Chochitika Chofunika Koposa m’Mbiri ya Anthu
1 Yesu anadza pa dziko lapansi atatumidwa ndi Atate wake kudzachitira umboni choonadi chimene chikatsogolera ku moyo wosatha. (Yoh. 18:37) Kukhulupirika kwake mpaka imfa kunalemekeza Yehova, kunayeretsa dzina la Mulungu, ndipo kunapereka dipo. (Yoh. 17:4, 6) Izi ndi zimene zinachititsa imfa ya Yesu kukhala chochitika chofunika koposa m’mbiri yonse ya anthu.
2 Kuyambira pa kulengedwa kwa Adamu, pa dziko lapansi pakhala anthu angwiro aŵiri okha. Adamu anali mumkhalidwe wokhoza kudzetsa madalitso abwino koposa kwa mbadwa zake zosabadwa panthaŵiyo. M’malo mwake, iye mwadyera anapanduka, akumawatayira m’mavuto amene akathera mu imfa. Pamene Yesu anadza, anasonyeza kukhulupirika ndi kumvera kwangwiro, akumatsegula mwaŵi wa moyo wosatha kwa onse okhulupirira.—Yoh. 3:16; Aroma 5:12.
3 Palibe chochitika china chilichonse chimene chingalingane ndi imfa ya nsembe ya Yesu. Inasintha mbiri ya anthu. Inapereka maziko oukitsira anthu miyandamiyanda kwa akufa. Inayala maziko a Ufumu wosatha umene udzathetsa kuipa ndi kusandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso. Potsirizira pake idzamasula mtundu wonse wa anthu pa kupondereza ndi ukapolo zamtundu uliwonse.—Sal. 37:11; Mac. 24:15; Aroma 8:21, 22.
4 Zonsezi zikutithandiza kuzindikira chifukwa chake Yesu analangiza ophunzira ake kukumbukira imfa yake mwa kuchita Chikumbutso chaka ndi chaka. (Luka 22:19) Pozindikira tanthauzo lake, tikuyang’ana kutsogolo kudzasonkhana ndi mipingo ya Mboni za Yehova pa dziko lonse pa Lachisanu, April 14, dzuŵa litaloŵa. Nthaŵiyo isanafike, ndi bwino kuŵerengera pamodzi monga banja nkhani za Yesu za m’Baibulo zonena za masiku ake otsiriza pa dziko lapansi ndi kuchirikiza kwake choonadi molimba mtima. (Ndime zosankhidwa zasonyezedwa pa Kalenda ya 1995, April 9-14.) Anatiikira chitsanzo cha kudzipereka kwa Mlengi wathu. (1 Pet. 2:21) Tiyeni tichite zomwe tingathe kuitanira mabwenzi athu ndi banja, limodzi ndi ophunzira Baibulo ndi anthu ena okondwerera, ku msonkhano wofunika umenewu. Fotokozani pasadakhale zimene zidzachitika ndi tanthauzo la zizindikiro.—1 Akor. 11:23-26.
5 Akulu ayenera kulinganiza zinthu pasadakhale ndithu kutsimikizira kuti Nyumba Yaufumu ili yaudongo ndi yoyera. Ayenera kupanga makonzedwe akuti wina akagule zizindikirozo. Ayeneranso kulinganiza bwino kaperekedwe ka zizindikiro. Malingaliro othandiza a mmene tingasonyezere ulemu pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye anaperekedwa mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, tsamba 17. Kuli koyenera kwambiri kwa mipingo kulinganiza ntchito ya utumiki wakumunda yowonjezereka kutatsala masiku angapo phwandolo lisanachitike ndi masiku angapo pambuyo pake.
6 Chaka chatha, anthu 12,288,917 pa dziko lonse anapezekapo pa kukumbukira chochitika chofunika chimenechi. Popeza kuti limenelo ndi tsiku lofunika koposa pa kalenda yathu, ife tonse tiyenera kupezekapo.