Zilengezo
◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu March: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. April ndi May: Mkupiti wa sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. June: Baibulo Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapa iyenera kutero pa fomu yawo ya Literature Request (S-AB-14) yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina wosankhidwa ndi iye ayenera kuŵerengera akaunti ya mpingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Mutachita zimenezi lengezani ku mpingo.
◼ Nthambi ili ndi timabuku ta Chicheŵa ta “Phunzirani Kuŵerenga ndi Kulemba” m’sitoko. Mipingo ikulimbikitsidwa kuoda timabuku timeneti ndi kuyamba makalasi ophunzira kuŵerenga ndi kulemba.
◼ Kuyambira pa July 3, 1995, brosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano” ndi buku la Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona, adzaphunziridwa pa Phunziro Labuku Lampingo.
◼ Tikulimbikitsa wofalitsa aliyense kulingalira za kulembetsa upainiya wothandiza m’April.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Chicheŵa: Kukambitsirana za m’Malemba; Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?; Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Chingelezi: “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial”; Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”; Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza; Mankind’s Search for God; mabaundi voliyumu a Watchtower a 1960-93. (Chaka chilichonse chili ndi voliyumu yake ndipo voliyumu imodzi ndi K72.00.) Chonde sonyezani bwino lomwe chaka (zaka) chimene mukufuna pa fomu ya Literature Request (S-AB-14).