Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/09 tsamba 7
  • Kodi Mungawonjezere Zimene Mumachita mu Utumiki?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungawonjezere Zimene Mumachita mu Utumiki?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 7/09 tsamba 7

Kodi Mungawonjezere Zimene Mumachita mu Utumiki?

1. Kodi n’chiyani chikufunika mwamsanga mu utumiki wakumunda, nanga n’chifukwa chiyani?

1 Ataona kuti anthu ambiri anali ndi chidwi ndi uthenga wabwino wa Ufumu, Yesu analangiza ophunzira ake ‘kupempha Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.’ (Mat. 9:37, 38) Popeza kuti tili kumapeto kwa nthawi yokolola, ntchito yathu ndi yofunika kuigwira mwachangu kwambiri kuposa kale. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kupemphera ndi kuganizira zimene tingachite kuti tizilowa mu utumiki wakumunda nthawi zonse.—Yoh. 14:13, 14.

2. Kodi ena achita chiyani pomvera pempho loti pakufunika antchito ambiri m’munda?

2 Zimene Mungachite Kuti Muwonjezere Utumiki: Anthu ambiri akwanitsa kuchita upainiya mothandizidwa ndiponso motsogoleredwa ndi Yehova. (Sal. 26:2, 3; Afil. 4:6) Ena amayesetsa mwapadera kuchita upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo pachaka. Imeneyi ndi njira yabwino kwambiri yowonjezera zimene amachita mu utumiki. Ndipo ambiri aganiza zoyamba upainiya wokhazikika chifukwa choti anasangalala kwambiri ndi upainiya wothandiza.—Mac. 20:35.

3. Ngati mbuyomu munachitapo upainiya, kodi panopo mungaganizire zochita chiyani?

3 Kodi Mungayambirenso Upainiya?: Ngati mbuyomu munachitapo upainiya, n’zosakayikitsa kuti mumasangalala mukakumbukira zimene munkachita nthawi imeneyo. Kodi munayamba mwapemphera n’kuganizira ngati mungathe kuyambiranso upainiya? N’kutheka kuti mavuto amene anakuchititsani kusiya upainiya anatha ndipo panopo mungayambirenso kuchita utumiki umenewu.—1 Yoh. 5:14, 15.

4. Kodi tonsefe tili ndi mwayi wapadera uti?

4 Ntchito yokolola ili mkati ndipo itha posachedwapa. (Yoh. 4:35, 36) Choncho, tonsefe tiyenera kuona mmene zinthu zilili pamoyo wathu kuti tione ngati tingasinthe zina ndi zina n’cholinga choti tiwonjezere zimene timachita mu utumiki wakumunda. Koma ngati taona kuti sitingathe kuchita zimenezi, kodi pali zimene tingachite kuti tizilalikira mogwira mtima mu utumiki? (Maliko 12:41-44) Umenewutu ndi mwayi wapadera kwambiri kwa anthu amene panopo moyo wawo ukuwalola kuti Yehova awagwiritsire ntchito mu utumiki wapaderawu.—Sal. 110:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena