Kufeŵetsa Zinthu pa Msonkhano
1 Timafuna dalitso la Yehova pamene tikupita patsogolo mosalekeza. Tikukondwa kuona kuti wapatsa anthu ake mzimu wofunika wa nzeru ndi kuzindikira. Tiyenera kuvomerezadi kuti kupyolera mwa kagulu ka kapolo wokhulupirika, Yesu Kristu wasamalira zinthu bwino lomwe kuti chifuno cha Yehova chichitike m’njira yodabwitsa. (Mat. 24:45-47; Akol. 1:9, 10) Chonde dziŵani kuti sipadzakhala makafiteriya. Chakudya chidzakonzedwa kokha kaamba ka awo amene adzakhala akuyenda ulendo wautali kupita ku msonkhano. Komabe, zakumwa zoziziritsa kukhosi pa malo amisonkhano zidzakhala zopezeka kwa onse. Mabotolo ake ayenera kubwezeredwa kumalo ogulitsira zakumwa zoziziritsa kukhosi.
2 Monga chotulukapo cha kufeŵetsa kayendetsedwe ka utumiki wathu wachakudya abale ndi alongo ambiri amene anali kugwira ntchito zolimba mkati mwa magawo amsonkhano kutikonzera chakudya anali okhoza kumvetsera programu. Kunali kusintha kwabwino chotani nanga kumeneku, kukumapeputsa ntchitoyo ndi kulola kuti chisamaliro chowonjezereka chiperekedwe kumbali zauzimu za msonkhano, antchitowo akumakhoza kumvetsera ndi kusangalala kwambiri ndi programuyo. (Deut. 31:12) Kuchotsa Utumiki wa Chakudya kudzatheketsadi ambiri kupindula mokwanira ndi programu yauzimu.
3 M’zaka zimene chakudya chinali kukonzedwa ndi kuperekedwa, panafunikira antchito odzifunira ochuluka kuti makonzedwewo alinganizidwe ndi kuchirikizidwa.
4 Kutumikira mofunitsitsa kwa awo amene atumikira monga antchito odzifunira m’mbali imeneyi kwakhala kwaphindu losayerekezereka ndi koyamikiridwa kwambiri. Komabe, ndi kufeŵetsa zinthu kumeneku, okwanira zikwi amenewo otumikira pa kugulidwa kwa zinthu, kukonza, kutumiza, ndi kupereka chakudya adzakhala okhoza kugwiritsira ntchito nthaŵi yawo pa zinthu zofunika za Ufumu, kuphatikizapo kusangalala ndi mayanjano mokwanira pa misonkhano. Antchito odzifunira amenewo amene anali kutumikira mu Utumiki wa Chakudya tsopano adzakhala okhoza kuthandiza m’madipatimenti ena, monga ngati a Ukalinde ndi Kuyeretsa. Zimenezi zidzapeputsa zinthu kwa aliyense ndipo sizidzafuna kuti ambiri agwire ntchito kufikira usiku kwambiri, mbandakucha, kapena mkati mwa magawo a programu, monga momwe zinalili m’madipatimenti ambiri a Utumiki wa Chakudya.
5 Kuchirikiza Makonzedwewo: Sosaite ikuyamikira kwambiri chichirikizo chabwino chimene abale ndi alongonu mwapereka “ndi mtima wangwiro” m’zaka zapitazi ku makonzedwe amsonkhano, kuphatikizapo utumiki wa chakudya. (1 Mbiri 29:9) Zimenezi zathandiza m’njira zambiri. Zakhozetsa awo amene afikapo kukhalabe pa malo amsonkhanopo m’nthaŵi ya kupuma kwakufupi kwa masana kotero kuti apeze chakudya moyenera, kutsitsimulidwa, ndiyeno kukhalapo pa programu yauzimu. Ndipo mosakayikira kuoloŵa manja ndi chichirikizo zimene zasonyezedwa ndi abale ndi alongo pochirikiza makonzedwe ameneŵa zidzapitirizabe. Zimenezi zakhala chisonyezero cha chiyamikiro chawo m’njira yothandiza.—Miy. 11:25; Luka 16:9.
6 Kudzikonzera Chakudya: Komabe, limodzi ndi kusintha kumeneku, kudzakhala kofunikira kuti munthu aliyense ndi mabanja adzikonzere chakudya chokwanira iwo okha pa kupuma kwathu kwakufupi kwa masana. Timaŵerengera kwambiri mapindu abwino a programu yauzimu. Kulola chakudya chakuthupi kukhala chinthu chofunika kopambana kungakhale kopanda nzeru. Nkofunika kwambiri kuti aliyense wa ife ‘atsimikizire za zinthu zofunika kwambiri’ pa nkhaniyi. (Afil. 1:9, 10a, NW) Misonkhano yaikulu yaposachedwapa ya anthu a Yehova ku Poland, Russia ndi Ukraine, ndiponso ndi kumalo ena, yachitidwa ndi chipambano chabwino kwambiri popanda makonzedwe achakudya. Pa uliwonse nthumwi zinadza ndi chakudya chawo cha masana. Ngati tidza ndi chakudya chopepuka chamasana, tidzapeza kuti chidzatithandiza kukhala ndi maganizo ogalamuka, ndi kutikhozetsa kupindula mokwanira ndi programu yamasana. Mogwirizana ndi zimenezi, aliyense ayenera kudza ndi chakudya chimene chili chosavuta kukonza ndi chomanga thupi. Mwachitsanzo, pamene Yesu anadyetsa makamu, anangogaŵira mitundu iŵiri ya chakudya, mkate ndi nsomba. (Mat. 14:16-20; onaninso Luka 10:42a.) Makonzedwe amodzimodziŵa adzatsatiridwa pa misonkhano yadera ndi misonkhano ya tsiku lapadera. Chifukwa chake, tili okondwa kupereka malingaliro ena onena za zimene zingakhale zoyenera ndi zothandiza polingalira za kupuma kwakufupi kwamasana ndi mtundu wa zinthu zimene tingagwiritsire ntchito.
7 Popeza kuti sipadzakhala makonzedwe a utumiki wa chakudya pa msonkhanopo, awo amene adzafikapo, limodzi ndi kulinganiza kwabwino, adzakhala okhoza kudya mfisulo ndi mabanja awo kunyumba kwawo kapena kumalo odyerako apafupi. Mwa kugona mokwanira usiku, mudzakhala wokhoza kudzuka mofulumira kuti mukonze zofunikira kaamba ka chakudya cha mmaŵa ndi kufika pa msonkhano nthaŵi ikalipo kuti mudzayanjane ndi nthumwi zina. Monga momwe zakhalira kumbuyoku, sipadzakhala pofunikira kwa aliyense kuthamangira kumalo amsonkhano kukafunafuna malo okhala, pakuti padzakhala malo okwanira olinganizidwira khamu loyembekezeredwa.
8 Kupuma kwamasana kudzakhala kofupikirako kuposa mmene kunalili pamisonkhano yapitayo. Komabe, kudzaperekabe mpata wa kudya chakudya chopepuka, ndiponso nthaŵi ya kucheza ndi ena. Abale ndi alongo athu amene akukhala mu mzinda wa msonkhanowo kapena pafupi nawo ndi amene adzakhala akubwerera kwawo tsiku lililonse madzulo adzatha mosavuta kukonzera chiŵalo chilichonse cha banja chakudya chochepa chodza nacho kaamba ka kupuma kwa masana. Chimenechi chingakhale chofanana kwambiri ndi chakudya chamasana chimene achichepere amatengera kusukulu, monga ngati masangweji ndi chipatso china, mabisiketi, ndi zakumwa zina. Anthu ambiri amatengera chakudya chamasana chofanana ndi chimenecho kuntchito kwawo. Tidzakondwa kuona kuti abale sakupita kwawo koma akukhalabe pamalo amsonkhano mkati mwa kupuma kwamasana.
9 Popeza kuti malo amsonkhano amakhala ngati Nyumba Yaufumu yaikulu mkati mwa msonkhanowo, kulinso kwanzeru kupeŵa kuyambitsa mkhalidwe wonga wa ku pikiniki mkati mwa kupuma kwamasana. Ndipo monga momwedi sitimadya kanthu mkati mwa misonkhano pa Nyumba Yaufumu, sitiyeneranso kudya kapena kumwa mkati mwa magawo a programu ya msonkhano. Mabokosi aakulu oziziritsira zinthu a ku pikiniki sadzaloledwa m’malo mmene msonkhano udzachitidwira popeza kuti akhoza kuchititsa ngozi. Ngati kuli kofunika, bokosi laling’ono loziziritsira zinthu limene lingaikidwe kunsi, osati pampando, lingagwiritsiridwe ntchito.
10 Tiyeneranso kusamala za mtundu wa zotengera zakumwa zimene tidzafuna kudza nazo kumalo amsonkhano. Zakumwa zotentha zingabweretsedwe zitaikidwa m’mafulasiki. Zotengera zagalasi za mtundu uliwonse zingakhaledi zangozi. Chotero, tikupempha kuti MUSABWERETSE ZOTENGERA ZAGALASI pamalopo.
11 Mapindu Ena: Zoonadi tingaone nzeru ya makonzedwe osinthidwa amenewo. Onse adzakhala okhoza kutchera khutu kuti alandire mapindu auzimu—chifuno chenicheni cha kusonkhana kwathu. Mapindu ameneŵa amaperekedwa m’kuyanjana kumene timakhala nako ndiponso m’programu yeniyeniyo. Chotero m’malo mwa kuchoka pamalopo pa kupuma kwamasana kukafunafuna chakudya, kudzakhala kopindulitsa chotani nanga kubwera ndi chakudya. Zimenezi zidzapangitsa kukhala kotheka kuyanjana ndi abale ndi alongo athu ndipo zidzatipeŵetsa kuphonya programu iliyonse yamasana.
12 Pokhala atatsitsimulidwa mwauzimu ndi programu yamasana, ena angafune kupitirizabe ndi mayanjano Achikristu ndi kukambitsirana ponena za zinthu zabwino zimene aphunzira pamene akudya chakudya ndi banja ndi mabwenzi m’malo odyera akumaloko. Ena angangogula kanthu kena m’golosale kapena pakantini. Awo amene ali okhoza kubwerera kwawo angasankhe kukadya kumeneko, monga momwedi amachitira pamasiku ena pamene aweruka kuntchito kapena mu utumiki wakumunda.
13 Timasangalaladi ndi phwando lauzimu pamasonkhano ameneŵa ndi misonkhano yaikulu, pamene timalandirapo zofalitsidwa zatsopano, chiphunzitso chabwino, ndi uphungu wothandiza. Madalitso ameneŵa ndiwo amene aliyense amakumbukira, limodzi ndi chisangalalo cha kukhala ndi anthu a Mulungu osonkhanitsidwa. Miyambo 10:22 imati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.” Zimenezi zili chifukwa chakuti monga anthu a Yehova, sitimafika pamisonkhano tili ndi lingaliro la kudzafunafuna zinthu zakuthupi ndi kupeza bwino. Timasonkhana tili ndi chikhumbo chabwino cha kupeza phindu lalikulu koposa lothekera m’njira yauzimu, ndipo Yehova amatidalitsa kwambiri chifukwa cha mzimu umene timasonyeza.—1 Tim. 6:6-8; Aheb. 11:6.
14 Nyengo za chilimbikitso zimenezi zimatikumbutsanso za kupita patsogolo kwa kututa kwauzimu. (Yoh. 4:35, 36) Mawu otsegulira a Yesaya chaputala 54 amapempha gulu longa mkazi la Yehova kukonzekerera chiwonjezeko chosangalatsa. Kukula kowonjezereka, chifutukuko, ndi kupatsidwanso nyonga zili patsogolapa monga momwe Yesaya analoserera: “Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako. Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere.” Kukwaniritsidwa kwa ulosi wokondweretsa umenewu kwachititsa chifutukuko chapadera kwambiri cha kulambira koona chimene tikuona tsopano.—Yes. 54:1-4.
15 Kukuonekeradi kukhala njira yanzeru kugwiritsira ntchito makonzedwe ofeŵetsedwa amsonkhano ameneŵa kotero kuti ndi zocheukitsa zochepetsedwa kwambiri, onse adzasangalala ndi programu yauzimu imene yakonzedwa. Tikukhulupirira kuti zimenezinso zidzakhala ndi dalitso la Yehova, popeza kuti zidzaloleza kusamalira bwino lomwe chiwonjezeko chinanso. Mwa kusumika maganizo pa zimene zikufunika, tidzakhala okhoza kusangalala ndi masiku athu olinganizidwa a kuyanjana kwachimwemwe ndi zinthu zabwino zauzimu. Pemphero lathu loona mtima nlakuti Yehova adalitse zoyesayesa zathu zonse pamene tikupitirizabe kusonkhana ndi kudyetsedwa pa gome lake.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 16:14, 15.
[Bokosi patsamba 6]
Malo a Msonkhano Wachigawo wa 1995
MALO AMSONKHANO DERA
RUMPHI M-1, 2, 4
CHITENGA M-6, 7, 10, 11
MPHUNZI M-14, 15, 16
MAKANDA M-23, 24
BANGA M-3, 5
CHIGWENEMBE M-8, 9, 12, 13
SONGANI M-17, 18, 19, 20
NKHONYA M-21, 22
BLANTYRE (Chingelezi) M-23
[Bokosi patsamba 6]
Mapindu a Kusakhala ndi Makonzedwe a Utumiki wa Chakudya
◼ Ntchito yochepa programuyo isanayambe, mkati mwake, ndi pambuyo pake, ikumaloleza kuyanjana kowonjezereka
◼ Palibe ziwiya za zakudya zoti zisamaliridwe
◼ Anthu ochuluka amatha kupereka chisamaliro chokwanira ku programu yauzimu
◼ Pamakhala antchito odzifunira ambiri oti athandize m’madipatimenti ena
◼ Pamapezeka nthaŵi yambiri yochita zinthu zina zateokrase
Chakudya Chimene Mungabwere Nacho cha Nthaŵi ya Kupuma Kwamasana
◼ Chakudya chamasana chopepuka, chosavuta kukonza, ndi chomanga thupi
◼ Mtedza, mandasi, zipatso
◼ Mabokosi oziziritsira zinthu aang’ono ngati ali ofunika
◼ Zakumwa zoziziritsa kukhosi, madzi a zipatso, kapena madzi a m’botolo losakweka
MUSABWERETSE Zinthu Izi ku Malo a Msonkhano
◼ Moŵa
◼ Zotengera zagalasi
◼ Mabokosi oziziritsira zinthu aakulu a ku pikiniki