Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
▪ Ubatizo: Oyembekezera kubatizidwa ayenera kudzakhala pamalo amene adzawakonzera programu isanayambe Loŵeruka mmaŵa. Yense amene akufuna kubatizidwa adzapite ndi chovala chaulemu ndi thaulo. Munthu akamasonyeza mwa ubatizo kuti anadzipatulira, imeneyo ndi nkhani ya pakati pa munthuyo ndi Yehova. Si koyenera kuti obatizidwawo akumbatirane kapena kugwirana manja pobatizidwa.
▪ Mabaji: Muzivala mabaji a 1998 nthaŵi zonse pamene muli mumzinda wa msonkhano ndi pamenenso mukupita ndi pobwerako. Zimenezo nthaŵi zambiri zimatsegula mipata yoti tichitire umboni wabwino. Mungapeze mabaji ndi mapulasitiki ake kudzera mumpingo mwanu, popeza kuti sadzakhalako kumsonkhano. Kumbukirani kumanyamula khadi lanu latsopano la Advance Medical Directive/Release.
▪ Makamera, Mavidiyokamera, ndi Mawailesi akaseti: Makamera ndi zina ziŵiya zojambulira zingagwiritsiridwe ntchito pamisonkhano. Komabe, kuyendayenda mukumatenga zithunzi maprogramu ali mkati kungadodometse ena amene akuyesa kumvetsera programu. Ziŵiya zilizonse zojambulira zisalumikizidwe kumagetsi kapena ku zokuzira mawu.
▪ Kulipirira Zinthu Zowonongedwa Pamsonkhano: Nthaŵi zonse Sosaite imalamula kuti “mipando njaulere, tisayendetse mbale” pamisonkhano. Nangano, kodi ndalama zopangira hayala ndi zinthu zina zofunika zidzachokera kuti? Anthu opezekapowo ndiwo amapereka ndalama mooloŵa manja. Tikutsimikizira kuti mudzasonyeza mzimu wakuoloŵa manja wonga umene unasonyezedwa ndi atumiki a Mulungu akale potsanzira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (2 Akor. 8:7) Ndalama zoperekedwazo zimasungidwa bwino kwambiri, zimalembedwanso m’buku, ndi kuzigwiritsira ntchito yofunikira.
▪ Chipatala: Dipatimenti ya Chipatala nja matenda a mwadzidzidzi basi. Mungatenge maaspirin anu, mankhwala am’mimba, mabanditchi, mapini, ndi zina zoterozo, chifukwa zinthu zimenezo sizidzapezeka pamsonkhano. Nkosatheka kusamala anthu odwala matenda ofuna dokotala.
▪ Chakudya: Munthu aliyense wopezekapo ayenera kubwera ndi chakudya chakechake m’malo moti atuluke panja masana kukagula kanthu kena. Chakudya chopatsa thanzi chosavuta kunyamula chingakwanire. Tiyenera kukasamala ndi mabotolo ndi zinthu zina zamagalasi. Moŵa sumaloledwa pamalo a msonkhano. Ena mwa omvetsera aonedwapo akudya ndi kumwa programu ili mkati. Zimenezo zimasonyeza kupanda ulemu.
▪ Nthaŵi ya Maprogramu: Monga momwe mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa March 1998 unalengezera, programu idzayamba pa 8:45 a.m. ndi kutha pa 4:50 p.m. tsiku lililonse.
▪ Utumiki Wodzifunira: Kodi mungapatule nthaŵi pamsonkhano ya kuthandiza m’dipatimenti ina? Kutumikira abale anu, ngakhale kwa maola oŵerengeka chabe kungathandize kwambiri ndipo kungakupindulitseni ndithu. Ngati mukhoza kuthandiza, fikani ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira pamsonkhano. Ana osafika zaka 16 nawonso akhoza kuthandiza mwa kugwira ntchito moyang’aniridwa ndi kholo kapena wachikulire wina.
▪ Mawu Ochenjeza: Tsimikizirani kuti galimoto yanu ili yokhomedwa nthaŵi zonse, ndipo musasiye kanthu kalikonse koonekera kamene kangakope mbala. Mbala ndi opisa anzawo m’matumba amafuna pamene pali anthu ambiri. Sikungakhale kwanzeru kusiya zinthu zamtengo wapatali pamalo anu okhala. Simungatsimikize kuti aliyense amene ali pafupi nanu ndi Mkristu. Nkuperekeranji chiyeso? Talandira malipoti onena za anthu akunja amene ayesa kuba ana. YANG’ANIRANI ANA ANU NTHAŴI ZONSE.
Pepani musaimbire foni kapena kulembera kalata kwa amanijala a malo a msonkhano, nimufunsa nkhani zokhudza msonkhano. Ngati zimene mukufuna kudziŵazo akulu sangakuuzeni, ingolemberani ku komiti yamsonkhano, mugwiritsire ntchito adresi imene ili pamakalata amene mpingo wanu unalandira.