokotala ndi oweruza, muyenera kukhala wokonzekera kufotokoza kaimidwe kanu momvekera bwino ndi motsimikiza mtima. Ngati chilolezo cha khoti chiperekedwabe mosasamala kanthu za zoyesayesa zanu za kukana, pitirizani kuchonderera dokotalayo kuti asathire mwazi ndipo limbikitsani kugwiritsira ntchito njira ina yochiritsira. Pitirizani kumpempha kuti aone nkhani zonena za mankhwala ndi chilangizo cha madokotala ena amene ali ofunitsitsa kufunsidwa za vuto la zamankhwala limenelo kotero kuti apeŵe mwazi. Pazochitika zingapo, madokotala ena ooneka kukhala osafuna kusintha maganizo atuluka m’chipinda cha opaleshoni akumalengeza monyadira kuti sanagwiritsire ntchito mwazi. Motero, ngakhale chilolezo cha khoti chitaperekedwa, zivute zitani, musagonje!—Onani kope la Nsanja ya Olonda ya June 15, 1991, pa “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga.”

27 Kumbukirani kuti Yesu anati: “Chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu . . . ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.” Kuti zitiyendere bwino m’mikhalidwe yoteroyo, Yesu anawonjezera kuti mzimu woyera ukatithandiza kukumbukira zimene zikakhala zoyenera ndi zothandiza kunena panthaŵi zoterozo.—Mat. 10:16-20.

28 “Wolabadira mawu adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala.” (Miy. 16:20) Makolo, konzekerani pasadakhale kutetezera ana anu kuti asathiridwe mwazi ndi kudetsedwa mwauzimu. (Miy. 22:3) Ananu, labadirani chiphunzitso cha makolo anu cha malangizo okukonzekeretsani ndipo asungeni mumtima mwanu. Monga banja, “mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo . . . kuti chikukomereni inu” chifukwa cha kukhala ndi dalitso la Yehova ndi chiyanjo chake.—Deut. 12:23-25.

[Mawu a M’munsi]

a Njira zochiritsira zoonedwa ndi dokotalayo kukhala zofunikira kupulumutsa moyo kapena thanzi la mwana (kuphatikizapo kuthira mwazi) zingagwiritsiridwe ntchito mwalamulo popanda chivomerezo cha makolo kapena cha khoti kokha mkati mwa vuto lamwamsanga lofuna chisamaliro panthaŵi yomweyo. Ndithudi, thayolo liyenera kukhala m’manja mwa dokotalayo pamene adalira pa mphamvu ya lamulo limeneli la zamwadzidzidzi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena