Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu July ndi August: Lililonse la mabrosha a masamba 32 otsatirawa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Sangalalani ndi Moyo Padziko Lapansi Kosatha! September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. October: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Gaŵirani sabusikripishoni pamene mwapeza munthu wochita chidwi. Kuyambira chakumapeto kwa mweziwu, tidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35.
◼ Pokhala ndi milungu isanu yokwana bwino, mwezi wa August ungakhale nthaŵi yabwino kwa ambiri kuti achite upainiya wothandiza.
◼ Kuyambira September, oyang’anira dera adzapereka nkhani yapoyera yamutu wakuti “Khulupirirani Mphamvu Yopulumutsa ya Yehova.”
◼ Tikudziŵitsa ofalitsa onse a m’dera la Lilongwe kuti chipinda chamabuku tsopano chachoka ku Area 11 puloti nambala 36. Chasamukira ku Area 10 puloti nambala 313. Kumeneko nkumene mungagule mabuku anu pamasiku a Lolemba ndi Lachisanu monga tinalengezera mu Utumiki Wathu Waufumu wa January 1997. Ndiponso, mipingo imene imagwiritsira ntchito Njira Yoperekera Katundu Na. 2-00 ikhoza kumakatenga katundu wawo pamalo amodzimodziwa pamasiku a Lolemba ndi Lachisanu okha.