Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 4-5
  • Mtima Wodzipereka Umabweretsa Madalitso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtima Wodzipereka Umabweretsa Madalitso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Othandiza Ali Kwina Kulikonse
    Galamukani!—2001
  • Anthu Ongodzipereka Akugwiradi Ntchito
    Galamukani!—2001
  • “Tichitire Onse Chokoma”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Ntchito Yongodzipereka Yokhala ndi Mapindu Okhalitsa
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 4-5

Mtima Wodzipereka Umabweretsa Madalitso

1. Kodi Davide ndi Nehemiya anasonyeza bwanji mtima wodzipereka?

1 Goliati atanyoza asilikali a Isiraeli, msilikali aliyense akanatha kudzipereka kumenyana naye. Koma mnyamata yemwe anali m’busa, wosaphunzitsidwa kumenya nkhondo, ndi amene anadzipereka kumenyana naye. (1 Sam. 17:32) Ayuda omwe anatengedwa ukapolo atabwerera ku Yerusalemu n’kulephera kumanganso malinga, woperekera zakumwa kwa mfumu ya ku Perisiya ndi amene anadzipereka kusiya ntchito yake yabwino m’nyumba yachifumu n’kupita ku Yerusalemu kuti akalongosole ntchitoyo. (Neh. 2:5) Yehova anadalitsa amuna awiri onsewa, Davide ndi Nehemiya, chifukwa cha mtima umene anasonyeza.—1 Sam. 17:45, 50; Neh. 6:15, 16.

2. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusonyeza mtima wodzipereka?

2 Masiku ano, mtima wodzipereka ukusowa m’dzikoli. “M’masiku otsiriza” ano, anthu amakhala otanganidwa kwambiri, ndipo ambiri ndi “odzikonda.” (2 Tim. 3:1, 2) N’zosavuta kuti munthu angotanganidwa kwambiri ndi zokonda zake n’kumalephera kuona mipata yothandizira anthu ena pakafunika kutero. Komabe, ife monga Akhristu, timafuna kutsanzira Yesu, amene ankafunafuna mipata yothandizira ena. (Yoh. 5:5-9; 13:12-15; 1 Pet. 2:21) Kodi tingasonyeze bwanji mtima wodzipereka, ndipo ndi madalitso otani amene tidzalandire?

3. Kodi mtima wodzipereka umathandiza bwanji pa misonkhano ya mpingo?

3 Pothandiza Abale Athu: Tingagawire ena “mphatso . . . yauzimu” mwa kudzipereka kuyankha pa misonkhano pa nkhani zofunika kuti omvera ayankhepo. (Aroma 1:11) Kuyankha kumalemekeza Yehova, kumakhomereza choonadi kwambiri m’maganizo ndi mu mtima mwathu, ndipo kumatichititsa kusangalala ndi misonkhano. (Sal. 26:12) Tingadziperekenso kukamba nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu pakakhala kuti pakufunika munthu woti alowe m’malo mwa munthu wina. Zimenezi zingatithandize kupititsa patsogolo luso lathu la kuphunzitsa.

4. Kodi njira zina zomwe tingasonyezere mtima wodzipereka ndi ziti?

4 Abale angasonyeze mtima wodzipereka mwa kukalamira maudindo mu mpingo. (Yes. 32:2; 1 Tim. 3:1) Tonse tingathandize kuti misonkhano yadera ndi yachigawo iyende bwino mwa kudzipereka kugwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana. Tikadzipereka kupitira limodzi ndi woyang’anira woyendayenda mu utumiki kapena kumusamalira pankhani ya chakudya, tikhoza ‘kulimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Tikadzipereka kuthandiza ana amasiye, akazi amasiye, anthu odwala ndi ofooka, amayi a ana ang’onoang’ono, ndi anthu ena mu mpingo, timasangalala ndiponso Yehova amatiyanja.—Miy. 19:17; Mac. 20:35.

5. Kodi ndi ntchito ziti zokhudzana ndi Nyumba ya Ufumu zimene zimafuna anthu odzipereka?

5 Njira ina yomwe tingaperekere nthawi ndi mphamvu zathu ndiyo kuthandiza nawo kuyeretsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu. Komanso, chifukwa choti anthu ambiri akuphunzira choonadi, pakufunika Nyumba za Ufumu zatsopano zambiri, ndiponso anthu ambiri odzipereka kugwira ntchito yomangayi. Mwamuna wina ndi mkazi wake anadzipereka kuthandiza Komiti Yomanga Yachigawo yakwawo ngakhale kuti sankadziwa ntchito yomanga. M’kupita kwa nthawi, anaphunzitsidwa ntchitoyo ndipo panopa amathandiza nawo kumanga. Mkaziyo anati: “Kugwirira ntchito limodzi ndi anthu ena kwandithandiza kupeza mabwenzi apamtima. Tikamaweruka, timakhala otopa koma otsitsimulidwa mwauzimu.”

6. N’chifukwa chiyani kulalikira kuli ntchito yongodzipereka yofunika kwambiri imene tingachite?

6 mwa Kulalikira: Ntchito yongodzipereka yofunika kwambiri imene tingachite masiku ano ndi yolalikira za Ufumu. Anthu akathandizidwa kumvetsa ndi kutsatira malangizo a m’Baibulo, amayamba kukhala ndi cholinga m’moyo n’kupeza mphamvu zothetsera zizolowezi zoipa. Amaphunzira za chiyembekezo cholimbikitsa cha m’Baibulo chonena za m’tsogolo. Mwa kuphunzitsa anthu Baibulo, timakhala tikugwira ntchito yongodzipereka yosangalatsa imene imabweretsa madalitso osatha. (Yoh. 17:3; 1 Tim. 4:16) Mwina, malinga ndi mmene zinthu zilili pamoyo wathu, tikhoza kuchita zochuluka mu ntchito imeneyi mwa kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika, kusamukira ku dera limene kukufunika thandizo, kapena kuphunzira chinenero china.

7. N’chifukwa chiyani kudzipereka kuli kofunika kwambiri masiku ano?

7 Mfumu Davide inaneneratu kuti panthawi imene Mesiya adzayambe kulamulira, anthu a Mulungu “adzadzipereka eni ake.” (Sal. 110:3) Popeza Yehova akufulumizitsa ntchito yomaliza yotuta mwauzimu, pali ntchito zambiri zimene tingagwire mongodzipereka. (Yes. 60:22) Kodi mwanena kuti: “Ndine pano; munditumize ine”? (Yes. 6:8) Zoonadi, mwa kusonyeza mtima wodzipereka, timakondweretsa Yehova ndi kupindula kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena