Msonkhano Wachigawo wa mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
1 Programu ya msonkhano wachigawo chaka chino idzatithandizadi kusunga mtendere wathu waumulungu, ndipo idzafotokoza mbali yathu pa kuthandiza ena kupeza mtendere wotere. Mogwirizana ndi chilengezo cha mu Utumiki Wathu Waufumu wa March 1996, mutu wake ndiwo “Amithenga a Mtendere Waumulungu.” Kodi mwapanga makonzedwe anu kuti musaphonye programu iliyonse?
2 Programu ya Masiku Atatu: Tikudziŵa kuti mudzasangalaladi ndi msonkhano wachigawo wa chaka chino ndipo mudzabwerera kunyumba ndi nyonga yatsopano. (2 Mbiri 7:10) Chaka chino tidzakhalanso ndi programu ya masiku atatu. Kodi mwapanga kale makonzedwe kuti mukapemphe nthaŵi kuntchito yolembedwa kotero kuti mukakhalepo nthaŵi yonse?
3 Utumiki Wathu Waufumu wa March 1996 uli ndi mndandanda wa deti ndi malo a misonkhano 13 m’gawo la nthambi ya Malaŵi. Pa tsopano lino mlembi wa mpingo wanu akudziŵitsani za umene mwagaŵiridwako. Misonkhanoyi idzachitidwa m’Chicheŵa ndi Chingelezi pamalo olinganizidwa.
4 Pamasiku onse atatu programu idzayamba pa 9:30 a.m. ndi kutha pa Sande pafupifupi 4:00 p.m. Kodi tidzasonyeza chifundo kwa abale athu achikulire ndi opuwala mwa kuwasiyira mipando pamalo abwino kwambiri? Kumbukirani kuti “chikondi . . .sichitsata za mwini yekha.”—1 Akor. 13:4, 5; Afil. 2:4.
5 Kodi Mudzanoledwa? Pambuyo pa kugwira mawu Miyambo 27:17, “Chitsulo chinola chitsulo,” Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, inati: “Tili ngati zipangizo zimene zimafunikira kunoledwa nthaŵi zonse. Popeza kuti kukonda Yehova ndi kupanga zosankha zozikidwa pa chikhulupiriro chathu kumatanthauza kukhala osiyana ndi dziko, nthaŵi zonse tiyenera kuchita zinthu zosiyana ndi anthu onse.” Kodi ndi motani mmene tingagwiritsirire ntchito uphungu umenewo?
6 Tili osiyana ndipo tiyenera kukhalabe osiyana ndi dziko. Kuyesetsa kosalekeza kwa kukwaniritsa zimenezi kuyenera kupitiriza kuti tikhalebe achangu pantchito zokoma. (Tito 2:14) Nchifukwa chake nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yogwidwa mawu pamwambapo inapitiriza kunena kuti: “Pamene tili ndi ena amene amakonda Yehova, timanolana—timafulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.” Msonkhano wachigawo ndiwo amodzi a makonzedwe ochokera kwa Yehova otithandiza kukhalabe akuthwa mwauzimu. Sitiyenera kuphonya mbali iliyonse ya programuyo.
7 Munthu Wanzeru Adzamvetsera: Kumvetsera ndiko luso limene liyenera kukulitsidwa. Kwanenedwa kuti munthu wamba amakumbukira kokha pafupifupi theka la zimene wamva—kaya aganize kuti anamvetsera mosamalitsa kotani. Popeza tikukhala m’nthaŵi yokhala ndi zochenjeneketsa, nthaŵi zina tingavutike kusumika maganizo athu pankhani kwa nthaŵi yaitali. Kodi tingayese kuwonjezera nthaŵi ya kutchera kwathu khutu, makamaka pamene tili pakati pa anthu ambiri amene akumvetsera wina amene akulankhula? Ngati munapemphedwa kupereka chidule cha programu ya tsiku lililonse mutabwerera kunyumba, kodi mungathe kutero? Kodi ndi motani mmene tonsefe tingawongolere kukhoza kwathu kwa kumvetsera ndi kutchera khutu mosamalitsa ku mbali iliyonse imene ili pa programu ya msonkhano?
8 Chikondwerero chachikulu nchofunika, popeza mphatso yaumulungu ya kukumbukira singagwire bwino ntchito popanda chimenecho. Mwachitsanzo, pamene munthu asonyeza chikondwerero chowonjezereka pa nkhani ina, ndi pamenenso samavutika kwambiri kukumbukira nsonga zazikulu za nkhani kapena mbali ya programu. Komabe, zambiri zimadalira pa kutchera kwathu khutu koposa pa zinthu zimene tili ndi mwaŵi kuzimva pamsonkhano wachigawo. Chikondwerero chathu chachikulu ndi kutchera kwathu khutu ku mbali iliyonse ya programu ya msonkhano zili ndi chiyambukiro pa mkhalidwe wathu wauzimu watsopano lino limodzinso ndi pa ziyembekezo zathu zamtsogolo. Pamisonkhano timaphunzitsidwa njira za Yehova ndipo timapatsidwa malangizo kaamba ka kukwaniritsa ntchito yopulumutsa moyo. (1 Tim. 4:16) Dzilingalireni kukhala chombo m’nyanja yoŵinduka ndi namondwe. Malonjezo a Yehova ndiwo namgula wolimba wa chiyembekezo. Ngati munthu samatchera khutu ku maprogramu achikristu ndipo amalola malingaliro ake kutengekatengeka, angaphonye mfundo zofunika kwambiri za uphungu ndi malangizo zimene zingamtetezere pa kusweka kwauzimu monga chombo.—Aheb. 2:1; 6:19.
9 M’mbali zambiri za dziko, abale athu amayesetsadi kupezeka pamisonkhano. Nkochititsa chidwi kuona kutchera kwawo khutu kosamalitsa pamisonkhano yachigawo. Ngakhale zili choncho, kumalo ena anthu ena achenjeneketsa ena mwa kuyendayenda pamalo a msonkhano mkati mwa maprogramu. Ena amabwera mochedwa. Pamisonkhano ina yakumbuyoku, kunali kovuta kumvetsera mphindi zingapo zoyambirira za programu chifukwa cha ambiri amene anali kuyendayenda m’makonde ndi kumbuyo kwa malo okhala. Nthaŵi zambiri ameneŵa samakhala abale okhala ndi ntchito kapena amayi amene akusamalira ana awo aang’ono. Msokonezo wochuluka umachokera kwa anthu amene akungocheza. Chaka chino, Dipatimenti ya Akalinde idzapereka chisamaliro chachikulu pa vutoli, ndipo tikhulupirira onse adzakhala atakhala pansi pamene tcheyamani atipempha kuchita motero. Kumvera kwanu pankhaniyi kudzayamikiridwa kwambiri.
10 Kodi ndi njira zogwira ntchito ziti zimene zidzatithandiza kukhala otchera khutu kwambiri ku programu ya msonkhano ndi kukumbukira zambiri za zimene zalankhulidwa? Zimene zalankhulidwa m’zaka za kumbuyoku ziyenera kubwerezedwa: (a) Sumikani maganizo pa chifukwa chachikulu chopitira kumzinda wa msonkhano. Sindicho kukasanguluka, koma kukamvetsera ndi kuphunzira. (Deut. 31:12) Yesani kupuma mokwanira usiku uliwonse. Kuimba mpaka usiku kwambiri sikoyenera. Ngati mwabwera kumsonkhano muli wotopa kwambiri, kusumika maganizo kudzakhala kovuta. (b) Dzipatseni nthaŵi yabwino ya kuimika galimoto lanu ndi kukhala pansi programu isanayambe. Kuthamangira kumipando m’mphindi yothera kaŵirikaŵiri kudzakuchititsani kuphonya mbali ina yoyamba. (c) Lembani manotsi achidule a mfundo zazikulu. Kulemba manotsi kopambanitsa kungawonongetse kumvetsera kwabwino. Pamene mukulemba, tsimikizirani kuti simukuphonya mfundo zina chifukwa cha kusumika maganizo pa manotsi anu. (d) Pamene mbali ya msonkhano idziŵitsidwa, iyembekezereni mwachidwi. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingaphunzirenji pa mbali iyi chimene chidzakulitsa chiyamikiro ndi chikondi changa pa Yehova? Kodi ndi motani mmene uthengawu ungandithandizire kusonyeza kwambiri umunthu watsopano? Kodi zimenezi zidzandithandiza motani kuwongolera utumiki wanga?’
11 Khalidwe Limene Limakometsera Utumiki Wathu: Paulo analimbikitsa Tito kudzisonyeza kukhala “chitsanzo cha ntchito zabwino.” Mwa kusonyeza kupanda chinyengo m’kuphunzitsa kwake, Tito anatha kuthandiza ena ‘kukometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’ (Tito 2:7, 10) Chaka chilichonse, timalandira zikumbutso zokoma mtima ponena za chifukwa chimene khalidwe laumulungu lililidi lofunika pamene tikupita kumsonkhano ndi kubwerako, ndi pamenenso tili kumalesitilanti ndi pamsonkhano penipenipo. Chaka chatha tinamvanso ndemanga zina zosangalatsa zimene tikufuna kugaŵana nanu.
12 Manijala wa hotela ina anati: “Nthaŵi zonse kumakhala kokondweretsa kupatsa malo Mboni chifukwa zili zodekha, zogwirizanika, ndipo zimayang’anira ana awo mosamalitsa.” Kalaliki wina wa m’hotela ananena kuti ntchito yake imakhala “yopepuka kwenikweni pamene Mboni ziloŵa ndi kutuluka m’hotela chifukwa, mosasamala kanthu kuti zimaimirira pamzere, izo nthaŵi zonse zimakhala zaulemu, zodekha, ndi zomvetsetsa.” Mkazi wina ku New England anakondwera kwambiri ndi khalidwe la achichepere a Mboni amene anali kukhala pa motela imodzimodziyo kwakuti anapempha mabuku ena onena za gulu lathu.
13 Ngakhale kuti utumiki wa zakudya unalekeka pamisonkhano yathu, padakali zotayidwa zambiri zoloŵetsedwa pa kuchita lendi malo, ndi kusamalira nkhani zosiyanasiyana. Zopereka zathu zodzifunira zimasamalira zowonongedwa zimenezi. Mlongo wina wokhala ndi ana achichepere anabwera kumsonkhano ndi ndalama zochepa. Komabe, iyeyo ndi ana ake anathandizabe ndi chopereka chaching’ono. Zimene aliyense wasankha kuchita pa zimenezi ili nkhani yaumwini, koma tikudziŵa kuti mumayamikira zikumbutso zotere.—Mac. 20:35; 2 Akor. 9:7.
14 Odziŵika ndi Mavalidwe Athu: Mavalidwe athu amavumbula zambiri ponena za ifeyo ndi malingaliro athu kulinga kwa ena. Achichepere ochuluka ndi achikulire ambiri amakonda mavalidwe a masitayelo ndi osasamala kusukulu kapena kuntchito kwawo. Chaka chilichonse masitayelo amavalidwe amakhala onkitsa mowonjezereka, ngakhale ochititsa kakasi. Ngati sitili osamala, tingasonkhezeredwe mosavuta ndi mabwenzi akudziko kuvala monga mmene amavalira. Masitayelo ambiri ngosayenerera kuvala pamisonkhano ya kulambira. Kalata imene inalandiridwa pambuyo pa umodzi wa misonkhano yachaka chatha inafotokoza chiyamikiro kaamba ka programuyo koma inawonjezera kuti: “Ndinadabwa chifukwa chimene panalili atsikana ambiri okhala ndi madiresi aafupi chotero, mabulauzi otseguka kwambiri, ndi masiliti aatali.” Mosakayikira tonsefe timakhumba kuvala m’njira yoyenerera atumiki achikristu pamisonkhano ndiponso pamene tikucheza pambuyo pa msonkhano. Panthaŵi zonse timachita bwino kukumbukira uphungu wa mtumwi Paulo kwa Akristu wa kuvala “chovala [chokonzeka bwino ndi ulemu, NW] ndi chidziletso.”—1 Tim. 2:9.
15 Kodi ndani amene ayenera kunena chimene chili chovala chaulemu, “chokonzeka bwino”? Kukhala waulemu kumatanthauza kukhala “wosapambanitsa kapena wosadzigangira.” Dikishonale ikufotokozanso ulemu kukhala “wosadzionetsera.” Sosaite kapena akulu sangaike malamulo ponena za kavalidwe ndi kapesedwe. Ngakhale zili choncho, kodi masitayelo amene mosakayikira saali aulemu kapena abwino sayenera kuoneka mosavuta kwa Mkristu? (Yerekezerani ndi Afilipi 1:10.) Kapesedwe ndi kavalidwe kathu siziyenera kuchenjeneketsa ena mosayenera. Maonekedwe athu ayenera kukhala okondweretsa, osati akudziko kapena okhumudwitsa. Monga atumiki a uthenga wabwino, kukhala kwathu ovala ndi opesa moyenerera mkati mwa nthaŵi pamene tili mumzinda wamsonkhano kumadzetsa ulemu kwa Yehova ndipo kumasonyezanso bwino za gulu lathu. Chotero, makolo adzapereka chitsanzo ndipo adzatsimikizira kuti ana awo avala moyenerera kaamba ka chochitikacho. Akulu adzayenera kupereka chitsanzo chabwino ndi kukhala okonzeka kupereka uphungu wachikondi ngati nkofunika.
16 Makamera, Makamera a Vidiyo ndi Matepirikoda: Nkololeka kugwiritsira ntchito makamera ndi ziŵiya zina zojambulira, malinga ngati tiganizira ena amene alipo. Ngati tiyendayenda kujambula zithunzi mkati mwa maprogramu, sitidzangochenjeneketsa ena amene akuyesa kumvetsera koma ifenso tidzaphonya mbali ina ya programuyo. Nthaŵi zambiri timapindula kwambiri pamsonkhano mwa kutchera khutu mosamalitsa kwa alankhuli ndi kulemba manotsi oyenerera. Tingamajambulire mbale kapena mlongo amene ali wobindikiritsidwa m’nyumba; komabe, ngati tikufuna kukazigwiritsira ntchito ife eni, tingapeze kuti titabwerera kunyumba pambuyo pojambula maola ambiri a programu, sitidzakhala ndi nthaŵi yabwino yopenda zambiri za zimene tinajambula. Palibe ziŵiya zojambulira zilizonse zimene ziyenera kugwirizanitsidwa ku magetsi kapena ku zolankhuliramo, ndiponso ziŵiya siziyenera kutseka njira za pakati pamipando, malikole, kapena kuchinga ena.
17 Mipando: Tikupitirizabe kuona kuwongolera pankhani ya kusunga mipando. Chaka chatha, ambiri a inu anatsatira malangizo akuti: MIPANDO INGASUNGIDWIRE A M’BANJA LANU OKHA NDI ALIYENSE AMENE MUNGANYAMULE M’GALIMOTO LANU. Muyenera kuti munaziona kukhala zosapsinja kwenikweni chifukwa ambiri anali kutsatira malangizo omvekera ameneŵa. Chofunika kwambiri, kumvera kwanu zimenezi kunali kokondweretsa kwa Yehova ndi kwa “kapolo wokhulupirika,” amene amapereka chakudya chauzimu.—Mat. 24:45.
18 Pali chiŵerengero chomakula cha abale athu amene akudwala. Ena amabwera kumsonkhano panjinga za opunduka ndipo achibale amafunikira kuwasamalira. Ena ali pa chisamaliro cha mankhwala osiyanasiyana kaamba ka matenda osatha onga matenda a mtima, kapena kukomoka. Kumatisangalatsadi kuona abale ndi alongo okondedwa ameneŵa pamsonkhano wachigawo, ali otsimikizira kusaphonya chilichonse cha zakudya zauzimu. Komabe, nthaŵi zina, pakhala vuto la anthu ena amene adwala mkati mwa msonkhano, osakhala ndi achibale kapena a mumpingo aliwonse owathandiza. Panthaŵi zina oyang’anira msonkhano anafunikira kuitanitsa utumiki wofulumira wa zamankhwala kuti apereke mbale kapena mlongo kuchipatala. Thayo la kusamalira odwala matenda osatha liyenera kukhala kwakukulukulu pa a m’banja ndi achibale apafupi. Dipatimenti ya Chipatala ya msonkhano wachigawo siingasamalire odwala matenda osatha. Ngati wa m’banja lanu afunikira chisamaliro chapadera, chonde tsimikizirani kuti sakusiyidwa yekha mwinamwake angafune thandizo lamwamsanga. Ndiponso, pamisonkhano yachigawo sipadzakhala makonzedwe a zipinda zapadera zokhalamo amene amadwala matenda amene samawalola kukhala pamalo a anthu onse. Akulu adzayenera kukhala atcheru kwa aliyense wamumpingo wawo amene ali ndi matenda ndi kutsimikizira kuti makonzedwe apangidwa pasadakhale kaamba ka chisamaliro chawo.
19 Zakudya Zofunika Pamsonkhano Wachigawo: Ndemanga zambiri zabwino zanenedwa ponena za mapindu a kunyamula zakudya zathu. Mbale wina analemba kuti: “Ndikuona bwinobwino phindu lalikulu lauzimu kuchokera pa zimenezi. Nthaŵi yonseyo ndi nyonga tsopano zingalunjikitsidwe pa zinthu zauzimu. Sindinamvepo ndemanga yotsutsa iliyonse.” Mlongo wina analemba kuti: “Mwa kupereka chitsanzo, abalenu okondedwa mukutilimbikitsa monga Mkristu aliyense payekha kudzisanthula ndi kufunafuna njira zopeputsira moyo wathu ndi kuchulukitsa ntchito yathu yateokrase.” Woyang’anira woyendayenda wina analemba ponena za makonzedwe akale a utumiki wa chakudya kuti: “Makonzedwe akale anachititsa chiŵerengero chachikulu ndithu cha abale kuphonya programu yonse ya msonkhano.” Ponena za chakudya chimene abale ananyamula, mkulu wina analemba kuti: “Anali ndi zimene anafuna, ndipo sanafunikire kukhala pamzere kuziyembekezera.” Pomalizira, mlongo wina analemba kuti: “Pambuyo pa programu panali bata ndiponso panalibe phokoso ndipo panali mzimu wachisangalalo.” Inde, aliyense anatha kunyamula zokwanira zompatsa nyonga kwa nthaŵi yonse yamasana. Ambiri ananena kuti anali ndi nthaŵi yowonjezereka yocheza ndi mabwenzi.
20 Sipadzakhalanso utumiki wa chakudya chaka chino. Mungatenge mphindi zingapo kupenda mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa July 1995, ndime 25, kaamba ka malingaliro a zakudya zopatsa thanzi zimene mungapite nazo kumsonkhano. Chonde kumbukirani, moŵa suyenera kubweretsedwa pamalo a msonkhano. Ngati zoziziritsira zazing’ono nzofunika, ziyenera kukwanira pansi pa mpando wanu. Kumbukirani kuti pali nthaŵi yokwanira yakupuma masana ya kudya ndi kumwa zimene mwanyamula. Monga pa Nyumba zathu za Ufumu mkati mwa misonkhano, timapeŵa kudya mkati mwa maprogramu a msonkhano wachigawo nthaŵi zonse. Motero timasonyeza ulemu kaamba ka makonzedwe a kulambira ndi a chakudya chauzimu choperekedwa.
21 Posachedwapa yoyambirira ya Misonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu” idzayamba. Kodi mwamaliza makonzedwe anu a kupezekapo, ndipo kodi tsopano muli wokonzeka kusangalala ndi masiku atatu a kuyanjana kwachimwemwe ndi zinthu zabwino zauzimu? Pemphero lathu lochokera pansi pa mtima ndi lakuti Yehova adalitse zoyesayesa zanu za kufika pamsonkhano wachigawo chilimwe chino.
[Bokosi patsamba 6]
Zikumbutso za pa Msonkhano Wachigawo
Ubatizo: Opita kuubatizo ayenera kukhala pamalo amene adzapatsidwa programu isanayambe pa Loŵeruka mmaŵa. Kwaonedwa kuti ena amavala mtundu wa zovala zosapatsa ulemu ndi zimene sizimapatsa chithunzi chabwino cha chochitikacho. Aliyense amene akufuna kubatizidwa ayenera kunyamula zovala zosambira zaulemu ndi thaulo. Akulu a mpingo ofunsa mafunso opita kuubatizo mu buku la Uminisitala Wathu adzayenera kutsimikizira kuti aliyense wamvetsa mfundozi. Pambuyo pa nkhani yaubatizo ndi pemphero loperekedwa ndi mlankhuli, tcheyamani wa programuyo adzapereka malangizo achidule kwa opita kuubatizo ndiyeno adzaitanitsa nyimbo. Nyimboyo itatha, akalinde adzatsogolera opita kuubatizo kumalo omizira. Popeza ubatizo wosonyeza kudzipatulira kwa munthu mwini uli nkhani yaikulu ya munthu mwini ndi Yehova, palibe makonzedwe a otchedwa kuti maubatizo a paubwenzi pamene anthu aŵiri kapena oposapo amakupatirana kapena kugwirana manja pamene akubatizidwa.
Mabaji: Chonde valani mabaji a 1996 pamsonkhano wachigawo ndi popita kumalo amsonkhano ndi pobwerako. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimatitheketsa kupereka umboni wabwino pamene tili paulendo. Muyenera kugula mabaji ndi zoikamo zake kumpingo, popeza sizidzakhalapo pamsonkhano wachigawo. Musayembekezere mpaka kutatsala masiku ochepa msonkhano usanafike kuti mufunsire baji lanu ndi mabaji a banja lanu. Kumbukirani kunyamula khadi lanu latsopano la Advance Medical Directive/Release.
Utumiki Wodzifunira: Posakhalanso ndi utumiki wa chakudya, ambiri amene kale ankagwira ntchito m’dipatimenti imeneyo tsopano angasankhe kudzipereka kuntchito zina. Kodi mungapatule nthaŵi ina pamsonkhano kuti muthandize mu imodzi ya madipatimenti? Kutumikira abale athu, kwa maola angapo okha, kungakhale kothandiza kwambiri ndi kokhutiritsa kwambiri. Ngati mungathandize, chonde pitani ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira pamsonkhanopo. Ana osakwanitsa zaka 16 angathandize kwambiri mwa kugwira ntchito pansi pa uyang’aniro wa kholo kapena wachikulire wina wosamala.
Mawu a Chenjezo: Khalani atcheru ku mavuto amene angabuke kuti mupeŵe zovuta zosafunikira. Kaŵirikaŵiri mbala ndi anthu ena opanda makhalidwe abwino amakonda kuukira anthu amene ali kutali ndi kwawo. Tsimikizirani kuti galimoto lanu nlokiya nthaŵi zonse, ndipo musasiye chilichonse choonekera chimene chingachititse wina kuthyola. Mawu a chenjezowa akugwiranso ntchito kwa eni njinga. Mbala zimafuna pamene pali anthu ambiri. Sikungakhale kwanzeru kusiya zinthu zilizonse zamtengo wapatali pampando wanu. Simungadziŵe kuti aliyense amene ali pafupi nanu ndi Mkristu. Nkuperekeranji chiyeso? Nkhani zamveka zakuti anthu ena akunja amafuna kuba ana mwa kuwanyengerera. YANG’ANIRANI ANA ANU NTHAŴI ZONSE.