Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/06 tsamba 1
  • Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Makhalidwe Amene Amatichititsa Kupezeka Pamisonkhano
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • “Muzichita Zimenezi” Chikumbutso Chidzachitika pa April 5
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Tiyeni Tisonyeze Kuyamikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 3/06 tsamba 1

Thandizani Ena Kupindula ndi Dipo

Chikumbutso cha Imfa ya Kristu Chidzachitika pa April 12

1. Kodi ndi njira imodzi iti imene anthu a Mulungu amasonyezera kuti amayamikira dipo?

1 “Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.” (2 Akor. 9:15) Mawu amenewa amafotokoza bwino kwambiri mmene timamvera poona ubwino ndi kukoma mtima zimene Mulungu wasonyeza anthu ake kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu. Kuyamikira kumeneku kudzaonekera makamaka tikadzasonkhana pa April 12 kuchita Chikumbutso cha imfa ya Kristu.

2. Kuwonjezera pa atumiki a Yehova, kodi ndaninso amapezeka pa mwambo wa Chikumbutso, ndipo ayenera kuchita chiyani kuti apindule ndi dipo?

2 Chaka chilichonse, kuphatikiza pa atumiki a Yehova, anthu enanso okwanira pafupifupi teni miliyoni amapezeka pa Chikumbutso. Potero, amasonyeza kuti akuyamikira nsembe ya Kristu. Koma kuti apindule ndi dipo afunika kulikhulupirira. (Yohane 3:16, 36) Kodi tingawathandize bwanji kukhala ndi chikhulupiriro chimenecho? Pa nyengo ino ya Chikumbutso, tiwalimbikitse kukhala ndi phunziro lawolawo la Baibulo ndiponso kupezeka pamisonkhano ya mpingo ya mlungu ndi mlungu. Taonani malingaliro otsatirawa.

3. Kodi tingayambe bwanji kuchita phunziro la Baibulo ndi anthu amene tawaitanira ku Chikumbutso?

3 Maphunziro a Baibulo: Mukaitanira anthu achidwi ku Chikumbutso, bwanji osayesa kuyamba nawo phunziro la Baibulo m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? M’pempheni munthuyo kuti mum’fotokozere za mwambo wa Chikumbutso. Tsegulani pa masamba 206 mpaka 209 ndipo phunzirani mutu wakuti “Mgonero wa Ambuye Ndi Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu.” Mungaphunzire mutu umenewu pa ulendo umodzi kapena maulendo awiri, mwina monga phunziro la Baibulo lachidule. Mukamaliza mutu umenewu, munthu amene mukukambirana naye angafune kuphunzira mutu 5, wakuti, “Dipo la Yesu Ndilo Mphatso ya Mulungu ya Mtengo Wapatali Koposa Zonse.” Mukangoyamba kuchita phunziro la Baibulo lokhazikika, bwererani ku mitu inayi yoyambirira ya bukuli ndipo iphunzireni.

4. Kodi ndani amene tingayambe nawo phunziro la Baibulo panyengo ino ya Chikumbutso?

4 Kodi ndani amene tingayambe nawo phunziro la Baibulo mwa njira imeneyi? Mwinamwake anthu ena amene mumagwira nawo ntchito, anzanu a kusukulu, kapena omwe mukukhala nawo pafupi angafune kuti muphunzire nawo. Abale angafikire amuna osakhulupirira a alongo a mumpingo. Ndipo musanyalanyaze achibale anu omwe si Mboni. Komanso, tidzafunika kuyesetsa kwambiri kuitanira ku Chikumbutso anthu amene panthawi ina anali kugwirizana mwachangu ndi mpingo. (Luka 15:3-7) Tiyeni tiyesetse kuthandiza anthu onse otero kupindula ndi dipo.

5. Kodi tingalimbikitse bwanji ophunzira Baibulo ndiponso anthu ena achidwi kupezeka pamisonkhano ya mpingo ya mlungu ndi mlungu?

5 Misonkhano ya Mpingo: Chikumbutso ndi msonkhano woyamba umene ophunzira Baibulo ambiri ndiponso anthu ena achidwi amapezekapo. Koma kodi tingawalimbikitse bwanji kupezeka pa misonkhano ina ya mpingo ndiponso kupindula nayo? Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2005, patsamba 8, unali ndi malingaliro otsatirawa: “Tchulani mutu wa nkhani ya onse ya mlungu umenewo. Aonetseni zimene mukaphunzire pa Msonkhano wa Nsanja ya Olonda ndiponso pa Phunziro la Buku la Mpingo. Afotokozereni za Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi Msonkhano wa Utumiki. Mukakhala ndi nkhani mu sukulu, mwina mukhoza kuyesezera nawo limodzi. Auzeni mfundo zabwinozabwino zimene zinakambidwapo pa misonkhano. Aonetseni zithunzi za m’mabuku athu kuti muwathandize kukhala ndi chithunzi cha zimene zimachitika pa misonkhano. Paphunziro loyambirira lenileni, apempheni kuti abwere ku misonkhano.”

6. Kodi ndi njira ziwiri ziti zimene tingathandizire anthu oona mtima kupindula ndi dipo?

6 Ngati anthu oona mtima aphunzira Baibulo ndi kupezeka pamisonkhano nthawi zonse, amapita patsogolo mwamsanga mwauzimu. Chotero, tiyeni tilimbikitse ena kupindula ndi zinthu zauzimu zimenezi. Alimbikitseninso kupindula ndi dipo, limene lili mphatso yaikulu koposa yomwe Mulungu watipatsa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena