Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/07 tsamba 1
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • “Muzichita Zimenezi” Chikumbutso Chidzachitika pa April 5
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Chifukwa Chake Timapezeka pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 3/07 tsamba 1

“Muzichita Zimenezi Pondikumbukira Ine”

Tidzakumbukira Imfa ya Yesu pa April 2

1. N’chifukwa chiyani deti la April 2, 2007 n’lofunika kwambiri?

1 Pa April 2, 2007, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse adzasonkhana kuti akumbukire imfa yansembe ya Yesu. Iye anafa chifukwa choikira kumbuyo ulamuliro wa Atate wake wakumwamba. Zimenezi zinapereka umboni wakuti Satana Mdyerekezi ananama ponena kuti anthu amatumikira Mulungu ndi zolinga zadyera basi. (Yobu 2:1-5) Komanso Mgonero wa Ambuye umatikumbutsa kuti kudzera mu imfa yake monga munthu wangwiro, wopanda uchimo, Yesu ‘anapereka moyo wake dipo lowombola anthu ambiri.’ (Mat. 20:28) Motero, Yesu analamula ophunzira ake kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.” (Luka 22:19) Kodi kuyamikira mphatso yamtengo wapatali ya Mulungu imeneyi kwakulimbikitsani kuyamba kukonzekera kuti mudzakumbukire nawo chikondi chachikulu kwambiri chimene Mulungu anasonyezachi?—Yoh. 3:16.

2. Kodi tingakonzekeretse bwanji mitima yathu kaamba ka Chikumbutso?

2 Konzekeretsani Mitima: Tingathe kukonzekeretsa mitima yathu kaamba ka mwambo wa Chikumbutsowu mwa kuganizira zimene zinachitika m’masiku omalizira a moyo wa Yesu padziko lapansi. Ndandanda ya kuwerenga Baibulo mwapadera imene mungaipeze m’kabuku ka Kusanthula Malemba—2007 ndiponso mu Kalendala ya 2007, ingakuthandizeni kukonzekeretsa mitima yanu. Ndandanda imeneyi yakonzedwa motsatira zimene zinachitika masiku angapo imfa ya Yesu itayandikira, ndipo masikuwo afananitsidwa ndi masiku a pakalendala imene timagwiritsa ntchito lerolino. Baibulo limatchula masiku mogwirizana ndi kalendala ya Ayuda, ndipo pakalendala imeneyo tsiku limayamba pamene dzuwa likulowa ndi kutha pamene dzuwa likulowanso. Pokonza ndandanda ya kuwerenga Baibulo kwa panthawi ya Chikumbutsoyi tinaganizira kusiyana kumeneku. Tidzapindula kwambiri ndi mwambo wa Chikumbutsowu ngati tiganizira mfundo zimene tingazipeze pa kuwerenga Baibulo kumeneku. Tingapindulenso mwa kupemphera ndi kusinkhasinkha za kukula kwa chikondi cha Mulungu.

3. Kodi anthu achidwi ndiponso osalalikira tingawathandize motani kuti adzapindule ndi Chikumbutso?

3 Itanirani Ena ku Mwambowu: Mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa February inalengeza za ntchito yapadera yoitanira anthu kumwambo wofunikawu. Kodi mwakonzekera kuti mudzagwire nawo ntchitoyi mokwanira? Kodi mwalemba mayina a anthu omwe mukuwadziwa oti muwaitanire ku mwambowu? Kodi mwayamba kale kuwaitana? Konzani zoti mudzafike mwamsanga tsiku la Chikumbutsolo kuti mudzalandire anthu omwe munawaitana komanso anthu ena achidwi. Mungathe kukonza zoti mudzakhale nawo, ndi kuonetsetsa kuti ali ndi Baibulo ndiponso buku la nyimbo. Asonyezeni kwa anthu ena a mumpingo mwanu. Mwambo wa Chikumbutso ukadzangotha dzapezeni nthawi yoyankha mafunso awo. Dzawapempheni kuti adzamvere nawo nkhani ya onse yapadera yomwe idzakambidwe pa April 15. Akulu makamaka afunika kuonetsetsa kuti Akhristu amene ankasonkhana ndi mpingo ndipo anasiya kulalikira aitanidwa kuti adzakhale nawo pa Chikumbutso ndiponso kuti adzamvere nawo nkhani yapaderayi.

4. Kodi tingawathandize bwanji anthu amene achita nawo Chikumbutso kuti apitirize kupita patsogolo mwauzimu?

4 Thandizani Achidwi Ndiponso Osalalikira Kuti Apite Patsogolo: Wokamba nkhani ya Chikumbutso adzafotokoza mwachidule kuti timakhala ndi maphunziro a Baibulo apanyumba aulere ndipo adzalimbikitsa anthu achidwi kuti apitirize kuphunzira za Yehova. Mungathe kudzagwiritsa ntchito ndemanga zake polimbikitsa anthu amene mudzawaitane kuti mupitirize kuwathandiza mwauzimu. Ngati sakuphunzira Baibulo, dzaonetsetseni kuti pambuyo pa Chikumbutso mudzakawachezere ndi kuwasonyeza mmene timachitira phunziro la Baibulo laulere. Kuti apite patsogolo mwauzimu, afunikanso azifika pa misonkhano ya mpingo. (Aheb. 10:24, 25) Ndipo kuti izi zitheke, alimbikitseni kufika pa misonkhanoyo kawirikawiri. Akulu akonze zodzachezera Akhristu osalalikira omwe adzafike pa Chikumbutso ndi kuwathandiza kuganizira mofatsa mfundo za m’nkhani ya Chikumbutso. Kuchita zimenezi kungawathandize kuyambiranso kutumikira ndi mpingo.

5. Kodi mwambo wa Chikumbutso umatipindulitsa motani?

5 Mwambo wa Chikumbutso umatipatsa mwayi woganizira mofatsa zimene Yehova ndi Yesu anatichitira. Kuchita zimenezi kumazamitsa chikondi chathu pa Yehova ndi Yesu ndiponso kumakhudza khalidwe lathu. (2 Akor. 5:14, 15; 1 Yoh. 4:11) Ino ndiyo nthawi yofunika kuti ifeyo tiyambe kukonzekera ndiponso kukonzekeretsa anthu achidwi kudzachita nawo mwambo wofunika kwambiriwu, umene umatipatsa mpata ‘wolengeza imfa ya Ambuye.’—1 Akor. 11:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena