Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/97 tsamba 3-6
  • Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Msonkhano Wachigawo wa mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa “Atamandi Achimwemwe”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Misonkhano Yachigawo ya 1999 ya “Mawu Aulosi a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 7/97 tsamba 3-6

Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”

1 Mtumwi Paulo anamkumbutsa Timoteo kuti “lemba lililonse adaliuzira Mulungu.” (2 Tim. 3:16) Popeza Mawu a Mulungu ali ouziridwa, tili ndi chifukwa chabwino chowakhulupirira. Chaka chino mutu wa msonkhano wachigawo ndi wakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu.” Programuyo idzalimbikitsa kukhulupirira kwathu Baibulo, kaya tadziŵa choonadi kwa zaka zambiri kapena tangoloŵa kumene m’gulu la Yehova. Tonsefe tiyeni tikonzekere kukapezekapo paprogramu yonse. Kudzakhala kolimbikitsa chotani nanga ngati okondwerera atsopano, makamaka aja omwe timaphunzira nawo Baibulo, akhalapo limodzi nafe!

2 Msonkhano wa Masiku Atatu: Chaka chino programu ya masiku atatu ya msonkhano wachigawo yakonzedwa kuti tipeze nayo phindu. Mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa March 1997, yandandalika misonkhano yachigawo 13 yodzachitika muno m’Malaŵi. Tikhulupirira kuti tsopano mukudziŵa msonkhano wachigawo umene mpingo wanu unaikidwako, ndipo muyenera kuti mwapanga kale makonzedwe okapezeka paprogramu yonse ya masiku atatu. Kodi munakambitsirana ndi okulembani ntchito kuti akuloleni nthaŵi yatchuti? Ngati muli ndi ana opita kusukulu ndipo msonkhano wanu uli mkati mwa masiku a sukulu, kodi mwadziŵitsa aphunzitsi mwaulemu kuti ana anu sadzakhalako kusukulu pa Lachisanu chifukwa cha chochitika chofunika kwambiri chimenechi cha maphunziro awo achipembedzo?—Deut. 31:12.

3 Tsiku lililonse Programuyo idzayamba pa 9:30 a.m. Anthu adzayamba kuloŵa pa 8.00 a.m. Omwe adzaloledwa kuloŵa nthaŵiyo isanakwane ndi aja okha omwe adzapatsidwa ntchito, koma sadzaloledwa kusunga mipando kufikira nthaŵi itakwana yakuti onse ayambe kuloŵa.—Afil. 2:4.

4 Tiyenera Kumvetsera: Mtumwi Petro anakumbutsa Akristu a m’zaka za zana loyamba kuti anayenera kumvetsera mawu a ulosi monga nyali yoŵala m’malo a mdima. (2 Pet. 1:19) Ifenso tiyenera kuchita zimenezo. Kukhala m’dziko lakaleli lolamulidwa ndi Satana kuli ngati kukhala m’malo amdima. Tili osangalala kuti taitanidwa kuchoka mumdima wauzimu. (Akol. 1:13; 1 Pet. 2:9; 1 Yoh. 5:19) Kuti tikhalebe m’kuunika, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba mwa kumvetsera Mawu ouziridwa a Yehova. Msonkhano wathu wachigawo chaka chino udzatilimbikitsa kuchita zimenezo.

5 Tifunikira kuchita khama la kusumika maganizo paprogramu, ndipo tidzadalitsidwa pochita zimenezo. Tiyenera kuyesayesa kufika pamalo a msonkhano titapumula bwino kotero kuti tikatchere khutu pamaprogramu. Tsiku lililonse fikani pamalo a msonkhano nthaŵi idakalipo kuti programu ikupezeni mutakhala kale. Ndiyeno imbani nawo nyimbo yoyamba ndi pemphero poyamba programu ya tsikulo. Akulu akulu ayenera kupereka chitsanzo, ndipo makolo ayenera kuphunzitsa ana awo.—Aef. 6:4.

6 Ngati tioneratu mitu ya nkhani programu ya tsikulo isanayambe, tingayambe kuganizira za mfundo zomwe zingaperekedwe m’nkhanizo. Izi zidzakulitsa chidwi chathu pamene nkhanizo zikukambidwa. Tingafune kumva mfundo zimene zidzatithandiza kufotokozera ena chifukwa chake timakhulupirira Mulungu ndi lonjezo lake lodalirika la kudalitsa aja omfunafuna moona mtima. (Aheb. 11:1, 6) Tingachite bwino kulemba mfundo zachidule zomwe zingatithandize kukumbukira mfundo zazikulu paprogramuyo. Ngati tilemba zambiri, mfundo zazikulu zingatipite chifukwa timakhala otangwanika kwambiri.

7 Chaka chathanso panali akulu ndi achinyamata ambiri omwe anali kumangoyendayenda mkati ndi kunja kwa malo osonkhanira, akumachezerana ndi ena pamene programu inali mkati, m’malo mwa kumvetsera zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anapereka kuti zitipindulitse. Yesu analonjeza kuti adzatipatsa chakudya chauzimu panthaŵi yake. (Mat. 24:45-47) Choncho, tiyenera kukhalapo kuti tipindule ndi chakudyacho m’malo mwa kusonyeza kusayamikira. (2 Akor. 6:1) Kukuonekanso kuti pamene ana ena afuna kukaseŵera, kaŵirikaŵiri amapempha kuti apite kuchimbudzi. Ngati tiwaphunzitsa bwino kunyumba anawo, maulendo otulukatuluka kupita kuchimbudzi adzachepa. Nthaŵi zina, achinyamata amakhala paokha m’timagulu akumalankhula, kunong’onezana, ndi kupatsirana timapepala. Achinyamata athu omwe amakumana ndi mavuto ambiri lerolino, afunikira kutchera khutu pamene nkhani zikuperekedwa, osati kumachita zinthu zina pamene programu ili mkati. Achinyamata ayenera kupeŵa zilakolako zaunyamata zosagwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:22.) Kutchera khutu kwa onse, akulu ndi achinyamata, kudzalemekeza Yehova ndi kumkondweretsa.

8 Ngati kukhala koyenera kuti kalinde apereke uphungu kwa aliyense pankhanizi, tiyenera kulandira uphunguwo monga chikondi chochokera kwa Yehova. (Agal. 6:1) Tonse tifunikira kukumbukira kuti chifukwa chimene timachitira khama kuti tipezeke pamsonkhano wachigawo nchakuti ‘timvetsere ndi kuphunzira.’ (Deut. 31:12) Ndiponso, ‘wanzeru adzamva, nawonjezera kuphunzira.’ (Miy. 1:5) Nthaŵi yotsalayi musanapite kumsonkhano wachigawo, kambitsiranani monga banja kufunika kwa kukhala pamodzi pamsonkhano, kusayendayenda mkati mwa programu, ndi kutchera khutu kuti mukapindule mokwanira ndi programuyo.

9 Mavalidwe Omwe Amakondweretsa Yehova: Anthu onse m’dziko amafuna kuona Mboni za Yehova. (1 Akor. 4:9) Ambiri amatidziŵa chifukwa cha mavalidwe oyenera ndi kapesedwe kabwino. Kutsatira mapulinsipulo a m’Malemba pa 1 Timoteo 2:9, 10 ndi 1 Petro 3:3, 4 kwachititsa ambiri kuyamba kuoneka bwino kwambiri kusiyana ndi mmene anaonekera pamene anangoyamba kuyanjana ndi mpingo wachikristu. Zimenezi zikusiyana kwambiri ndi mavalidwe ndi mapesedwe omwe tikuona m’dziko omwe akuipiraipira nthaŵi zonse. Tikufuna kukhala maso kuti tisafanane ndi dziko m’maonekedwe athu—kuvala zovala zosayenera, kutsatira masitayelo a dziko okonzera tsitsi, kapena kuvala zovala zosapatsa ulemu. Mavalidwe athu abwino ndi kapesedwe ziyenera kuthandiza atsopano obwera pamsonkhano kuona mmene Akristu ayenera kuvalira.

10 Pamene kuli kwakuti tinapereka chithunzi chabwino pamisokhano yachigawo ya chaka chatha, tidakali ndi vuto la kavalidwe ka dziko kwa abale ndi alongo ena, makamaka panthaŵi yakupuma. Pokonzekera msonkhano, tiyenera kupenda mavalidwe ndi kapesedwe kathu. Makolo, mwanzeru samalani zimene ana anu aang’ono ndi achinyamata adzavala. Tisamale kuti tisalole masitayelo a dziko kuipitsa kaonekedwe kathu kachikristu.

11 Sungani Khalidwe Labwino: Khalidwe labwino ndi chizindikiro cha Akristu oona. (1 Pet. 2:12) Mkhalidwe wathu kulikonse kumene tingakhale—pamsokhano wachigawo, kulesitiranti, kumahotela, ndi pamene tili paulendo—ungapereke umboni wabwino ndi kuthandiza ena kuona mmene kukhulupirira Mulungu ndi Mawu ake kungathandizire anthu. Zimenezi zingawasonkhezere kufuna kumdziŵa Yehova. (Yerekezerani ndi 1 Petro 3:1, 2.) Tili ndi mwaŵi wa kulemekeza Yehova mwa khalidwe lathu. Amanijala a hotelo ina ku Alabama anati nthumwi zathu ndizo “alendo abwino koposa kuwachereza.” Anawonjezera kuti: “Ungakhale mwaŵi wathu ngati mungabwerenso mtsogolo.” Bungwe loyang’anira misonkhano ndi alendo kumpoto koma chakumadzulo kwa United States linalemba kuti: “Chaka chilichonse, anthu onse kuno kwathu amayang’anira mwachidwi msonkhano wa Watchtower Society. Anthu anu ndi abwino kwambiri; ali ndi khalidwe laulemu kwenikweni. Amalonda kuno kwathu amadziŵa chimenechi ndipo amakondwera pamene ‘banja’ la alendoli libweranso chaka chilichonse.” Malipoti otere amakondweretsa kuwaŵerenga, kodi sichoncho? Komabe, tiyenera kusamala kuti tisunge mbiri yabwino ya anthu a Yehova.

12 Timakumbutsidwa kambirimbiri za kulamulira ana athu, kuti tisamawalole kumathamangathamanga pamalo a msonkhano ali okha, akumadodometsa ena. Chaka chilichonse, Sosaite imalandira malipoti onena za ana athu ena kuti amakhala opanda wowayang’anira akuyendayenda pafupi ndi dziŵe losambira kapena amaonedwa akuthamangathamanga m’malikole ndi paliponse. Ngakhale kuti misonkhanoyo imatipatsa mpata wocheza ndi kuyanjana ndi abale athu, makolo ayenera kukumbukira udindo wawo woyang’anira ana awo nthaŵi zonse. Umenewu ndiwo udindo umene Yehova amapatsa kholo lililonse. (Miy. 1:8; Aef. 6:4) Kungowalekerera ana osawadzudzula angachite zinthu zimene zingawononge mbiri yabwino imene Mboni za Yehova zina zagwira ntchito yaikulu kuipanga.—Miy. 29:15.

13 Kulipirira Ndalama Zowonongedwa Pamsonkhano: Tonsefe tidzawononga ndalama pofika pamisonkhano imeneyi. Koma pali ndalama zina zowonongedwa zimene tiyenera kulingalira. Malo omwe timasonkhanira amafuna ndalama zambiri. Palinso zinthu zina zofuna ndalama. Zopereka zathu zaufulu pamisonkhano yachigawo zimayamikiridwa kwambiri.—Mac. 20:35; 2 Akor. 9:7, 11, 13.

14 Malo Okhala: Malangizo omwe tapereka pazaka zingapo adzagwirabe ntchito. SUNGIRANI MIPANDO APABANJA OKHA NDI ALIYENSE AMENE MUKUYENDA NAYE M’GALIMOTO LANU. Zakhala bwino kuona kuti zaka zaposachedwapa ambiri atsatira malangizo ameneŵa, ndipo zimenezi zakulitsa chikondi chosonyezedwa pamisonkhano. M’malo ambiri mipando ina ili pafupi kuposa ina. Chonde sonyezani chikondi mwa kusiyira mipando yapafupiyo aja amene angayenere kukhalapo chifukwa cha mikhalidwe yawo.

15 Makamera, Mavidiyo Kamera, ndi Marediyo Kaseti: Makamera ndi ziŵiya zina zojambulira angazigwiritsire ntchito pamisonkhano. Komabe, pamene tizigwiritsira ntchito sitiyenera kusokoneza ena. Sitiyenera kuyendayenda ndi kumajambula pamene programu ili mkati, pakuti zimenezo zidzasokoneza ena omwe akuyesa kumvetsera programu. Palibe amene ayenera kulumikiza chiŵiya chilichonse chojambulira ku magetsi kapena ku zokuzira mawu, ndipo chiŵiyacho sichiyenera kutsekereza njira, kapena kulepheretsa ena kuona.

16 Chipatala: Dipatimenti ya Chipatala ili ya zamwadzidzidzi zokha. Siitha kusamalira matenda aakulu. Ndicho chifukwa chake muyenera kusamalira za matenda anu ndi a banja lanu pasadakhale. Chonde, nyamulani mankhwala anu monga aspirin, mankhwala a m’mimba, zomangira chilonda, anapini, ndi zina zotero, pakuti sizidzakhalapo pamsonkhano. Munthu aliyense amene amachita khunyu, nthenda ya shuga, kudwala mtima, ndi zina zotero ayenera kukonzekera pasadakhale mmene adzasamalira vuto lake. Ayenera kukhala ndi mankhwala ofunikira, ndipo wapabanja kapena wa mumpingo wodziŵa bwino za vutolo ayenera kukhala naye nthaŵi iliyonse kuti amthandize. Zachititsa mavuto pamsonkhano pamene anthu odwala matenda aakulu anasiyidwa okha ndiyeno nthenda yawo nkuuka. Oyang’anira msonkhano akakamizika kufunafuna ambulansi ya mwadzidzidzi kuti awapititse kuchipatala. Ngati ena odwala alibe achibale omwe angawasamalire, akulu mumpingo wawo afunika kudziŵa za mkhalidwewo ndi kupanga makonzedwe a kuwathandiza. Pamsonkhano sipadzakhala zipinda zapadera zokhalamo amene ali ndi matenda.

17 Chakudya Pamsonkhano: Kusakhala ndi dipatimenti ya chakudya pamisonkhano kwachititsa ambiri kukhala omasuka mkati mwa maprogramu ndi kulandira bwino chakudya chauzimu. Talandira makalata ambiri oyamikira kupeputsa zinthu kumeneku chiyambire pamene makonzedwewa anakhazikitsidwa. Onse ayenera kukonzekera kunyamula chakudya chawo chabwino cha masana, monga chija chotchulidwa m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa July 1995, ndime 25. Ena m’gulumo akhala akumadya ndi kumwa mkati mwa programu. Kutero kumasonyeza kupanda ulemu. Kumene anthu ena amagulitsa zakudya pafupi ndi msonkhano, abale ena apita kumeneko mkati mwa programu. Kachitidwe kameneko nkosayenera

18 Timayamikiradi phwando lathu lauzimu ndi mayanjano amtendere panthaŵi zakupuma. Malinga ndi cholinga cha makonzedwe ameneŵa, m’malo mwa kuchoka pamalo a msonkhano popuma masana ndi kukagula chakudya, chonde bweretseni chakudya chanu. Mukatero, mudzakala ndi nthaŵi yaikulu yocheza ndi abale ndi alongo anu.

19 Tili osangalala chotani nanga kuti Msonkhano Wachigawo wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” uyamba posachedwa! Tonsefe tikufuna kutsimikiza kuti takonzekera bwino lomwe kukapezeka paprogramu yonse, kuti tikasangalale mokwanira ndi phwando lauzimu limene Yehova watikonzera kupyolera m’gulu lake. Mwa njira imeneyo tidzakhala “wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino masiku akudzawo.”—2 Tim. 3:17.

[Bokosi patsamba 6]

Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo

Ubatizo: Opita ku ubatizo ayenera kukhala m’malo awo programu isanayambe Loŵeruka mmaŵa. Aliyense wofuna kubatizidwa ayenera kubweretsa chovala choyenera choloŵera m’madzi ndi thaulo yake. Kumbuyoku ena anavala chovala chosayenera ndipo zimenezo sizinapereke ulemu pachochitikacho. Akulu pokambitsirana ndi ofuna kubatizidwa mafunso a ubatizo m’buku la Uminisitala Wathu ayenera kutsimikiza kuti aliyense akumvetsa mfundo zimenezi. Pambuyo pa nkhani ya ubatizo ndi pemphero loperekedwa ndi wokamba nkhaniyo, tcheyamani wa programuyo adzaitanitsa nyimbo. Ataimba mzera womaliza, akalinde adzaperekeza opita ku ubatizo kumalo obatizira. Ubatizo pokhala chizindikiro cha kudzipatulira kwa munthu uli nkhani yaumwini pakati pa munthuyo ndi Yehova. Choncho, nkosayenera kuti obatizidwawo akumbatirane kapena kugwirana manja pobatizidwa.

Mabaji: Chonde valani baji yanu ya 1997 nthaŵi zonse pamene muli mumzinda mmene msonkhanowo ukuchitika ndiponso popita ndi pobwerako kumsonkhano. Iwo kaŵirikaŵiri amatipatsa mpata woperekera umboni wabwino. Mabaji ndi mapulasitiki ake muyenera kuwagula pampingo panu, chifukwa sadzakhalako kumsonkhano. Musayembekezere mpaka kutatsala masiku oŵerenga a msonkhano kuti mufunse zamabaji a banja lanu. Kumbukirani kunyamula khadi lanu latsopano la Advance Medical Directive/Release.

Ntchito Yaufulu: Kodi mungapatule nthaŵi pamsonkhano ndi kuthandiza m’dipatimenti ina pamsonkhanopo? Kutumikira abale athu, ngakahle pamaola ochepa chabe, kungakhale kothandiza kwambiri ndipo kumakhutiritsa. Ngati mutha kuthandiza, chonde pitani ku Dipatimenti ya Ntchito Yaufulu pamsonkhanopo. Ana osafika zaka 16 angathandizenso kwambiri mwa kugwira ntchito pamodzi ndi kholo kapena munthu wina wamkulu.

Mawu Ochenjeza: Khalani osamala za mavuto omwe angabuke kuti mupeŵe zovuta. Kaŵirikaŵiri mbala ndi anthu ena oipa amakonda kubera alendo. Khomani galimoto lanu nthaŵi zonse, ndipo musasiye chinthu chilichonse choonekera chimene mbala ingakopeke nacho mtima ndi kuphwanya galimoto. Mbala ndi opisa m’thumba amakonda pamene anthu ambiri amasonkhana. Sikungakhale kwanzeru kusiya zinthu zilizonse zofunika pampando wanu. Simungadziŵe kuti aliyense wokhala nanu pafupi ali Mkristu. Nanga nkumuyeseranji aliyense? Talandira malipoti akuti anthu ena ayesa kunyengerera ana kuti apite nawo. YANG’ANIRANI ANA ANU NTHAŴI ZONSE.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena