Tiyeni Tisonyeze Kuyamikira
Chikumbutso Chidzachitika pa April 17
1. Pa nyengo ya Chikumbutso, kodi tiyenera kuganizira mawu ati amene wamasalimo ananena?
1 Atasonyezedwa chifundo ndiponso kupulumutsidwa m’njira zambiri, wamasalimo anafunsa kuti: “Yehova ndidzamubwezera chiyani pa zabwino zonse zimene wandichitira?” (Sal. 116:12) Masiku anonso, atumiki a Mulungu ali ndi zifukwa zambiri zokhalira oyamikira. Patapita zaka zambiri kuchokera pamene mawu ouziridwa amenewa analembedwa, Yehova anapatsa mtundu wa anthu mphatso yapadera kwambiri imene ndi dipo. Pamene tikukonzekera kukumbukira imfa ya Khristu pa April 17, tili ndi zifukwa zambiri zokhalira oyamikira.—Akol. 3:15.
2. Tchulani zifukwa zimene zimatichititsa kuyamikira dipo.
2 Madalitso Amene Timapeza Chifukwa cha Dipo: Chifukwa cha dipo, ‘machimo athu amakhululukidwa.’ (Akol. 1:13, 14) Zimenezi zimatipatsa mwayi wolambira Yehova ndi chikumbumtima choyera. (Aheb. 9:13, 14) Timatha kulankhula momasuka ndi Yehova m’pemphero. (Aheb. 4:14-16) Amene amakhulupirira dipo ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.—Yoh. 3:16.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira Yehova chifukwa cha dipo limene anapereka?
3 Sonyezani Kuyamikira: Njira imodzi imene tingasonyezere kuyamikira dipo ndi kuwerenga ndiponso kusinkhasinkha ndime za m’Baibulo zimene zasankhidwa kuti tiziwerenge pa nyengo ya Chikumbutso tsiku ndi tsiku. Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2011, ya mutu wakuti, “Kodi Mukukonzekera Tsiku Lofunika Kwambiri Chaka Chino?” inakonzedwa kuti itithandize kukwaniritsa cholinga chimenechi. Tingamuuzenso Yehova kudzera m’pemphero lochokera pansi pa mtima kuti timayamikira kwambiri dipo. (1 Ates. 5:17, 18) Timasonyezanso kuyamikira mwa kupezeka pa mwambo wa Chikumbutso pomvera lamulo la Yesu. (1 Akor. 11:24, 25) Kuwonjezera pamenepo, tingatsanzire chikondi cha Yehova chopanda malire mwa kuitanira anthu ambiri kuti adzasonkhane nafe.—Yes. 55:1-3.
4. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?
4 Atumiki a Yehova oyamikira saona tsiku la Chikumbutso ngati tsiku lina lililonse la msonkhano. Tsiku limeneli ndi tsiku la msonkhano wapadera kwambiri pa chaka. Pamene tsiku la Chikumbutso likuyandikira, tiyeni tikhale otsimikiza mtima ngati wamasalimo amene analemba kuti: “Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usaiwale zochita zake zonse.”—Sal. 103:2.