Msonkhano Wachigawo Wakuti “Mantha Aumulungu” wa 1994
1 Amuna achikhulupiriro asonyeza “mantha aumulungu” kuyambira mu nthaŵi ya Abele ndi ya Nowa kufikira tsopano lino. (Aheb. 11:4, 7, NW) Kusonyeza mantha aumulungu kumatanthauza kusonyeza “mantha ndi ulemu waukulu kwa Mlengi ndi kuwopa koyenera kwa kusamkondweretsa.” (it-1 tsa. 818) Mkati mwa August ndi September, tidzasonyeza ulemu waukulu umenewu mwa kufika kwathu pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Mantha Aumulungu.” Kodi mudzakhalapo kuti mudzasangalale ndi programu yonse, kuyambira pa nyimbo yotsegulira mpaka pa pemphero lomaliza?
2 Chaka chilichonse timakonzekera msonkhano wachigawo ndi chiyembekezo champhamvu. Ngakhale kuti kuyesayesa kokulirapo kwaumwini ndi ndalama zingaloŵetsedwemo, madalitso ake oti adzalandiridwe ndi ambiri. Timabwerera kwathu ndi chisangalalo, okhutira ndi omangiriridwa mwauzimu. (Yerekezerani ndi 1 Mafumu 8:66.) Mayanjano ake ndi otsitsimula, ndipo msonkhanowo umapereka njira zatsopano. Koma kumbukirani, timasonkhana kuti tilambire Yehova. Iye amatilamulira kuchita motero. Akutiphunzitsa mmene tingapindulire ife eni.—Deut. 31:12, 13; Sal. 122:1.
3 Msonkhano Wamasiku Atatu: Programuyo idzaperekedwa pamisonkhano 49 m’Zambia chaka chino. Kuwonjezera pa Wachingelezi, misonkhano idzakhalako m’Chibemba, Chicheŵa, Chiluvale, Chitonga, ndi Silozi.
4 Programu yake idzayamba pa tsiku loyamba ndi 9:20 a.m. ndipo idzamalizidwa pa tsiku lomaliza pafupifupi 4:15 p.m. Pa tsiku lachiŵiri, programu idzayamba pa 9:00 a.m. ndipo pa tsiku lomaliza, magawo adzayamba pa 9:30 a.m.
5 Ulemu Waukulu kwa Yehova Umatisonkhezera Kufikapo: Paulo analangiza Akristu Achihebri ‘kutumikira Mulungu ndi kumchitira ulemu ndi mantha [aumulungu, NW].’ (Aheb. 12:28) Msonkhano wathu wachigawo wa chaka chino wakonzedwa kutithandiza kuti tichite zimenezo kumene. Tingakumane ndi zopinga zina zimene zingayese kutsimikiza mtima kwathu kwa kufikapo. Izo zingaoneke monga mapiri, koma mothandizidwa ndi Yehova zimenezi zikhoza kugonjetsedwa. (Mat. 17:20) Ngati muli wosakhoza kulinganiza tchuti chanu kuti chidzaphatikizepo masiku a msonkhano wonse, pa tsiku loyamba mmaŵa mpaka pa tsiku lomaliza masana, kodi mwafikira wokulembani ntchito wanu mwapemphero kuti mupemphe nthaŵiyo? (Yak. 1:6-8) Ana a usinkhu wopita kusukulu amene adzafunikira kufika pa umodzi wa misonkhano yoyambirira sukulu isanatsekeredwe ayenera kudziŵitsa aphunzitsi awo mwaulemu kuti sadzapezeka kusukulu chifukwa cha mbali yofunika imeneyi ya kulambira kwawo kwachipembedzo.
6 Gwiritsirani Ntchito Bwino Chumacho: Kodi chumacho nchiyani? Nthaŵi ndi kuyesayesa zimene zimatheredwa pamsonkhano. Kungakhale kopanda nzeru kupanga makonzedwe osamalitsa a kufika pamsonkhano wachigawo wa chaka chino ndi kungobwerera kwanu pa tsiku lomaliza madzulo mutaphonya mbali yaikulu ya programuyo. Kodi mungachoke pakati pa phwando kotero kuti mukasamalire zinthu zina? Komabe, kukula kwathu kwauzimu ndi mantha aumulungu siziyenera kutilola kuphonya kanthu kalikonse kamene Yehova watikonzera.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 2:9, 10.
7 Ambiri a ife mwinamwake sitingaganize zochokapo mwamsanga. Komabe, tikhoza kuphonya mbali yokulirapo ya programuyo. Kodi zimenezi zingachitike motani? Mwa kusakonzekera kwathu pasadakhale kutsimikizira kuti tikalandire phindu lalikulu m’nkhani zoperekedwa. Tifunikira kudzuka mofulumira patsikulo kuti tidye mfisulo wokwanira ndi kusamalira zinthu zina zofunikira kotero kuti tingakakhale pamalo pathu maprogramu asanayambe. Kupeza tulo tabwino usiku kulinso kofunika kotero kuti tidzakhale ogalamuka ndi okhoza kumvetsera mosamalitsa programu yonse ya tsikulo.
8 Njira yotsimikiziridwa yopezera phindu lalikulu m’programu ndiyo ya kulemba manotsi oyenera. Nkofunika kwambiri kwa achichepere ndi achikulire omwe kulemba manotsi. Wofalitsa wina wa zaka zakubadwa 16 akunena kuti: “Ndimalemba malemba otchulidwa m’nkhani. Ndiyeno ndimakapenda nkhaniyo kunyumba.” Wachichepere wina wa zakanso zakubadwa 16 akuwonjezera kuti: “Ndimalemba mfundo zazikulu. Zimandichititsa kutsatira bwino nkhaniyo.” Kaŵirikaŵiri zinthu zokha zimene mumafunikira pa programuyo ndizo Baibulo lanu, buku la nyimbo, notibuku yaikulu bwino, ndi cholembera. Zoonadi, makolo okhala ndi ana aang’ono ayenera kusamalira zosoŵa zawo, koma kuli bwino koposa kusadzisokoneza ife eni ndi ena ndi zoziziritsa zakumwa zazikulu ndi zinthu zathu zambirimbiri.
9 Abale ena amajambula programu, akumagwiritsira ntchito tepirikoda kapena kamera ya vidiyo, kuti akamvetserenso ndi kukaonereranso kwawo. Imeneyi ndi nkhani ya munthu mwini ngati iye achita zimenezi, koma kwa ena zimachitika kuti atangoyambiranso moyo wawo wamasiku onse, samakhala ndi nthaŵi yomvetsera kapena kuonerera zimene anajambula. Ndiponso, mfundo zina zazikulu mu nkhani zingaphonyedwe pokonza chipangizo chojambuliracho.
10 Tiyenera kuyesayesa mwamphamvu kuti tikhale pamalo athu programuyo isanayambe. Ngakhale kuti mwina tingakhale tili mkati mwa kukambitsirana zokumana nazo zokondweretsa ndi mabwenzi athu akale pamene tcheyamani akulengeza kuti programuyo ili pafupi kuyamba, timasonyeza ulemu kwa awo amene ali paprogramuyo, ndi abale athu onse, ngati ife nthaŵi yomweyo tileka kukambitsirana kwathu ndi kukakhala pamalo athu.
11 Misonkhano yachigawo nthaŵi zonse imakhala zochitika zokondweretsa chifukwa cha dalitso lalikulu la Yehova. Timalandira mapindu auzimu ndi akuthupi omwe. Tiyenera kukumbukira kuti ndalama zambiri zaloŵetsedwa m’kulipirira malo a msonkhanowo. Kodi ndimotani mmene zimenezi ndi zowonongedwa zina zimalipiriridwira? Kupyolera m’zopereka zathu zodzifunira, kaya zandalama kapena macheke olipiridwa ku “Watch Tower Society.” Zimenezi nzogwirizana ndi mzimu wa pa Salmo 96:8, limene limatilimbikitsa ‘kupatsa Yehova ulemerero ndi kufika ndi chopereka ku mabwalo ake.’
12 Kodi Khalidwe Lanu Lidzadzetsa Chitamando? Chaka chilichonse kope la Utumiki Wathu Waufumu la July limatikumbutsa mokoma mtima za kufunika kwa khalidwe labwino pamene tili pamsonkhano wachigawo. Zoonadi, khalidwe lathu nthaŵi zonse liyenera kupereka chitsanzo chabwino, koma pamene tisonkhana m’ziŵerengero zazikulu, kaŵirikaŵiri timapenyedwa kwambiri ndi awo amene sali m’choonadi. Khalidwe lathu, labwino kapena loipa, linganene zambiri koposa kulalikira kwathu. Tikufuna kuti Yehova atamandidwe ndi zimene timanena ndi kuchita.—Miy. 27:2; 1 Pet. 2:12.
13 Pambuyo pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” wa chaka chatha, mlonda wa pa motelo ina anati: “Awa ali ana abwino koposa amene ndinafunikira kulonda kwanthaŵi yaitali.” Ndiyeno, atanena za makhalidwe oipa ndi kuwononga zinthu kwa timagulu tina ta achichepere, iye anawonjezeranso ponena za ana a Mboni kuti: “Ali ndi khalidwe labwino ndipo amasangalatsa kukhala nawo. Bwenzi misonkhano ina yochitidwa muno ikanakhala yonga uwu.”
14 Mkonzi wina wa nkhani za m’nyuzipepala ya kumadzulo koma chapakati pa United States ananena motere ponena za msonkhano: “Akazi ndi atsikana anavala madiresi abwino kwambiri, ndipo amuna ndi anyamata anavala masuti ndi mataye. Anali kulemba manotsi pamene anali kumvetsera kwa okamba nkhani kwa masiku anayi. Ndipo ngati amati udongo uli wachiŵiri kwa umulungu, ayi, Mboni za Yehova zimasonyeza lingaliro limeneli bwino koposa.” Komabe, si malipoti onse amene akhala abwino motere.
15 Pamsonkhano wina panasimbidwa kuti panali anthu ambiri oyendayenda mkati mwa magawo. Oposa 1,000 (ambiri a iwo anali ana) anaŵerengedwa akumayendayenda mkati mwa programu ya pa Loŵeruka masana, zimene zikusonyeza kuti makolo afunikira kuwaphunzitsa ndi kuwayang’anira mokulira kwambiri. Kuyendayenda kosalekeza kumachititsa phokoso limene limacheukitsa awo amene akuyesa kumvetsera. Anthu oŵerengeka angakhale ndi zinthu zofunikira kusamaliridwa mkati mwa programu, koma kodi ena tonsefe sitiyenera kukhala tili m’malo mwathu, tikumamvetsera mosamalitsa?
16 Makolo ambiri amalamulira mwamphamvu ana awo ponena za kufika pamisonkhano ya mpingo mlungu uliwonse. Kodi sayenera kuchita mwamphamvu mofananamo pankhani ya kutsimikizira kuti ana awo akhala nawo pamodzi ndipo sakuyendayenda mkati mwa maprogramu? Malo a msonkhano amakhala Nyumba Yaufumu yaikulu, koma linolo ndi dongosolo la Satana, ndipo kungakhale kosavuta kwa anthu opanda khalidwe kuloŵa m’malowo ndi zolinga zosayenera. MUFUNIKIRA KUDZIŴA KUMENE ANA ANU ALI NDI ZIMENE AKUCHITA NTHAŴI ZONSE.
17 Kavalidwe ndi Kapesedwe: Tikukhala m’nyengo imene kaonekedwe ka wamba, ngakhale kosasamala, kamaonedwa kukhala kovomerezeka. Anthu ambiri amapita kutchalitchi ndi kumakonsati kapena kukadya ku malesitilanti atavala mosasamala kotheratu. Mawu ogwidwa m’ndime 14 akusonyeza kuti pali awo amene amayamikirabe kavalidwe kolemekezeka, makamaka mogwirizana ndi kulambira kolinganizidwa. Kavalidwe kosasamala, ka wamba ndi kupesa kosayenera kamasonyeza zambiri ponena za ife. Osaiŵala konse kuti malo amsonkhano ali ngati Nyumba Yaufumu yofutukulidwa. Ena amavala molemekezeka kaamba ka msonkhano koma pambuyo pa maprogramuwo amamka ku malesitilanti ndi kwina atavala mosayenera.
18 Oyembekezera ubatizo afunikira kukumbutsidwa kuti zovala zakutizakuti zomizidwira sizoyenera pachochitikacho. Chovala chake chiyenera kukhala choyenera ndiponso chabwino. Kodi ndani ayenera kutsimikizira zimenezi? Akulu ali ndi thayo la kuona kuti aliyense amene akubatizidwa kuchokera mumpingo mwawo sakupereka chifukwa chilichonse chokhumudwitsa. (2 Akor. 6:3, 4) Zimenezi zikuletsa kuvala zovala zoonekera mkati ndi masikipa okhala ndi mawu osonkhezera audziko kapena osatsa malonda. Kungakhale koyenera kwa akulu kukambitsirana nkhaniyi ndi woyembekezera ubatizo pamene akufunsa mafunso openda a m’buku la Uminisitala Wathu.
19 Ziŵiya Zojambulira: Monga momwe kwanenedwera poyambapo, kugwiritsira ntchito ziŵiya zojambulira, ndipo makamaka zojambulira makaseti a vidiyo, kuli chosankha cha munthu mwini. Ngati mukufuna kujambula, chonde lingalirani ena amene akhala mokuzingani. Kungakhale kocheukitsa ngakhale pamene kujambulako kukuchitidwa pamalo amene munthuyo wakhalapo. Palibe aliyense amene ayenera kuphimbira kutsogolo a pamsonkhano anzake pojambula. Ndiponso, palibe chiŵiya chojambulira cha mtundu uliwonse chimene chiyenera kulumikizidwa kumagetsi kapena ku ziŵiya zokuzira mawu, kapenanso kutseka njira kapena moyenda anthu.
20 Malo Okhala: Zothetsa nzeru zokhudza kusunga malo okhala zifunikirabe chisamaliro. Tifunanso kukumbutsa aliyense kuti: MIPANDO INGASUNGIDWIRE ZIŴALO ZA BANJA LANU ZOKHA NDI ALIYENSE AMENE MUNGANYAMULE M’GALIMOTO YANU. Pamalo ena a msonkhano abale ndi alongo anachita mothamanga poloŵa. Kunanenedwa kuti “mabwenzi athu amene anayenda mwanjira ya masiku onse kumka kumalo awo okhala anangopeza pokhala kumbuyo kwenikweni kwa bwalolo. Ambiri anali kusunga pafupifupi zigawo zonse, ndiyeno ambiri a malo okhala amene iwo anasunga sanakhalidwe ndi anthu.” Zizoloŵezi zosalingalira ena zimenezi zikuonekera kukhala zikupitiriza mosasamala kanthu za zikumbutso zanthaŵi zonse. Kodi sitiyenera kupenda mtima wathu ponena za nkhani imeneyi ndi kusinkhasinkha pa malamulo a mkhalidwe a pa Afilipi 2:3, 4?
21 Pa msonkhano uliwonse pamapangidwa makonzedwe a malo a awo amene amafuna chisamaliro chapadera, monga okalamba ndi opunduka. Chonde tsimikizirani kusakhala pa chimodzi cha zigawo zimenezi ngati muli wosayenerera. Ndiponso, yang’anitsitsani kuti muthandize awo amene amafuna chisamaliro chapadera kupeza pokhala ngati alibe munthu wowasamalira.
22 Utumiki Wachakudya: Pamisonkhano ina paonedwa kuti abale amadziloŵetsa m’kugulitsa ndiwo ndi zinthu zina kwa abale awo. Sipayenera kukhala msika uliwonse pamalo a msonkhano. Dipatimenti ya Utumiki Wachakudya iyenera kutsimikizira kuti ndiwo ndi zakudya zina zikugulidwa kusitolo lalikulu. Ngati abale abweretsa ndiwo kumsonkhano zodzagulitsa ayenera kuzigulitsa kusitolo yamsonkhano pamtengo wabwino kotero kuti zingagulitsidwe kwa abale kumeneko. Chifukwa chathu chofikira pamisonkhano chiyenera kukhala cha kupindula mwauzimu ndipo osati kuchita malonda. Misika sidzaloledwa kulikonse pamalo a msonkhano wachaka chino.
23 Pa August 12, 1994, Msonkhano Wachigawo woyamba wakuti “Mantha Aumulungu” udzayamba. Kodi mwatsiriza makonzedwe anu, ndipo kodi muli wokonzekera kukasangalala pamasiku atatu a kuyanjana kwachimwemwe ndi zinthu zabwino zauzimu? Pemphero lathu loona nlakuti Yehova adalitse zoyesayesa zanu za kusonkhana m’chilimwe chikudzachi ndi kudyetsedwa pagome la Yehova la zinthu zabwino pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Mantha Aumulungu.”
Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo
Ubatizo: Oyembekezera ubatizo ayenera kukhala ali m’malo mwawo pachigawo cholinganizidwa programu isanayambe pa tsiku lachiŵiri mmaŵa. Kwaonedwa kuti ena amavala mtundu wa zovala umene uli wosalemekezeka ndi wocheukitsa pachochitikacho. Chovala chomizidwira choyenerera ndi thawulo ziyenera kunyamulidwa ndi aliyense amene akufuna kubatizidwa. Pambuyo pa nkhani yaubatizo ndi pemphero loperekedwa ndi wokamba nkhani, tcheyamani wa gawolo adzapereka malangizo achidule kwa oyembekezera ubatizowo ndiyeno adzapempha nyimbo kuimbidwa. Pambuyo pa vesi lotsiriza, akalinde adzatsogolera oyembekezera ubatizowo kumalo omizira. Popeza kuti ubatizo wochitira chizindikiro cha kudzipatulira kwa munthu uli nkhani yaikulu ya munthu mwini ndi Yehova, palibe makonzedwe otchedwa maubatizo a paubwenzi amene oyembekezera ubatizo aŵiri kapena owonjezereka amakumbatirana kapena kugwirana manja pobatizidwa.
Mabaji: Chonde valani mabaji a 1994 pamsonkhano ndi popita kumalo amsonkhano ndi pobwerako. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimatikhozetsa kupereka umboni wabwino kwambiri poyenda ulendo. Zimenezi zinali chonchodi chaka chatha ponena za misonkhano imene inachitika ku Moscow ndi ku Kiev. Makadi ndi zoikamo zake ziyenera kupezedwa kupyolera mu mpingo wanu, popeza kuti sizidzapezeka pamsonkhano. Kumbukirani kunyamula khadi lanu latsopano la Medical Directive. Ziŵalo za banja la Beteli ndi apainiya ayeneranso kunyamula makadi awo owadziŵikitsa.
Utumiki Wodzifunira: Kodi mungapatule nthaŵi pamsonkhano ya kuthandiza mu imodzi ya madipatimenti? Kutumikira abale athu, ngati kungakhale kwa maola oŵerengeka okha, kungakhale kothandiza kwambiri ndi kodzetsa chikhutiro chokulira kwambiri. Ngati mukhoza kuthandiza, chonde fikani ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira pamsonkhanopo. Ana osafika pausinkhu wa zaka 16 nawonso akhoza kuthandiza mwa kugwira ntchito moyang’aniridwa ndi kholo kapena wachikulire wina wathayo.
Mawu a Chenjezo: Mwa kukhala maso pamavuto othekera kubuka, ife enife tikhoza kupeŵa zovuta zosafunikira. Kaŵirikaŵiri mbala ndi anthu ena opanda khalidwe amayendayenda pakati pa anthu achilendo. Tsimikizirani kuti galimoto yanu ili yokhomedwa nthaŵi zonse, ndipo musasiye kanthu kalikonse koonekera kamene kangayese munthu wina kuba. Mbala ndi opisa m’matumba amapeza bwino kwambiri pa namtindi wa anthu. Sikungakhale kwanzeru kusiya zinthu zamtengo wapatali pamalo anu okhala. Simungatsimikize kuti aliyense amene wakuzingani ndi Mkristu. Nkuperekeranji chiyeso? Malipoti osimba za kuyesayesa kuba ana kochitidwa ndi akunja alandiridwa. YANG’ANIRANI ANA ANU NTHAŴI ZONSE.
Malo a 1994
Aug. 12-14 Chililabombwe (CB-11b); Kitwe Kamitondo (CB-6, CB-13); Kitwe Chamboli (CB-7, CB-8); Luanshya (CB-2); Lusaka Eng. (EC-1); Mufulira (CB-10); Mufulira Eng. (EC-2); Mumbwa (C-1); Nsama (N-6, N-8a); Senga Hill (N-4, N-5); Luwingu (N-7, N-8b)
Aug. 16-18 Malambanyama (C-2a, b; C-3); Luswishi (CB-9); Manyinga (NW-1); Kabula (L-4, CB-12b); Kalungu (N-2a, N-3); Mununga (L-1)
Aug. 19-21 Mansa (L-5); Lundazi (E-8a); Chipata (E-6, E-7, E-8b); Ndola Chifubu (CB-4); Ndola Mushili (CB-5); Chingola (CB-11a, c; NW-4a)
Aug. 22-24 Kasempa (NW-2); Muyombe (N-2c); Kawambwa (L-2, L-3); Lualaba (C-5); Senanga (W-4); Mwandi (W-5); Mpongwe (CB-1)
Aug. 23-25 Katete (E-4, E-5); Samfya (L-6, L-7, L-8); Ukwimi (E-10)
Aug. 26-28 Solwezi (NW-3, NW-4b, NW-5); Chinsali (N-2b); Kabwe (C-4); Mongu (W-2a, W-3); Kalomo (S-1, S-2); Lusaka Matero (LK-1, LK-3); Lusaka Woodlands (LK-5); Kashitu (C-6, CB-3); Lusaka Chelston (LK-2, LK-4)
Aug. 29-31 Nyanje (E-2, E-3, E-9); Nyimba (E-1); Kawa (Turn-Off); (C-9, C-10, C-11)
Aug. 30-Sept. 1 Kaoma (W-1, W-2b)
Sept. 2-4 Mkushi (C-7, C-8); Mpika (N-1); Kafue (S-3, S-4)