“Ndani Adzatimukira Ife?”
Yehova atafunsa funso limeneli, Yesaya anayankha mwamsanga kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yes. 6:8) Popeza pali zambiri zofuna kututa lerolino, chiitanocho chikuperekedwa tsopano. Antchito a nthaŵi zonse owonjezereka—apainiya okhazikika—akufunika mwamsanga! (Mat. 9:37) Kodi mukufuna kudzipereka? Ngati zili choncho, September 1, kuyamba kwa chaka chautumiki cha 1998, idzakhala nthaŵi yabwino yoloŵera upainiya. Bwanji osapempha fomu yofunsirapo kwa akulu?